Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 124

Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa

Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa

MATEYU 26:47-56 MALIKO 14:43-52 LUKA 22:47-53 YOHANE 18:2-12

  • YUDASI ANAPEREKA YESU M’MUNDA WA GETSEMANE

  • PETULO ANADULA KHUTU LA MUNTHU WINA

  • YESU ANAMANGIDWA

Yudasi anafika kumene kunali Yesu nthawi itapitirira 12 koloko usiku. Pa nthawiyi ansembe anali atagwirizana zoti alipire Yudasi ndalama 30 zasiliva kuti apereke Yesu. Choncho Yudasi anatsogolera gulu la ansembe aakulu, Afarisi komanso gulu la asilikali achiroma pamodzi ndi mtsogoleri wawo pamene ankafunafuna Yesu. Pamene asilikaliwo ankapita komwe kunali Yesu anatenga zida.

Zikuoneka kuti Yudasi anapita kwa ansembe aakulu Yesu atangomutulutsa m’chipinda chimene anachitira mwambo wa Pasika. (Yohane 13:27) Ansembe aakuluwo anasonkhanitsa alonda komanso gulu la asilikali. N’kutheka kuti poyamba Yudasi anapita ndi anthuwo kunyumba imene Yesu ndi atumwi ake anachitirako mwambo wa Pasika. Koma atachoka kumeneko, Yudasi ndi gululo anawoloka chigwa cha Kidironi n’kulowera kumunda wa Getsemane. Kuwonjezera pa zida zimene ananyamula zija, anthuwo anatenganso miyuni ndi nyale zomwe zikusonyeza kuti anali okonzeka kukafunafuna Yesu.

Pamene Yudasi ndi gulu la anthuli ankakwera phiri la Maolivi, Yudasi ankadziwa kumene akanapeza Yesu. Tikutero chifukwa masiku angapo apitawo, Yesu ndi atumwi ake ankakonda kuima m’munda wa Getsemane akamapita ku Yerusalemu komanso pobwerera ku Betaniya. Koma poti unali usiku, Yesu ayenera kuti anabisika ndi zithunzithunzi za mitengo ya maolivi yomwe inali m’mundamo. Ndiye kodi asilikaliwo, omwe mwina anali asanaonepo Yesu, akanamuzindikira bwanji? Pofuna kuwathandiza, Yudasi anawauza kuti akawapatsa chizindikiro. Iye anawauza kuti: “Amene ndim’psompsone ndi ameneyo. Mum’gwire ndi kupita naye osam’taya.”—Maliko 14:44.

Atafika m’mundamo Yudasi anaona Yesu ali ndi atumwi ake ndipo anapita pamene panali Yesu n’kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu Rabi!” Kenako anapsompsona Yesu mwachikondi. Koma Yesu anamufunsa kuti: “Bwanawe, ukupezeka kuno ndi cholinga chotani?” (Mateyu 26:49, 50) Yesu anadziyankha yekha ponena kuti: “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa munthu mwa kupsompsona?” (Luka 22:48) Kenako Yesu anasiya kuganizira zimene Yudasi anachita ndipo anayamba kulankhula ndi gulu la anthulo.

Yesu anayandikira gulu la anthulo moti miyuni ndi nyale zimene anthuwo anatenga zinkamuunika. Iye anawafunsa kuti: “Mukufuna ndani?” Iwo anayankha kuti: “Yesu Mnazareti.” Yesu ananena molimba mtima kuti: “Ndine amene.” (Yohane 18:4, 5) Pamenepo anthuwo anagwa pansi chifukwa choti sankadziwa zimene zichitike.

Yesu akanatha kuthawa pa nthawi imeneyi koma anangoima n’kuwafunsanso kuti akufuna ndani. Anthuwo atayankhanso kuti, “Yesu Mnazareti,” iye anawayankha mtima uli m’malo kuti: “Ndakuuzani kuti ndine amene. Choncho ngati mukufuna ine, awa alekeni azipita.” N’zochititsa chidwi kuti ngakhale pa nthawi yovuta ngati imeneyi, Yesu anakumbukira zimene ananena kuti sadzatayapo ophunzira ake ngakhale mmodzi. (Yohane 6:39; 17:12) Yesu anasunga atumwi ake okhulupirika ndipo sanataye ngakhale mmodzi kupatulapo Yudasi, yemwe anali “mwana wa chiwonongeko.” (Yohane 18:7-9) Choncho anapempha kuti anthuwo alole ophunzira ake kuti azipita.

Atumwiwo ataona kuti asilikali omwe anagwa aja adzuka n’kupita pamene panali Yesu, anazindikira zimene zinkachitika. Kenako anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?” (Luka 22:49) Koma Yesu asanayankhe, Petulo anasolola limodzi mwa malupanga awiri omwe atumwiwo anali nawo. Nthawi yomweyo anadula khutu la kudzanja lamanja la wantchito wa mkulu wa ansembe yemwe dzina lake linali Makasi.

Koma Yesu anagwira khutu la Makasi n’kumuchiritsa. Kenako anaphunzitsa mfundo yofunika kwambiri ndipo anauza Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake , pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”Yesu anali wokonzeka kuti anthu amugwire chifukwa kenako ananena kuti: “Nanga Malemba amene ananeneratu kuti izi ziyenera kuchitika adzakwaniritsidwa bwanji?” (Mateyu 26:52, 54) Ndiyeno ananenanso kuti: “Kodi sindiyenera kumwa za m’kapu imene Atate wandipatsa?” (Yohane 18:11) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yesu ankafunitsitsa kuti zofuna za Mulungu zichitike moti analolera kufa.

Ndiyeno Yesu anafunsa gulu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba? Tsiku  ndi tsiku ndinali kukhala pansi m’kachisi ndi kuphunzitsa, koma simunandigwire. Koma zonsezi zachitika kuti malemba a aneneri akwaniritsidwe.”—Mateyu 26:55, 56.

Gulu la asilikali, mkulu wa asilikali komanso akuluakulu a Ayuda anagwira Yesu n’kumumanga. Atumwi ataona zimenezi anathawa. Koma “mnyamata wina” sanathawe nawo. N’kutheka kuti mnyamata ameneyu anali Maliko yemwe anali wophunzira wa Yesu ndipo cholinga chake chinali choti azitsatira kumene gululo linkapita ndi Yesu. (Maliko 14:51) Anthu ena pa gululo anazindikira mnyamatayu ndipo ankafuna kumugwira. Chifukwa cha zimenezi mnyamatayu anathawa n’kusiya nsalu yake.