Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI

Kodi Ndingayambe Bwanji?

Kodi Ndingayambe Bwanji?

Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzipindula powerenga Baibulo? Taonani mfundo 5 zimene zathandiza anthu ambiri.

Muzipeza malo abwino. Muziyesetsa kupeza malo aphee komanso opanda zinthu zimene zingakulepheretseni kuika maganizo pa zimene mukuwerenga. Malowo azikhala owala mokwanira ndiponso odutsa mpweya wabwino n’cholinga choti muzipindula ndi zimene mukuwerengazo.

Muzikhala ndi maganizo oyenera. Baibulo ndi lochokera kwa Atate wathu wakumwamba. Choncho mukamaliwerenga, mungachite bwino kukhala ndi maganizo ofanana ndi a mwana yemwe amafunitsitsa kuphunzira zinthu kwa bambo ake achikondi. Ngati muli kale ndi zikhulupiriro kapena maganizo enaake okhudza Baibulo, muziyesetsa kuti musamaganizire zimenezo powerenga. Zimenezi zingachititse kuti Mulungu azikuthandizani kuzindikira mfundo zoona.—Salimo 25:4.

Muzipemphera musanayambe kuwerenga. Maganizo amene ali m’Baibulo ndi a Mulungu. Choncho iyeyo ndi amene angatithandize kuti tilimvetse. Mulungu analonjeza kuti azipereka “mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Mzimuwu ungakuthandizeni kumvetsa maganizo a Mulungu. Mukapitiriza kumadalira mzimuwu, ukhoza kukuthandizani kumvetsa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”—1 Akorinto 2:10.

Muzimvetsa zimene mukuwerenga. Musamangoti bola kuwerenga. Muziganizira kwambiri zimene mukuwerengazo. Muzidzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi munthu wa m’nkhani imene ndawerengayi anali ndi makhalidwe abwino ati? Kodi ndingasonyeze bwanji makhalidwewa pa moyo wanga?’

Muzikhala ndi cholinga. Kuti muzipindula mukamawerenga Baibulo, muziyesetsa kuphunzira mfundo inayake imene ingakuthandizeni pa moyo wanu. Mukhoza kukhala ndi zolinga monga kuphunzira zinthu zambiri zokhudza Mulungu, kuphunzira mfundo zimene zingakuthandizeni kukhala munthu wabwino, kapena zimene zingathandize kuti banja lanu liziyenda bwino. Kenako mungasankhe nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kukwaniritsa zolingazo. *

Mfundo 5 zimenezi zingakuthandizeni kuyamba kuwerenga Baibulo. Koma kodi mungatani kuti kuwerengako kuzikhala kosangalatsa kwambiri? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

^ ndime 8 Ngati simukudziwa nkhani za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanu, a Mboni za Yehova angakuthandizeni.