Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mankhwala Odzikongoletsera Ochokera ku Mitengo

Mankhwala Odzikongoletsera Ochokera ku Mitengo

Mankhwala Odzikongoletsera Ochokera ku Mitengo

▪ Dera la kum’mwera chakumadzulo kwa dziko la Madagascar ndi lotentha kwambiri, ndipo akazi kumeneku amakonda kuyenda mphepete mwa nyanja kufunafuna zigoba za nkhono za m’madzi zomwe amazigulitsa kwa alendo obwera m’dzikoli. Akaziwa amapakapaka nkhope zawo mankhwala ochokera ku mitengo. Amadzipaka mankhwala amenewa ndi cholinga choti khungu lawo lisapse ndi dzuwa komanso kuti azioneka bwino.

Mankhwalawa amapangidwa kuchokera ku mitengo inayake ya maluwa. (masonjoany ndi fihamy) Kupanga kwake n’kosavuta: Akaziwa amatenga makungwa a mitengo n’kuwanyenya pamwala wophwatalala, ndipo amathira madzi pang’onopang’ono mpaka makungwawa ataoneka ngati phala. Kenako amayamba kuzipaka mankhwalawa mwaluso pankhope pawo pogwiritsira ntchito kamtengo kosongoka bwino.

Akazi ena amapaka mankhwalawa nkhope yawo yonse kungosiyapo maso okha, pamene ena amangopaka pachipumi, m’masaya ndi kuchibwano. Mankhwalawa amawagwiritsa ntchito pofuna kubisa zipsera kunkhope, kuteteza khungu kapenanso pofuna kudzikongoletsa. Nthawi zina m’makungwawa amaphatikizamo zinthu zina kuti apange mitundu yosiyanasiyana ya mankhwalawa.

Anthu ambiri sangakhulupirire kuti mankhwala odzikongoletsera amenewa amapangidwa kuchokera ku mitengo. Mosiyana ndi anthu a mayiko ena amene amagwiritsa ntchito mankhwala opangidwa ku fakitale, anthu a m’dziko la Madagascar, amakonda kugwiritsa ntchito mankhwala ochokera ku mitengo.