Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzikoli langodzaza ndi mavuto okhaokha. Koma kodi Mulungu ndi amene akuchititsa zimenezi?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.” (Yobu 34:10) Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa komanso mavuto amene timakumana nawo.

Mfundo zinanso zomwe Baibulo limanena

  • Satana Mdyerekezi, yemwe ndi ‘wolamulira wa dzikoli,’ ndi amene amachititsa mavuto ambiri.—Yohane 14:30.

  • Anthu amakumananso ndi mavuto chifukwa chosasankha zinthu mwanzeru.—Yakobo 1:14, 15.

Kodi mavutowa adzatha?

Anthu ena amakhulupirira kuti anthu akhoza kuthetsa mavuto ngati atamachita zinthu limodzi polimbana ndi mavutowo, pomwe ena amaona kuti n’zosatheka kuti zinthu zisinthe kwambiri m’dzikoli. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

Mulungu adzathetsa mavuto. Baibulo limati: “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Mfundo zinanso zomwe Baibulo limanena

  • Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu kuti athetse mavuto onse amene Mdyerekezi wachititsa.—1 Yohane 3:8.

  • Anthu abwino adzakhala mwamtendere padzikoli mpaka kalekale.—Salimo 37:9-11, 29.