Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI

Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?

Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?

Kodi mumaona kuti kuwerenga Baibulo n’kotopetsa, kapena kosangalatsa? Zimene mumachita powerenga n’zimene zingachititse kuti muzisangalala kapena ayi. Tiyeni tione zimene mungachite kuti muzisangalala powerenga Baibulo.

Muziwerenga Baibulo lolondola komanso losavuta. Ngati mutamawerenga Baibulo limene lili ndi mawu ambiri ovuta kapena akalekale omwe simukuwadziwa, kuwerengako sikungakusangalatseni. Choncho mungachite bwino kupeza Baibulo losavuta kumva limene lingakufikeni pamtima. Komabe muyenera kutsimikizira kuti Baibulolo linamasuliridwa molondola. *

Mungawerenge pogwiritsa ntchito chipangizo chamakono. Masiku ano mukhoza kuwerenganso Baibulo pa intaneti kapena kulichita dawunilodi kuti muziwerengera pakompyuta, tabuleti kapena pafoni. Mabaibulo ena amakhala ndi zinthu zokuthandizani kuona mwamsanga mavesi osiyanasiyana okhudza nkhani imene mukuwerenga komanso kuona mmene Mabaibulo ena anamasulirira mavesi amene mukuwerenga. M’zilankhulo zina, Baibulo limapezekanso longomvetsera. Anthu ambiri amakonda kumvetsera Baibulo akakwera basi, akamachapa kapena kuchita zinthu zina. Kodi mungayeseko zina mwa zinthu zimene tatchulazi?

Muzigwiritsa ntchito zinthu zothandiza pophunzira Baibulo. Pali zinthu zina zimene zingakuthandizeni kwambiri powerenga Baibulo. Mwachitsanzo, pali mapu a madera otchulidwa m’Baibulo omwe angakuthandizeni kudziwa pamene pali malo enaake ndiponso  kumvetsa nkhani imene mukuwerenga. Nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda kapena za pachigawo chakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa” pawebusaiti ya jw.org, zingakuthandizeni kumvetsa nkhani zambiri za m’Baibulo.

Muzisinthasintha njira zowerengera. Ngati mumaona kuti kuwerenga Baibulo kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso n’kovuta, mukhoza kuyamba ndi nkhani imene imakusangalatsani kwambiri. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza anthu otchuka a m’Baibulo, mungayambe ndi kuwerenga za anthuwo. Mukhoza kuwerenga malemba amene ali m’bokosi lakuti “ Anthu a M’Baibulo Amene Mungawerenge Nkhani Zawo.” Apo ayi, mwina mungafune kuwerenga malemba onse okhudza nkhani inayake kapena kuwerenga potsatira nthawi imene zinthu zinachitika. Mungachite bwino kuyesa imodzi mwa njira zimene tatchulazi.

^ ndime 4 Anthu ambiri amaona kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ndi lolondola, lodalirika komanso losavuta kuwerenga. Baibuloli linapangidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezeka m’zilankhulo zoposa 130. Mukhoza kuchita dawunilodi Baibulo limeneli pawebusaiti ya jw.org kapena pa pulogalamu ya JW Library. Komanso ngati mungakonde, a Mboni za Yehova akhoza kukupatsani Baibuloli.

^ ndime 46 Mabukuwa akupezeka m’Chingelezi.