Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | INOKI

‘Mulungu Anakondwera Naye’

‘Mulungu Anakondwera Naye’

INOKI anali atakhala ndi moyo kwa zaka 365. Kwa ifeyo zingakhale zovuta kumvetsa kuti munthu angakhale ndi moyo nthawi yaitali chonchi chifukwa masiku ano anthu ambiri amangokhala ndi moyo zaka 70 kapena 80 zokha. Komatu Inoki sanali ndi zaka zambiri tikamuyerekezera ndi anthu ena amasiku amenewo. Nthawi imeneyo, yomwe ndi zaka zoposa 5,000 zapitazo, anthu ankakhala ndi moyo zaka zambiri kuposa masiku ano. Inoki anabadwa Adamu, yemwe ndi munthu woyamba kulengedwa, ali ndi zaka zoposa 600 ndipo anakhalabe ndi moyo zaka zina 300. Ndipotu ana ena a Adamu anakhala ndi moyo zaka zoposa pamenepa. Choncho, ngakhale kuti Inoki anali ndi zaka 365, ayenera kuti ankaonekabe wamphamvu ngati munthu woti akhalabe zaka zina zambiri. Komatu si mmene zinakhalira.

Zimene zinachitika tsiku lina zinasonyeza kuti moyo wa Inoki unali pa ngozi. Iye ankathawa anthu amene anali atangowauza kumene uthenga wochokera kwa Mulungu. Nkhope zawo zinkachita kuonekeratu kuti ndi olusa ndipo amadana naye. Iwo ankadana ndi uthenga wake komanso Mulungu amene anamutuma. Zinali zosatheka kuti amenyane ndi Yehova amene anatuma Inoki koma akanatha kuphwetsera mkwiyo wawo pa Inokiyo. N’kutheka kuti Inoki ankaganizira za mkazi wake ndiponso ana ake aakazi, kapena za mwana wake wamwamuna dzina lake Metusela. Mwinanso ankaganiza za Lameki yemwe anali mdzukulu wake ndipo n’kutheka kuti ankakayikira ngati adzaonanenso ndi anthuwa. (Genesis 5:21-23, 25) Koma kodi zinatha bwanji?

Baibulo silinena zambiri za Inoki, moti pali mabuku atatu okha amene amafotokoza za iye ndipo amangomufotokoza mwachidule. (Genesis 5:21-24; Aheberi 11:5; Yuda 14, 15) Komabe zimene zimafotokozedwa m’mabukuwa zimatithandiza kudziwa kuti Inoki anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ngati muli ndi udindo wosamalira banja kapena ngati munakumanapo ndi mavuto enaake chifukwa chotsatira zimene mumakhulupirira, ndiye kuti chitsanzo cha Inoki chingakuthandizeni.

“INOKI ANAYENDABE NDI MULUNGU WOONA”

Inoki anabadwa pa nthawi imene makhalidwe a anthu anali atafika poipa kwambiri. Iye anali wa m’badwo wa 7 kuchokera pa Adamu. Anthu a pa nthawiyi anali adakali ndi matupi amphamvu komanso olimba chifukwa anabadwa pasanapite nthawi yaitali kuchokera pa Adamu ndi Hava, omwe poyamba anali angwiro. N’chifukwa chake ankakhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Komabe anthuwa sankachita zimene Mulungu ankafuna ndipo zachiwawa zinali paliponse. Zimenezi zinayamba pamene Kaini anapha m’bale wake Abele. Zikuonekanso kuti mdzukulu wina wa Kaini ankadzitama kuti anali wachiwawa kuposa agogo akewo. Kenako anthu anayamba “kuitanira pa dzina la Yehova” koma osati pofuna kumupembedza. Iwo ankagwiritsa ntchito dzinali mopanda ulemu ndiponso monyoza.—Genesis 4:8, 23-26.

Mu nthawi ya Inoki kupembedza konyenga kunali kutafala kwambiri. Choncho Inoki ankafunika kusankha pakati pa kutsatira zimene anthu ambiri ankachitazi kapena kutsatira Yehova Mulungu amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Koma kodi anasankha ziti? Inoki ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri atamva za Abele amene anaphedwa chifukwa choti ankalambira Yehova. Choncho nayenso anasankha kulambira Yehova. Lemba la Genesis 5:22 limati: “Inoki anayendabe ndi Mulungu woona.” Vesili likusonyeza kuti Inoki anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anthu ambiri a pa nthawiyo sankalambira Mulungu. Iye ndi munthu woyamba amene Baibulo limamufotokoza chonchi.

