Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 10

Yosefe ndi Banja Lake Anapita ku Yerusalemu

Yosefe ndi Banja Lake Anapita ku Yerusalemu

LUKA 2:40-52

  • YESU ALI NDI ZAKA 12 ANAFUNSA MAFUNSO APHUNZITSI

  • YESU ANANENA KUTI YEHOVA NDI ‘ATATE WAKE’

Banja la Yosefe, achibale ake komanso anthu ena ananyamuka ulendo wopita ku Yerusalemu. Ulendowu unkachitika chaka ndi chaka kuti akakhale nawo pa chikondwerero cha Pasika potsatira zimene Chilamulo chinkanena. (Deuteronomo 16:16) Ulendo wochoka ku Nazareti kupita ku Yerusalemu unali wautali makilomita pafupifupi 120. Anthu ankatanganidwa kwambiri komanso ankasangalala nthawiyi ikamayandikira. Yesu, yemwe pa nthawiyi anali ndi zaka 12, ankayembekezera mwachidwi kukakhala nawo pa chikondwerero chimenechi komanso kupita kukachisi.

Mwambo wa Pasika womwe unkachitika tsiku limodzi ukatha, Yosefe ndi banja lake ankakhalabe kwa masiku angapo ku Yerusalemu. Tsiku la Pasika likadutsa, tsiku lotsatiralo ankayamba “chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa” chomwe chinkatenga masiku 7. (Maliko 14:12) Chikondwererochi chinkaonedwanso ngati mbali ya mwambo wa Pasika. Ulendo wonse wopita ku Yerusalemu n’kubwereranso ku Nazareti unkawatengera milungu iwiri. Koma pa nthawiyi, ulendo wawo unatenga masiku ambiri chifukwa cha vuto limene analizindikira pobwerera ku Nazareti.

Pamene ankabwerera kwawo, Yosefe ndi Mariya ankaganiza kuti Yesu ali limodzi ndi achibale komanso anzawo ena omwe ankayenda nawo limodzi. Koma usiku ataima pamalo ena kuti agone, anazindikira kuti Yesu wasowa. Choncho anayamba kumufunafuna ngati anali ndi anzawo ena koma sanamupeze. Kenako Yosefe ndi Mariya anabwerera ku Yerusalemu kuti akamuyang’ane.

Atafika ku Yerusalemu, anamufunafuna kwa tsiku lathunthu koma osamupeza. Anamufunafunanso tsiku lachiwiri koma sanamupeze. Kenako pa tsiku lachitatu, anakamupeza ali mkatikati mwa kachisi pakati pa aphunzitsi a Chiyuda akuwafunsa mafunso komanso akumvetsera mayankho awo moti aphunzitsiwo anadabwa kwambiri ndi nzeru zake.

Atamupeza, Mariya anamufunsa kuti: “Mwanawe, n’chifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Ine ndi bambo akowa tinada nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna.”—Luka 2:48.

Yesu anadabwa kuti makolo akewo sanadziwe kumene iye anali, moti anawafunsa kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simunadziwe kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?”—Luka 2:49.

Kenako Yesu anabwerera ku Nazareti ndi makolo ake ndipo anapitiriza kuwamvera. Anapitirizabe kukula ndipo ankachita zinthu mwanzeru. Ngakhale kuti anali wamng’ono, Yesu ankachita zinthu zokondweretsa Mulungu ndipo ankakondedwa ndi anthu. Choncho kuyambira ali mwana, Yesu anali chitsanzo chabwino pa nkhani yokonda zinthu zauzimu komanso kulemekeza makolo ake.