Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 3

Kubadwa kwa Wokonza Njira

Kubadwa kwa Wokonza Njira

LUKA 1:57-79

  • KUBADWA KWA YOHANE M’BATIZI KOMANSO ZIMENE ZINACHITIKA POM’PATSA DZINA

  • ZEKARIYA ANANENERATU NTCHITO IMENE YOHANE ADZAGWIRE

Elizabeti anali atatsala pang’ono kubereka ndipo panali patadutsa miyezi itatu akukhala limodzi ndi m’bale wake Mariya. Koma tsopano Mariya anaganiza zoyamba ulendo wautali wobwerera kwawo ku Nazareti, komwe kunali kumpoto kwa mapiri a ku Yudeya. Pa nthawiyi nayenso ankayembekezera kuti pakapita miyezi 6 abereka mwana.

Mariya atangochoka, Elizabeti anabereka mwana. Zinali zosangalatsa kuti Elizabeti anabereka bwinobwino ndipo iye limodzi ndi mwanayo anali athanzi. Achibale komanso anthu ena anasangalala kwambiri Elizabeti atawaonetsa mwanayo.

Pa nthawiyi Mulungu anali atalamula Aisiraeli kuti mwana wamwamuna azidulidwa komanso kupatsidwa dzina pa tsiku la 8 kuchokera pamene wabadwa. (Levitiko 12:2, 3) Anthu ena ankafuna kuti mwana wa Elizabeti apatsidwe dzina la bambo ake lakuti Zekariya. Koma Elizabeti anakana ndipo ananena kuti: “Limenelo iyayi! Dzina lake akhala Yohane.” (Luka 1:60) Kumbukirani kuti mngelo Gabirieli anali atanena kuti adzamupatse dzina lakuti Yohane.

Koma achibale komanso anthu ena ananena kuti: “Palibe wachibale wako aliyense wotchedwa ndi dzina limenelo.” (Luka 1:61) Kenako anthuwo pogwiritsa ntchito manja anafunsa Zekariya kuti atchule dzina limene ankafuna kupatsa mwanayo. Zekariya anapempha cholembapo chathabwa ndipo analemba kuti: “Dzina lake ndi Yohane.”—Luka 1:63.

Atangotero Zekariya anayambanso kulankhula. Mwina mukukumbukira kuti iye anasiya kulankhula chifukwa sanakhulupirire zimene mngelo ananena zoti Elizabeti adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndiyeno Zekariya atangoyamba kulankhula, anthu onse anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani kwenikweni?” (Luka 1:66) Anthuwo anaona kuti dzanja la Mulungu linali pa mwanayo poona zimene zinachitika kuti mwanayo apatsidwe dzina.

Kenako, motsogoleredwa ndi mzimu woyera Zekariya ananena kuti: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, chifukwa wacheukira anthu ake ndi kuwapatsa chipulumutso. Iye watikwezera ife nyanga yachipulumutso  m’nyumba ya mtumiki wake Davide.” (Luka 1:68, 69) Pamene Zekariya ananena kuti “nyanga yachipulumutso” ankanena za Ambuye Yesu amene anali atatsala pang’ono kubadwa. Iye ananena kuti kudzera mwa Yesu, Mulungu “pambuyo pakuti tapulumutsidwa m’manja mwa adani, atipatse mwayi wochita utumiki wopatulika kwa iye mopanda mantha, mokhulupirika ndi mwachilungamo pamaso pake masiku athu onse.”—Luka 1:74, 75.

Ponena za mwana wake, Zekariya ananeneratu zimene adzachite m’tsogolo kuti: “Kunena za iwe, mwanawe, udzatchedwa mneneri wa Wam’mwambamwamba, pakuti udzatsogola pamaso pa Yehova kuti ukakonzeretu njira zake. Kukadziwitsa anthu ake za chipulumutso pokhululukidwa machimo awo, chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu. Ndi chifundo chimenechi, kuwala kwa m’mawa kudzatifikira kuchokera kumwamba, ndipo kudzaunikira amene akhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa, ndi kutsogolera bwinobwino mapazi athu panjira yamtendere.” (Luka 1:76-79) Kunena zoona, ulosiwu unali wolimbikitsa kwambiri.

Pa nthawiyi, n’kuti Mariya yemwe anali asanakwatiwe atafika kwawo ku Nazareti. Kodi chinachitika n’chiyani zitadziwika kuti akuyembekezera kukhala ndi mwana?