Vesili limanenanso kuti Inoki anayendabe ndi Yehova atabereka mwana wake wamwamuna dzina lake Metusela. Inoki anayamba kubereka ana ali ndi zaka pafupifupi 65. Baibulo silitchula dzina la mkazi wake kapena kuti anabereka ‘ana aamuna ndi aakazi’ angati. Koma kuti bambo ayendebe ndi Mulungu kwinaku akusamalira banja lake, ayenera kusamalira banjalo m’njira imene ingasangalatse Mulungu. Inoki ankadziwa zoti Yehova ankafuna kuti iye akhalebe wokhulupirika kwa mkazi wake. (Genesis 2:24) N’zosakayikitsa kuti ankayesetsanso kuphunzitsa ana ake za Yehova Mulungu. Koma kodi zimenezi zinathandizadi anawa?

Baibulo silinena zambiri pa nkhani imeneyi. Silinenanso chilichonse za chikhulupiriro cha Metusela, yemwe anakhala ndi moyo zaka zambiri kuposa anthu onse a m’Baibulo, ndipo anamwalira m’chaka chimene kunachitika Chigumula. Metusela anabereka mwana wamwamuna dzina lake Lameki. Inoki anakhalabe ndi moyo kwa zaka zoposa 100 Lameki atabadwa. Lameki atakula ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Yehova anamugwiritsa ntchito kuti alosere zokhudza Nowa, yemwe anali mwana wake, ndipo ulosiwu unakwaniritsidwa pambuyo pa Chigumula. Mofanana ndi Inoki, Baibulo limanena kuti Nowa ankayenda ndi Mulungu. Nowa sanamuonepo Inoki, koma mwina ankadziwa za mbiri yake yabwino. N’kutheka kuti anamva za Inoki kuchokera kwa bambo ake, a Lameki, kapena kwa agogo ake, a Metusela, kapenanso kwa Yaredi, yemwe anali bambo ake a Inoki ndipo anamwalira Nowa ali ndi zaka 366.—Genesis 5:25-29; 6:9; 9:1.

Inoki anali wosiyana kwambiri ndi Adamu. Zili choncho chifukwa Adamu anali wangwiro koma anachimwira Yehova n’kusiyira ana ake chitsanzo choipa komanso mavuto okhaokha. Inoki sanali wangwiro komabe anayenda ndi Mulungu ndipo anasiyira ana ake chitsanzo chabwino chokhala wokhulupirika. Adamu anamwalira Inoki ali ndi zaka 308. Kodi ana a Adamu analira bambo awo odzikondawo atamwalira? Sitikudziwa. Chomwe tikungodziwa n’choti Inoki “anayendabe ndi Mulungu woona.”—Genesis 5:24.

Ngati mukusamalira banja, pali zambiri zimene mungaphunzire kwa Inoki. N’zoona kuti muyenera kupezera a m’banja lanu zofunika pa moyo koma chofunika kwambiri ndi kuwathandiza kukonda Yehova. (1 Timoteyo 5:8) Zimene mumalankhula komanso kuchita zingawathandize kukonda Yehova. Mukamayenda ndi Mulungu n’kumachita zimene iye amafuna ngati mmene Inoki ankachitira, nanunso mudzasiyira banja lanu chitsanzo chabwino kwambiri.

INOKI ‘ANALOSERA ZA IWO’

Chifukwa choti anthu ambiri ankachita zoipa n’kutheka kuti Inoki ankaona kuti analibe anzake otumikira nawo Mulungu. Komatu Yehova Mulungu ankamuona kuti ndi wofunika. Tsiku lina Yehova analankhula ndi mtumiki wake wokhulupirikayu n’kumupatsa uthenga woti akauze anthu ena. Choncho Inoki anakhala mneneri wa Yehova ndipo ndi mneneri woyamba yemwe uthenga wake ukupezeka m’Baibulo. Izi zili choncho chifukwa patapita zaka zambiri, Yuda, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, analemba uthengawo m’buku lake la m’Baibulo. *

Uthenga wa Inoki unali wakuti: “Taonani! Yehova anabwera ndi miyandamiyanda ya oyera ake, kudzapereka chiweruzo kwa onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha ntchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazichita mosaopa Mulungu, komanso chifukwa cha zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ochimwa osaopa Mulungu anamunenera.” (Yuda 14, 15) Mukhoza kuona kuti Inoki analankhula uthenga wakewu ngati kuti zinthuzo zinali zitachitika kale. Umu ndi mmene maulosi ambiri analembedwera. Aneneriwo ankafotokoza chonchi chifukwa choti sankakayikira ngakhale pang’ono kuti zimene akunenazo zidzachitikadi.—Yesaya 46:10.

