Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndimasowa Anthu Ocheza Nawo?

N’chifukwa Chiyani Ndimasowa Anthu Ocheza Nawo?

 Zimene Achinyamata Amadzifunsa

N’chifukwa Chiyani Ndimasowa Anthu Ocheza Nawo?

“Likafika Loweruka ndi Lamlungu, ndimangoona ngati anthu padziko lonse apita kokasangalala kundisiya ndekhandekha.”—Anatero Renee.

“Anzanga amatengana kukacheza kundisiya ndekha.”—Anatero Jeremy.

KUNJA kwacha bwinobwino, koma inu mukusowa chochita. Anzanu onse ali ndi zochita. Onse apita kokasangalala. Leronso mwatsala nokha!

Ndi zoona kuti zimapweteka anzanu akaitanizana kupita kokasangalala, inu kukusiyani nokha. Zimapwetekanso kwambiri mukaganizira chifukwa chimene akusiyirani. Mungaganize kuti: ‘Mwina ndili ndi vuto. Nanga bwanji anthu onse safuna kucheza nane?’

N’zopwetekadi

Ndi chibadwa kuti munthu akhale ndi mtima wofuna kucheza ndi anzake. Pajatu anthufe timasangalala kukhala ndi anzathu ocheza nawo. Asanalenge Hava, Yehova anaona kuti: “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha.” (Genesis 2:18) Zoonadi, munthu amafunika kukhala ndi mnzake; ndi mmene tinalengedwera. N’chifukwa chake zimapweteka kwambiri munthu ukamasowa wocheza naye.

Zimakhala zokhumudwitsa kwambiri ngati anthu nthawi zonse safuna kucheza nanu kapena ngati amasonyeza kuti inuyo si woyenerera kukhala bwenzi lawo. Mtsikana wina dzina lake Marie, ananena kuti: “Pali atsikana ena amene amachita zinthu zaphindu ndithu, koma umatha kuona wekha kuti iwo akuona kuti iweyo sukuyenerera kukhala m’gulu lawo.” Anthu akamakusankha chonchi, umasungulumwa.

Nthawi zina munthu umatha kusungulumwa ngakhale uli pakati pa anzako. Nicole anati: “Mwina simungamvetse, koma ndikukumbukira kuti tsiku lina ndinasungulumwa kwambiri ndili pa phwando. Ndikuganiza kuti zinali choncho chifukwa, ngakhale ndinali pagulu la anthu ambiri, panalibe aliyense amene ndikanati ndi  mnzanga.” Ena mpaka amasungulumwa ali pa misonkhano ikuluikulu yachikhristu. Meagan anati: “Zimaoneka ngati onse akudziwana kupatulapo ineyo.” Mtsikana winanso dzina lake Maria akugwirizana ndi zimenezi. Iye anati: “Zimakhala ngati kuti uli pakati pa anzako koma kwenikweni ulibe mnzako.”

Munthu aliyense, ngakhale amene amaoneka otchuka kapena osangalala, amasungulumwa. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Ngakhale m’kuseka mtima uwawa.” (Miyambo 14:13) Kusungulumwa kukakula ndipo ngati sikukutha, munthu umazunzika. Baibulo limati: “Moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima.” (Miyambo 15:13) Kodi mungatani ngati mtima wanu umawawa chifukwa chakuti anzanu sakucheza nanu?

Zimene Mungachite Mukasungulumwa

Mukasungulumwa, chitani zinthu zotsatirazi:

Muziganizira zimene mumachita bwino. (2 Akorinto 11:6) Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimachita bwino zinthu zotani?’ Ganizirani za luso kapena khalidwe labwino limene muli nalo, ndipo lembani zimenezi pansipa.

․․․․․

Mukasungulumwa chifukwa choti anzanu sakucheza nanu, ganizirani za zinthu zimene mumachita bwino, monga zimene mwazilemba pamwambapa. N’zoona kuti muli ndi zinthu zina zimene simuchita bwino, ndipo mungofunikira kuyesetsa. Koma musataye mtima ndi zolephera zanuzo. M’malo mwake, muziona kuti m’pofunika kuleza mtima. Sikuti mungachite zinthu zonse bwino, koma zilipo zimene mumachita bwino. Muziganizira zinthu zimene mumachita bwinozo.

Muzikhala omasuka. (2 Akorinto 6:11-13) Yambani inuyo kucheza ndi anthu. Kuchita zimenezi si kophweka. Mtsikana wina wa zaka 19, dzina lake Liz anati: “Anthu akakhala pa gulu amaopsa, koma mutangopita kwa munthu mmodzi ndi kum’patsa moni, basi ndiye kuti anthuwo akhala anzanu.” (Onani bokosi lakuti “Mfundo Zothandiza Kucheza ndi Anthu.”) Popeza aliyense amafuna kukhala ndi wocheza naye, onetsetsani kuti inuyo simukupatulapo aliyense, ngakhale achikulire. Mtsikana wina wa zaka 17, dzina lake Cori anati: “Pamene ndinali ndi zaka 10 kapena 11, ndikukumbukira kuti ndinali ndi mnzanga wamkulu kwambiri kwa ineyo. Anali mnzanga kwambiri ngakhale kuti tinali ndi zaka zosiyana.”

Ganizirani anthu awiri achikulire mumpingo mwanu amene mukufuna kuti mudziwane nawo bwino. Lembani mayina awo pansipa.

