Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 8

Anathawa Mfumu Yankhanza

Anathawa Mfumu Yankhanza

MATEYU 2:13-23

  • MAKOLO A YESU ANATHAWIRA KU IGUPUTO

  • YOSEFE NDI BANJA LAKE ANASAMUKIRA KU NAZARETI

Pakati pa usiku, mngelo wa Yehova anaonekera kwa Yosefe n’kumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo. Ukakhale kumeneko kufikira nthawi imene ndidzakuuze, chifukwa Herode akukonza zoyamba kufunafuna mwanayu kuti amuphe.”—Mateyu 2:13.

Nthawi yomweyo, Yosefe anadzutsa Mariya n’kumuuza za uthengawo. Yosefe, Mariya ndi mwanayo ananyamuka usiku womwewo. Anachita bwino kunyamuka nthawi yomweyo chifukwa pa nthawiyi Herode anali atazindikiranso kuti okhulupirira nyenyezi aja amupusitsa. Paja Herode anali atawauza kuti adzamuuze kumene kuli Yesu koma iwo sanachite zimenezi ndipo Herode anakwiya kwambiri. Pofunitsitsa kuti Yesu aphedwe, Herode analamula kuti ana onse aamuna osapitirira zaka ziwiri a ku Betelehemu komanso m’madera onse ozungulira aphedwe. Iye analamula kuti ana onse osapitirira zaka ziwiri aphedwe chifukwa anali atawerengetsera nthawi imene okhulupirira nyenyezi aja anabwera.

Zinali zochititsa mantha komanso zomvetsa chisoni kwambiri kuona anawo akuphedwa. Sitikudziwa kuti ndi ana angati amene anaphedwa koma chomwe tikudziwa n’chakuti, kulira mofuula komanso momvetsa chisoni kwa azimayi a anawo kunakwaniritsa ulosi wa m’Baibulo umene Mulungu anauza mneneri Yeremiya kuti alembe.—Yeremiya 31:15.

Pa nthawi imene zonsezi zinkachitika, n’kuti Yosefe ndi banja lake ali ku Iguputo komwe anathawira. Koma usiku wina mngelo wa Yehova anaonekeranso kwa Yosefe m’maloto n’kumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo upite m’dziko la Isiraeli, chifukwa amene anali kufuna moyo wa mwanayu anafa.” (Mateyu 2:20) Chifukwa cha uthengawu, Yosefe anaganiza zobwerera kwawo. Zimenezi zinakwaniritsa ulosi winanso wa m’Baibulo wakuti Mwana wa Mulungu adzatuluka mu Iguputo.—Hoseya 11:1.

 Poyamba, Yosefe anaganiza zoti akakhale ku Yudeya, mwina chakufupi ndi tauni ya Betelehemu komwe ankakhala asanathawire ku Iguputo. Koma asanafike ku Yudeya anamva kuti Arikelao mwana wa Herode ndi amene ankalamulira monga mfumu ya Yudeya. Mulungu analankhulanso ndi Yosefe kudzera m’maloto ndipo anamuchenjeza kuti asapite ku Yudeya. Choncho Yosefe ndi banja lake analowera chakumpoto n’kukakhala ku Galileya, mumzinda wa Nazareti, womwe unali kutali ndi likulu la chipembedzo chachiyuda. Yesu anakulira mumzinda umenewu, zomwe zinakwaniritsanso ulosi wakuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”—Mateyu 2:23.