Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?

Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?

 Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?

“Agogo anga aamuna onse aŵiri amakonda kusimba tinkhani. Tinkhani tawo timandithandiza kumvetsa bwino malingaliro anga.”—Joshua.

KALE anthu m’banja ankakonda kukhala moyandikana mibadwo ingapo—nthaŵi zambiri m’nyumba imodzi. Nthaŵi zonse anthu ankagwirizana kwambiri ndi agogo awo.

Masiku ano, kukhala motalikirana kungasiyanitse achinyamata ndi agogo awo. Ndiponso, mabanja ambiri atha posudzulana. Nyuzipepala ya The Toronto Star inanena kuti “agogo angavutikenso ndi chisudzulo ndipo sangathe kuona zidzukulu zawo zimene amakondazo.” Nthaŵi zina, vuto n’lakuti achinyamata ambiri amaipidwa ndi achikulire, ndipo amawaona ngati anthu achikale amene maganizo awo, khalidwe ndi zokonda zawo n’zosiyana kwambiri ndi za achinyamatawo. Zotsatirapo zake? Achinyamata ambiri sakondana ndi agogo awo monga momwe anayenera kuchitira.

Zimenezi n’zomvetsa chisoni. Monga momwe nkhani yapitayo m’nkhani zotsatizana zino inanenera, kukhala ndi ubale wolimba ndi agogo a munthuwe—makamaka ngati ali oopa Mulungu—n’kwabwino, kopindulitsa, ndiponso kosangalatsa. * Ponena za agogo ake, mtsikana wina dzina lake Rebekah akuti: “Nthaŵi zonse timaseka limodzi.” Mnyamata wina dzina lake Peter mofananamo akuti: “Sindiopa kuwafotokozera mmene ndikuganizira ndi zolinga zanga. Nthaŵi zina ndimakhala womasuka kulankhula nawo kusiyana ndi makolo anga. Ndimaganiza kuti ndingalankhule ndi agogo anga nkhani iliyonse.”

Bwanji inuyo? Mwina munali kuwakonda kwambiri agogo anu mukali wamng’ono. Koma popeza tsopano mwakula, mwina simunachitepo kanthu panopa kulimbitsa ubalewo. Ngati ndi choncho, mfundo yake ya uphungu wa m’Baibulo pa 2 Akorinto 6:11-13 ingagwire ntchito pankhaniyi. Mfundoyo imanena za ‘kukulitsa’ chikondi chanu kwa iwo. Funso n’lakuti, Motani?

Yambani Inuyo

‘Kukulitsa’ kukutanthauza kuti muyambe ndinu kuchitapo kanthu. Ndi iko komwe, Baibulo limati: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.” (Miyambo 3:27) Muli wamng’ono,  mwina simunali ‘wokhoza’ kuchita chilichonse chokhudza ubale wanu ndi agogo. Koma popeza mwakula, mungapeze kuti pali njira zambiri zoyenera zomwe mungatsatire.

Mwachitsanzo, ngati agogo anu amakhala pafupi, muziwachezera nthaŵi zonse. Kodi zimenezo ndi zotopetsa? Zingatero ngati mumangokhala phee. M’malo mwake, yambitsani nkhani. Kodi mungalankhule chiyani? Mfundo yachikhalidwe ya m’Baibulo pa Afilipi 2:4 ndi yothandiza. Imati “munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” M’mawu ena, khalani ndi chidwi mwa agogo anu. Alankhulitseni zinthu zimene amakonda. Akumva bwanji? Akhala akuchitanji? Mwina angakonde kusimba zakale. Choncho afunseni mmene analili akali aang’ono. Kapena, kodi bambo kapena mayi anu anali otani akali aang’ono? Ngati agogo anu ndi Akristu, afunseni chimene chinawakopa kuti alandire choonadi cha Baibulo.

Nthaŵi zambiri, agogo ali ngati nkhokwe zimene tingapezemo chidziŵitso chochuluka cha mbiri ya banja, ndipo mwina amafunitsitsa kukusangalatsani ndi nkhani zochititsa chidwi. Ndithudi, kucheza ndi agogo anu kungakhale kosangalatsa zedi. Yesani kuwafunsa mafunso, mwina mukumalemba notsi kapena kujambula pakaseti kapena pavidiyo. Ngati simukudziŵa chomwe mungawafunse, pemphani makolo anu akuthandizeni kukonza mafunso oyenera. Mosakayikira mudzaphunzira zinthu zambiri zimene zidzakuthandizani kuwadziŵa bwino agogo anu, makolo anu, ndiponso inu eni. Joshua ananena kuti: “Agogo anga aamuna onse aŵiri amakonda kusimba tinkhani. Tinkhani tawo timandithandiza kumvetsa bwino malingaliro anga.”