․․․․․

Tsiku limene mupite ku misonkhano, yesani kukumana ndi mmodzi wa iwo ndi kuyamba kucheza naye. Funsani munthuyo kuti anayamba bwanji kuphunzira Baibulo. Mukamacheza kwambiri ndi “gulu lonse la abale,” simungasowe wocheza naye ndipo simungasungulumwe.—1 Petulo 2:17.

Lankhulani ndi munthu wina wamkulu. (Miyambo 17:17) Kusungulumwa kungachepe ngati muuza makolo anu kapena munthu wina wamkulu nkhawa zanu. Izi ndi zimene zinachitikira mtsikana wina wa zaka 16. Poyamba, iye ankadandaula kwambiri chifukwa chosowa munthu wocheza naye. Anati: “Ndikasungulumwa, ndinkafufuza chifukwa chake. Kenako ndinkakambirana ndi mayi ndipo ankandipatsa nzeru zothetsera vuto langa. Kulankhula ndi munthu wina kumathandiza.”

Ngati mukufuna kulankhula ndi winawake chifukwa chakuti kusungulumwa kwanu kukupitirira, kodi mungalankhule ndi ndani? Lembani dzina lake pansipa.

․․․․․

Muziganizira ena. (1 Akorinto 10:24) Baibulo limatiuza kuti ‘tisamangodzifunira zopindulitsa ife tokha basi, komanso zopindulitsa ena.’ (Afilipi 2:4) Ndi zoona kuti munthu ukasowa wocheza naye, umakhumudwa. Koma m’malo mongokhumudwabe, bwanji osaganiza zothandiza munthu wina? Muthanso kupeza anzanu ena m’njira imeneyi.

Ganizirani munthu wina aliyense, m’banja lanu kapena mumpingo mwanu, amene angafune kucheza naye kapena kum’thandiza. Lembani  dzina lake pansipa, ndi mmene mungamuthandizire.

․․․․․

Mukamachita zinthu zoganizira ena m’malo mongodziganizira nokha, simusungulumwa. Munthu woganizira ena amakhala ndi moyo waubwenzi ndipo anthu ambiri amafuna kucheza naye. Lemba la Miyambo 11:25 limati: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”

Muzisankha bwino ocheza nawo. (Miyambo 13:20) Ndi bwino kukhala ndi anzanu ochepa koma okukondani kwambiri kusiyana ndi kukhala ndi anzanu ambiri omwe angakuikeni m’mavuto. (1 Akorinto 15:33) Chitsanzo chabwino pankhani imeneyi, ndi Samueli wa m’Baibulo pamene anali mnyamata. Ayenera kuti ankasowa wocheza naye ku chihema. Anthu amene ankagwira nawo ntchito kumeneko, monga Hofeni ndi Pinehasi, sakanakhala anzake abwino. Iwo anali ndi makhalidwe oipa ngakhale kuti anali ana a mkulu wa ansembe. Samueli akanati agwirizane nawo, akanaika pachiswe moyo wake wauzimu. Iye sanafune kugwirizana nawo ngakhale pang’ono. Baibulo limati: “Ndipo mwanayo Samueli anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anam’komera mtima.” (1 Samueli 2:26) Anthu ake ati? N’zodziwikiratu kuti sanali Hofeni ndi Pinehasi, chifukwa mwina anthu amenewa ankamusala Samueli poona makhalidwe ake abwino. M’malo mwake, anthu amene ankamukonda Samueli chifukwa cha makhalidwe akewo, anali anthu amene ankatsatira mfundo za Mulungu zamakhalidwe abwino. Choncho, anzanu azikhala anthu amene amakonda Yehova.

Musataye Mtima. (Miyambo 15:15) Aliyense nthawi zina amaona ngati kuti anzake sakufuna kucheza naye. Koma kodi inu mungatani ngati mukuona choncho? M’malo motaya mtima, ganizirani za zinthu zabwino za pamoyo wanu. Ngakhale kuti simungathe kusintha zinthu zina pamoyo wanu, kumbukirani kuti mutha kusintha maganizo anu a mmene mumaonera zinthuzo.

Ngati mukuona kuti anthu sakufuna kucheza nanu, chitanipo kanthu kuti musinthe vutolo kapena kuti musinthe maganizo anu a mmene mukuonera vutolo. Kumbukirani kuti Yehova amadziwa bwino mmene mulili, ndipo amadziwa zimene mukusowa ndi mmene mungapezere zosowa zanuzo. Ngati nthawi zonse mumamva kuti mukusowa wocheza naye, muyenera kupemphera kwa Yehova. Ndipo dziwani kuti ‘iye adzakugwirizizani.’—Salmo 55:22.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mungatani ngati mukuona kuti mukusowa anzanu ocheza nawo?

▪ Kodi ndi malemba ati amene angakuthandizeni kukhala ndi maganizo abwino m’malo motaya mtima?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

Mfundo Zothandiza Kucheza ndi Anthu

Muzimwetulira. Anthu amakhala omasuka kucheza nanu akaona kuti ndinu wansangala.

Dzidziwikitseni. Tchulani dzina lanu ndi kumene mumakhala.

Muzifunsa mafunso. M’funseni munthuyo kuti akuuzeni za moyo wake. Koma pewani kufunsa mafunso ochititsa manyazi.

Muzimvetsera. Munthuyo akamalankhula muzingomvetsera, popanda kuganizira zoti munene akamaliza. Ngati mumamvetseradi, simudzasowa chonena.

Muzikhala omasuka Mungapeze anzanu ena chifukwa chocheza bwino ndi anthu. Choncho masukani pocheza ndi anthu.