Inoki ankauza anthu uthenga wa Mulungu molimba mtima ngakhale kuti ankadana naye

Kodi mukuganiza kuti Inoki ankamva bwanji pamene ankauza anthu ena za uthengawu? Uthengawu unali wamphamvu kwambiri chifukwa anagwiritsa ntchito mawu akuti “osaopa Mulungu” kangapo podzudzula anthuwo komanso pofotokoza zimene ankachita. Uthengawu unasonyeza kuti kungoyambira nthawi imene Adamu ndi Hava anatulutsidwa mu Edeni, zinthu zinali zikungoipiraipirabe. Unachenjezanso anthu kuti Yehova adzabwera ndi angelo ake ambirimbiri kuti adzawononge anthu oipa onse. Ngakhale kuti Inoki anali yekha, anauza anthu uthengawu molimba mtima. Pa nthawiyi n’kuti Lameki ali mwana ndipo ngati anaona agogo ake akuchita zinthu molimba mtima chonchi, ayenera kuti anadabwa kwambiri.

Tikaganizira zimene Inoki anachita tingachite bwino kudzifunsa ngati timaona zinthu za m’dzikoli mmene Mulungu amazionera. Uthenga umene Inoki anapereka ukukhudzanso anthu amasiku ano. Mogwirizana ndi zimene Inoki anachenjeza, Yehova anabweretsa Chigumula chachikulu chimene chinawononga anthu oipa a m’nthawi ya Nowa. Zimene zinachitikazi zikusonyeza zimene zidzachitikenso m’tsogolo. (Mateyu 24:38, 39; 2 Petulo 2:4-6) Mofanana ndi nthawi ya Nowa, Mulungu limodzi ndi angelo ake ambirimbiri ndi okonzeka kuperekanso chiweruzo kwa anthu onse oipa. Choncho aliyense wa ife ayenera kumvera chenjezo la Inoki komanso kuthandiza nawo pochenjeza anthu ena. N’kutheka kuti achibale komanso anzathu sangagwirizane ndi zimene tikuchita ndipo tikhoza kumva ngati tili tokhatokha. Koma Yehova sanasiye Inoki ndipo sangasiyenso atumiki ake okhulupirika masiku ano.

“INOKI ANASAMUTSIDWA KUTI ASAFE MOZUNZIKA”

Kodi Inoki zinamuthera bwanji? Chochititsa chidwi kwambiri pa moyo wa Inoki ndi mmene anafera. Buku la Genesis limanena kuti: “Inoki anayendabe ndi Mulungu woona. Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anam’tenga.” (Genesis 5:24) Kodi mawu oti “Mulungu anam’tenga” akutanthauza chiyani? Pa nthawi ina mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mwa chikhulupiriro, Inoki anasamutsidwa kuti asafe mozunzika, moti sanapezeke kwina kulikonse chifukwa Mulungu anamusamutsa. Pakuti asanasamutsidwe, Mulungu anamuchitira umboni kuti akukondwera naye.” (Aheberi 11:5) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti “anasamutsidwa kuti asafe mozunzika”? Mabaibulo ena amanena kuti Mulungu anamutenga n’kupita naye kumwamba. Koma zimenezi n’zosatheka chifukwa Baibulo limasonyeza kuti Yesu Khristu ndi amene anali woyambirira kupita kumwambako.—Yohane 3:13.