Musaiŵalenso kuti agogo anu amafuna kudziŵa za moyo wanu ndi zochita zanu. Mukawauza zomwe mukuchita, ndiye kuti mukufuna kuti azikuthandizani pamoyo wanu. Ndithudi, zimenezi zidzalimbitsa ubale wanu. Mnyamata wina ku France dzina lake Igor akuti: “Ine ndi agogo anga aakazi timakonda kumwera limodzi tiyi m’kantini, ndipo timakambirana zimene tachita posachedwa.”

Kodi Tingachitire Limodzi Zinthu Ziti?

Mukangoyamba kulankhulana, mwinanso mungayambe kuchitira limodzi zinthu zina. Kungoganiza pang’ono kaye, mungapeze kuti pali zambiri zimene mutha kuchitira limodzi. Mtsikana wina dzina lake Dara akukumbukira kuti: “Agogo anga aakazi onse aŵiri andiphunzitsa kuphika, kuika zakudya m’zitini, kuphika buledi, kubzala ndi kusamalira mbewu ndi maluŵa.” Army amatsagana ndi agogo ake kumapwando a banja ndi kutchuti. Agogo ena ndi okangalika malinga ndi msinkhu wawo. Aaron amakonda kuseŵera mpira wa gofu ndi agogo ake aakazi. Joshua amapha nsomba ndiponso kugwira ntchito zina zapakhomo limodzi ndi agogo ake aamuna.

Ngati agogo anu amalambira Yehova, zingakhale zosangalatsa kwambiri kuchitira limodzi ntchito zokhudza kulambira Yehova, monga kuuza ena za m’Baibulo. Igor anapita ndi agogo ake aakazi kumsonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova ku Poland. Iye akuti: “Zimene tinachitazi n’zosaiwalika, ndipo timakonda kukamba za msonkhanowo.” Zoonadi, agogo ena sangathe kuyenda ulendo ngati umenewu. Komabe, mungapindule kwambiri ngati mucheza nawo.

Choloŵa Chauzimu

Nthaŵi za m’Baibulo mkazi wotchedwa Loisi anachita mbali yofunika kwambiri kuthandiza mdzukulu wake, Timoteo, kukhala munthu wa Mulungu wabwino kwambiri. (2 Timoteo 1:5) N’zosadabwitsa kuti agogo ambiri achikristu akuchita chimodzimodzi lerolino. Ponena za agogo ake, Joshua akuti: “Anayamba kutumikira Yehova ine ndisanabadwe, choncho ndimawalemekeza kwambiri chifukwa ndi agogo komanso chifukwa cha kukhulupirika kwawo.” Amy akuti: “Agogo anga nthaŵi zonse amati ndimawalimbikitsa ndi kuwasangalatsa potumikira Yehova mokhulupirika. Komabe, chitsanzo chawo chabwino ndi changu chawo kwa Yehova monga apainiya [alaliki a nthaŵi zonse] zandilimbikitsa kupitirizabe utumiki wanga waupainiya.”

Chris anati agogo ake ndiye “munthu amene  anandilimbikitsa kwambiri kuphunzira ndi kukula mwauzimu.” Akuwonjeza kuti: “Sindidzaiŵala mawu awo akuti ‘tizichita zonse zomwe tingathe potumikira Yehova.’” Agogo ake a Pedro anam’thandiza kwambiri kukula mwauzimu. Iye akuti: “Nzeru yawo yandithandiza kwambiri. Agogo anga amanditenga nthaŵi zonse kukalalikira, ndipo ndikuyamikira kwambiri zimenezo.” Ndithudi, kukhala ndi ubale wolimba ndi agogo oopa Mulungu kungakuthandizeni kutumikira Mulungu mokwanira.

Agogo Amene Amakhala Kutali

Bwanji ngati agogo anu amakhala kutali? Ngati n’kotheka, yesetsani kuwachezera nthaŵi zonse. Pamene mukuyembekezera kudzawachezera ulendo wina, chitani zomwe mungathe kupitiriza kulankhulana. Hornan amakawaona agogo ake katatu kokha pachaka, koma iye akuti: “Ndimalankhula nawo patelefoni Lamlungu lililonse.” Dara, yemwenso amakhala kutali ndi agogo ake, akuti: “Amafuna kudziŵa za moyo wanga, ndipo timalankhulana patelefoni kapena kutumizirana makalata pakompyuta pafupifupi mlungu uliwonse.” Inde, kutumizirana makalata pakompyuta ndi kulankhulana patelefoni n’zoyenera, koma musanyalanyaze kufunika kwa njira yachikale ya kalata yolemba pamanja. Achinyamata ambiri adabwa kupeza kuti agogo awo anasunga makalata onse amene achinyamatawo analemba kuyambira akali aang’ono. Makalata angaŵerengedwe mobwerezabwereza—n’kuwasunga. Choncho, onetsetsani kuti mukulemba makalata!

Agogo amakonda zidzukulu zawo mwapadera kwabasi. (Miyambo 17:6) Pali njira zambiri zolimbikitsira ubale wanu ndi agogo, kaya akukhala pafupi kapena kutali. Inde, yetsetsani.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziŵana ndi Agogo Anga?” m’kope lathu la May 8, 2001.