Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 7

Okhulupirira Nyenyezi Anapita Kukaona Yesu

Okhulupirira Nyenyezi Anapita Kukaona Yesu

MATEYU 2:1-12

  • NYENYEZI INAWATSOGOLERA KU YERUSALEMU KENAKO KWA YESU

Kudera la Kum’mawa kunali anthu ena omwe ankakhulupirira nyenyezi. Iwo ankakhulupirira kuti akhoza kudziwiratu zimene zichitike pa moyo wa munthu poona mmene nyenyezi zikuyendera. (Yesaya 47:13) Ndiyeno tsiku lina ali kwawoko, anaona nyenyezi ndipo anayamba kuitsatira. Nyenyeziyo inawatsogolera ku Yerusalemu osati ku Betelehemu ndipo ulendowu unali wautali kwambiri.

Atafika ku Yerusalemu okhulupirira nyenyeziwo anafunsa kuti: “Ili kuti mfumu ya Ayuda imene yabadwa? Chifukwa pamene tinali kum’mawa, tinaona nyenyezi yake ndipo tabwera kudzaigwadira.”—Mateyu 2:1, 2.

Mfumu Herode, yomwe inkalamulira ku Yerusalemu pa nthawiyo, itamva za nkhaniyi inakwiya kwambiri. Choncho inaitanitsa ansembe onse aakulu ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda n’kuwafunsa kumene Khristu adzabadwire. Chifukwa chodziwa zimene Malemba ananena, iwo anayankha kuti: “Adzabadwira ku Betelehemu.” (Mateyu 2:5; Mika 5:2) Nthawi yomweyo Herode anaitanitsa okhulupirira nyenyezi aja mwamseri n’kuwauza kuti: “Pitani mukam’funefune mwanayo mosamala, ndipo mukakam’peza mudzandidziwitse, kuti nanenso ndipite kukam’gwadira.” (Mateyu 2:8) Koma cholinga chenicheni cha Herode chinali choti akamupeza mwanayo amuphe.

Okhulupirira nyenyeziwo atangonyamuka, nyenyezi yomwe inkawatsogolera ija inaonekeranso. Izi zikuonetseratu kuti nyenyezi imeneyi si inali nyenyezi wamba koma inachita kutumizidwa kuti iwatsogolere. Okhulupirira nyenyeziwo anaitsatirabe mpaka pamene inakaima pa nyumba imene Yosefe ndi Mariya ankakhala.

Iwo atalowa m’nyumbamo, anapeza Mariya atanyamula Yesu. Okhulupirira nyenyeziwo anagwada ndi kuweramira Yesu. Anamupatsanso mphatso za golide, lubani ndi mule. Koma pamene ankati azibwerera kwa Herode, Mulungu anawachenjeza kudzera m’maloto kuti asapitenso kumeneko. Choncho anadzera njira ina pobwerera kwawo.

Kodi mukuganiza kuti ndi ndani amene anatumiza nyenyezi imene inatsogolera anthuwa? Kumbukirani kuti poyamba nyenyeziyo siinayambe n’kuwatsogolera ku Betelehemu kumene kunali Yesu. M’malomwake inawatsogolera ku Yerusalemu kumene anakakumana ndi Mfumu Herode, yomwe inkafuna kupha Yesu. Mfumuyi ikanaphadi Yesu zikanakhala kuti Mulungu sanalowererepo pochenjeza okhulupirira nyenyeziwo kuti asabwererenso kwa Herode kukamuuza kumene Yesu anali. Zimenezi zikusonyeza kuti nyenyeziyo inatumizidwa ndi mdani wa Mulungu, yemwe ndi Satana. Iye anagwiritsa ntchito njira imeneyi pofuna kukwaniritsa cholinga chake chofuna kupha Yesu.