Choncho funso n’lakuti, kodi Inoki “anasamutsidwa” bwanji kuti “asafe mozunzika”? Zikuoneka kuti Yehova anachititsa kuti Inoki amwalire n’cholinga choti asaphedwe mwankhanza. Koma asanamwalire “Mulungu anamuchitira umboni kuti akukondwera naye.” N’kutheka kuti Inoki atatsala pang’ono kumwalira, Mulungu anamuonetsa masomphenya a mmene dzikoli lidzaonekere likadzakhala paradaiso. Inoki ataona umboni umenewu wosonyeza kuti Yehova akusangalala naye, anamwalira. Pamene mtumwi Paulo ankalemba za Inoki komanso atumiki ena okhulupirika a Mulungu, ananena kuti: “Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro.” (Aheberi 11:13) Atamwalira, adani ake ayenera kuti ankasakasaka kumene kunali mtembo wake koma ‘sunapezeke kwina kulikonse.’ Mwina Yehova anausowetsa n’cholinga choti anthuwo asauwononge kapena kuugwiritsa ntchito pa kulambira konyenga. *

Tikaganizira zimene malembawa akunena, kodi Inoki anafa bwanji? Mwina zimene zinachitika n’zoti atathawa kwa nthawi yaitali, anatopa kwambiri. Adani ake ankamuthamangitsabe ndipo ankachita kuonekeratu kuti ndi okwiya kwambiri chifukwa cha uthenga wake. Kenako Inoki anapeza malo oti n’kubisala koma ankadziwa kuti ngati atachedwapo akhoza kumugwira. Ankadziwa kuti akamugwira amupha mwankhanza. Akupuma, anayamba kupemphera kwa Mulungu. Kenako mtima wake unayamba kukhala m’malo ndipo anaona masomphenya.

Inoki ayenera kuti anali atatsala pang’ono kuphedwa mwankhanza pamene Yehova anamutenga

Taganizirani zimene mwina Inoki anaona m’masomphenyawo. Ayenera kuti anaona dziko lokongola kwambiri losiyana ndi mmene dziko linalili pa nthawiyo. Dziko limene anaonalo linali lokongola ngati munda wa Edeni, koma kunalibe akerubi otchinga kuti anthu asalowemo. M’dzikolo munali amuna ndi akazi ambirimbiri ndipo onse ankaoneka amphamvu komanso athanzi. Anthu onse ankakhala mwamtendere ndipo kunalibe zochitira nkhanza atumiki a Mulungu ngati mmene zinalili ndi iyeyo. Ataona zimenezi, anadziwa kuti Yehova amamukonda ndipo akusangalala naye. Anadziwanso kuti m’tsogolo adzakhala m’dziko langati limeneli. Mtima wake unakhala m’malo, moti anayamba kusinza mpaka anagona tulo tofa nato.

Iye sanadzukenso chifukwa anafera kutulo komweko. Koma sikuti Yehova anamuiwala. Ndipo Yesu analonjeza kuti tsiku lina anthu onse amene Mulungu akuwakumbukira adzamva mawu a Yesuyo ndipo adzauka. Pa nthawiyo dzikoli lidzakhala lokongola kwambiri komanso lamtendere.—Yohane 5:28, 29.

Kodi nanunso mungakonde kudzakhala m’dziko lokongolali? Tangoganizirani mmene zingakhalire mutakumana ndi Inoki. Mukhoza kudzaphunzira zinthu zochititsa chidwi kwa iye. Akhoza kudzatiuza ngati zimene tafotokoza m’nkhaniyi ndi zimene zinamuchitikiradi. Koma pali mfundo yofunika kwambiri imene tingaphunzire kwa iye panopa. Paulo atafotokoza za Inoki, anati: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Choncho tonse tiyenera kutsanzira Inoki pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro komanso kuchita zinthu molimba mtima.

^ ndime 14 Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti uthenga wa Inoki umene Yuda analemba anautenga m’buku lakuti Buku la Inoki. Koma Yuda sakanatenga uthengawu m’bukuli chifukwa nkhani zambiri za m’bukuli ndi zongopeka komanso si zoona kuti linalembedwa ndi Inoki ndipo silikudziwika kumene linachokera. N’zoona kuti bukuli lili ndi uthenga wa Inoki koma mwina olemba ake anautenga m’zolemba zina zakale kapena anachita kuuzidwa ndi anthu ena. N’kutheka kuti uthenga wa Inoki umene Yuda analembawu anautenganso kumene olemba Buku la Inoki anatenga uthengawu. Apo ayi, mwina anamva kwa Yesu, yemwe anali kumwamba pamene Inoki anali ndi moyo.

^ ndime 20 Mofanana ndi zimenezi, Mulungu ayeneranso kuti anaonetsetsa kuti adani ake asapeze mtembo wa Mose komanso wa Yesu.—Deuteronomo 34:5, 6; Luka 24:3-6; Yuda 9.