Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI?

Kodi Ubwino Wowerenga Baibulo Ndi Wotani?

Kodi Ubwino Wowerenga Baibulo Ndi Wotani?

“Ndinkaganiza kuti Baibulo ndi lovuta kumvetsa.”—Jovy

“Ndinkaona ngati nkhani zake n’zotopetsa.”—Queennie

“Ndinkaona kuti Baibulo ndi lalikulu kwambiri moti sindinkafuna n’komwe kuliwerenga.”—Ezekiel

Kodi munaganizapo zowerenga Baibulo koma kenako n’kugwa ulesi mofanana ndi anthu amene tawatchula pamwambawa? Anthu ambiri amaona kuti sangakwanitse kuwerenga Baibulo. Koma kodi mungafune kuliwerenga mutadziwa kuti likhoza kukuthandizani kukhala ndi moyo wosangalala? Nanga mungamve bwanji mutadziwa kuti pali zinthu zimene zingakuthandizeni kuti kuwerenga Baibulo kuzikusangalatsani?

Taonani zimene anthu ena ananena atayamba kuwerenga Baibulo n’kuona ubwino wake.

Ezekiel, yemwe ndi wazaka za m’ma 20, anati: “Poyamba ndinkachita zinthu ngati munthu amene akuyendetsa galimoto popanda kwenikweni kumene akupita. Koma kuwerenga Baibulo kwandithandiza kukhala ndi moyo wabwino chifukwa lili ndi malangizo amene amandithandiza tsiku ndi tsiku.”

Mtsikana wina dzina lake Frieda, yemwenso ndi wazaka za m’ma 20, ananena kuti: “Sindinkachedwa kuyambana ndi anzanga. Koma panopa ndimatha kuugwira mtima chifukwa chowerenga Baibulo. Zimenezi zandithandiza kuti ndisamavutike kugwirizana ndi anthu ena, moti panopa ndili ndi anzanga ambiri.”

Mayi wina wazaka za m’ma 50, dzina lake Eunice, anati: “Baibulo landithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kusiya zinthu zoipa.”

Baibulo lingakuthandizeni kukhala ndi moyo wosangalala mofanana ndi mmene lathandizira anthu amene tawatchulawa komanso anthu ena ambiri. (Yesaya 48:17, 18) Mwachitsanzo, likhoza kukuthandizani kusankha zinthu mwanzeru, kupeza anzanu abwino, kuchepetsa nkhawa ndiponso kuphunzira mfundo zoona zokhudza Mulungu, chomwe ndi chinthu chofunika kwambiri. Malangizo a m’Baibulo amachokera kwa Mulungu ndipo sangakugwiritseni fuwa la moto. Zili choncho chifukwa Mulungu sangapereke malangizo olakwika.

Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuyamba kuwerenga Baibulo komanso kusangalala poliwerenga?