Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungathetse Bwanji Matenda Ovutika Maganizo?

Kodi Mungathetse Bwanji Matenda Ovutika Maganizo?

 Kodi Mungathetse Bwanji Matenda Ovutika Maganizo?

RUTH, amene wakhala akudwala matenda ovutika maganizo kwa zaka zambiri, anati: “Ine ndi mwamuna wanga tinayesetsa kufufuza mankhwala a matendawa, tinasintha zinthu zina pamoyo wathu, komanso tinkayesetsa kuchita zinthu zothandiza kuti vutoli lichepe. Tikuona kuti tapeza mankhwala othandiza ndipo panopa ndikupezako bwino. Koma panthawi imene zinthu sizinkayenda bwino, chimene chinkandithandiza ndi chikondi chimene mwamuna wanga komanso mabwenzi anga ankandisonyeza.”

Monga mmene zinalili ndi Ruth, anthu amene akudwala matenda ovutika maganizo amafunika kulimbikitsidwa ndiponso kupatsidwa thandizo la mankhwala loyenera. Si bwino kunyalanyaza vutoli chifukwa nthawi zina ngati munthu salandira thandizo, moyo wake umakhala pangozi. Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, Yesu Khristu anasonyeza kuti anthu amene amadziwa mankhwala angathandize. Iye ananena kuti ‘odwala amafuna wochiritsa.’ (Maliko 2:17) Apa mfundo ndi yakuti madokotala angathandize kwambiri anthu amene ali ndi matenda ovutika maganizo. *

Njira Zina Zothetsera Matendawa

Pali njira zambiri zothandizira anthu amene akudwala matenda ovutika maganizo. Njira imene mungasankhe iyenera kugwirizana ndi mtundu wa matenda anu. (Onani bokosi lakuti,  “Zizindikiro za Matenda Ovutika Maganizo,” patsamba 5.) Anthu ambiri angathandizidwe  ndi dokotala wamba koma ena afunikira kuthandizidwa ndi dokotala amene amadziwa kwambiri za matenda amenewa. Dokotalayo angapereke mankhwala ochepetsa nkhawa kapena mitundu ina ya mankhwala. Ena amapeza bwino akamwa mankhwala azitsamba, akasintha chakudya, kapena akamachita masewera olimbitsa thupi.

Zimene Zimachitika Kawirikawiri

1. Anzanu amene sadziwa zachipatala angakuuzeni mtundu wa mankhwala amene muyenera kulandira ndi amene simuyenera kulandira. Nthawi zina angakulimbikitseni kuti muzimwa mankhwala azitsamba kapena akuchipatala, kapenanso kuti musamwe mankhwala alionse.

Ganizirani izi: Onetsetsani kuti malangizo amene mukutsatira akuchokera kwa anthu odalirika. Dziwani kuti inuyo ndi amene muli ndi udindo wosankha mankhwala oyenera.

2. Munthu wodwalayo angasiye kumwa mankhwala ngati sakuchira kapena ngati mankhwalawo akuyambitsa mavuto ena.

Ganizirani izi: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.” (Miyambo 15:22) Ngati wodwala afotokoza bwino vuto lake komanso ngati dokotala amvetsera, mankhwala amene angaperekedwe angakhale othandiza. Choncho, ndi bwino kufotokozera dokotala vuto lanu momasuka, ndipo mungamufunse ngati mufunika kusiya kumwa mankhwalawo mukaona kuti sizikusintha kapena ngati mungafunike kudikira kaye.

3. Kudziona kuti wachira kungachititse wodwalayo kusiya kumwa mankhwala. Iye  angaiwale ululu umene ankamva asanayambe kumwa mankhwala.

Ganizirani izi: Kusiya kumwa mankhwala popanda kuuzidwa ndi dokotala n’koopsa kwambiri ndipo kungaike moyo pangozi.

Ngakhale kuti Baibulo si buku la zachipatala, Mlembi wake ndi Yehova Mulungu, yemwenso ndi Mlengi wathu. Nkhani yotsatira ifotokoza za malangizo ndi chitonthozo chimene Mawu a Mulungu amapereka kwa odwala matenda a maganizo ndiponso kwa anthu amene akuwasamalira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Galamukani! sisankhira anthu thandizo la mankhwala. Munthu aliyense ayenera kusankha yekha mtundu wa mankhwala amene angalandire.

 [Bokosi patsamba 5]

ZIZINDIKIRO ZA MATENDA OVUTIKA MAGANIZO

Mankhwala amene munthu wodwala matenda a maganizo angasankhe, ayenera kugwirizana ndi zizindikiro za matenda ake. Pali mitundu ingapo ya matendawa ndipo ena ali ndi zizindikiro zotsatirazi.

Munthu amavutika maganizo kwambiri kwa miyezi 6 kapena kupitirira. Ndipo ngati sanapite kuchipatala msanga, matendawa amamulowerera kwambiri.

Munthu amasinthasintha, nthawi zina amatha kusangalala kwambiri ndipo nthawi zina amakhumudwa kwambiri. Onani nkhani yakuti “Kukhala ndi Matenda a Maganizo,” mu Galamukani! ya January 8, 2004.

Munthu amalephera kuchita bwino zinthu zina. Ndipo masiku ena amavutika kwambiri maganizo kuposa masiku ena.

Mayi amavutika maganizo akangobereka ndipo amakhala ndi nkhawa kwambiri. Onani Galamukani! yachingelezi ya June 8, 2003, tsamba 21 mpaka 23.

Munthu amavutika kwambiri m’nyengo yozizira pamene dzuwa siliwala kwambiri. Nyengo yotentha ikamayamba vutoli limachepa.