Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zigoba za Nkhono Zam’madzi

Zigoba za Nkhono Zam’madzi

Panagona Luso!

Zigoba za Nkhono Zam’madzi

Zigoba za nkhono zam’madzi zimaoneka zosalimba, koma n’zolimba kwambiri moti simungathe kuziphwanya. Wasayansi wina dzina lake Kenneth Vecchio, pokumbukira zimene ankachita ali mwana, anati: “Ndikafuna kuphwanya zigoba zimenezi, ndinkagwiritsa ntchito hamala.”

Taganizirani izi: M’kati mwa zigoba zimenezi muli mamba ang’onoang’ono kwambiri omwe sitingawaone ndi maso athu. Pulofesa wina wa payunivesite ya ku Massachusetts, ku U.S.A., dzina lake Christine Ortiz, anati: “Titaunika m’kati mwa zigoba za nkhono, tinachita chidwi kwambiri kuona kuti muli mamba ang’onoang’ono kwambiri ndipo tikuganiza kuti mamba amenewa ndi amene amachititsa kuti zigobazi zizikhala zolimba kwambiri.”

Mkulu wina wolemba nkhani za sayansi, dzina lake Charles Petit, ananena kuti mamba a nkhono zam’madzi “anayalana mwadongosolo kwambiri.” Iye anatinso: “Mamba amenewa amaoneka ngati njerwa zamakonamakona zoyalidwa bwino. Mambawa amakhala ngati apakidwa laimu ndipo amalumikizidwa ndi mafuta a m’thupi mwa nkhonozo.”

Asayansi akuganiza kuti angaphunzire zambiri kuchokera ku zigobazi, zomwe zingawathandize popanga zovala zoteteza munthu kunkhondo, zitsulo za magalimoto, mapiko a ndege, komanso zinthu zina zambiri. Pulofesa Ortiz anati: “M’chilengedwe muli zinthu zambiri zochititsa chidwi zimene zinapangidwa ndi tinthu ting’onoting’ono kwambiri. Asayansi akuyesa kubera nzeru zimenezi popanga zinthu, koma sanakwanitsebe.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi chigoba cholimba kwambiri cha nkhono zam’madzi chinakhalako mwangozi? Kapena chinachita kupangidwa ndi Mlengi?

[Chithunzi patsamba 25]

M’kati mwa chigoba cha nkhono zam’madzi

[Mawu a Chithunzi]

Inset: © Eye of Science/Photo Researchers, Inc.