Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 5

Kodi Yesu Anabadwa Liti Ndipo Anabadwira Kuti?

Kodi Yesu Anabadwa Liti Ndipo Anabadwira Kuti?

LUKA 2:1-20

  • YESU ANABADWIRA KU BETELEHEMU

  • ABUSA ANAPITA KUKAONA YESU ATANGOBADWA

Kaisara Augusito, yemwe anali mfumu ya Ufumu wa Roma, analamula kuti aliyense apite kwawo kuti akalembetse m’kaundula. Choncho Yosefe ndi Mariya anafunika kupita kwawo kumzinda wa Betelehemu, womwe unali kum’mwera kwa Yerusalemu.

Mzinda wa Betelehemu unadzaza ndi anthu amene anabwera kudzalembetsa m’kaundula. Chifukwa cha zimenezi, kunali kovuta kupeza malo ogona moti Yosefe ndi Mariya anapeza malo m’khola la abulu ndi nyama zina. Ndipo Yesu anabadwira m’kholamo. Atabadwa, Mariya anamukulunga m’nsalu ndipo anamugoneka mu chodyetsera nyamazo.

Mulungu ndi amene anachititsa kuti Kaisara Augusito apereke lamulo la kalemberayu. Tikutero chifukwa zimenezi zinachititsa kuti Yesu abadwire ku Betelehemu, womwe unali mzinda wa kwawo kwa Mfumu Davide. Malemba anali ataneneratu kukadali zaka zambiri kuti Wolamulira amene analonjezedwa adzabadwira mumzinda umenewu.—Mika 5:2.

Usiku umene Yesu anabadwa unali wapadera kwambiri. Abusa omwe anali kutchire kodyetsa nkhosa anaona kuwala kodabwitsa kutazungulira pamalo pamene anakhala. Kuwalako kunasonyeza ulemelero wa Yehova. Kenako mmodzi mwa angelo a Mulungu anauza abusawo kuti: “Musaope! Ine ndabwera kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu chimene anthu onse adzakhala nacho. Chifukwa lero wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye, mumzinda wa Davide. Ndikukupatsani chizindikiro ichi: Mukapeza mwana wakhanda wokutidwa m’nsalu, atagona modyeramo ziweto.” Mwadzidzidzi, panaoneka khamu lalikulu lakumwamba pamodzi ndi mngeloyo, likutamanda Mulungu kuti: “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”—Luka 2:10-14.

Angelowo atangochoka abusawo anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu tikaone zimene zachitikazo, zimene Yehova watidziwitsa.” (Luka 2:15) Iwo anapita mwamsanga ndipo anakam’pezadi Yesu kumene mngelo uja anawauza. Abusawo atafotokoza zimene mngelo uja anawauza, aliyense amene anamva za nkhaniyi anadabwa kwambiri. Mariya ankamvetsera mwatcheru ndipo anasunga mawu onsewa komanso ankaganizira tanthauzo la zimenezi mumtima mwake.

Masiku ano, anthu ambiri amakhulupirira kuti Yesu anabadwa pa 25 December. Koma ku Betelehemu, m’mwezi wa December kumakhala mvula komanso kumazizira kwambiri. Ndipo nthawi zina kumagwa sinoo. M’nyengo imeneyi, abusa sangakadyetse nkhosa zawo kutchire n’kumakagonera komweko. Komanso wolamulira wa Ufumu wa Roma sakanauza anthu, omwe sankasangalala kale ndi ulamuliro wake, kuti ayende m’nyengo yovutayi ulendo wa masiku angapo kukalembetsa. Choncho, pali umboni wosonyeza kuti Yesu anabadwa cha mu October.