Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 134

M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali Ataukitsidwa

M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali Ataukitsidwa

MATEYU 28:3-15 MALIKO 16:5-8 LUKA 24:4-12 YOHANE 20:2-18

  • YESU ANAUKITSIDWA

  • ZIMENE ZINACHITIKA KU MANDA A YESU

  • ANAONEKERA KWA AZIMAYI ANGAPO

Azimayi omwe anapita kumanda a Yesu anadabwa kwambiri atapeza kuti m’mandamo mulibe thupi la Yesu. Mariya Mmagadala anathamanga kupita kwa “Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina, amene Yesu anali kumukonda.” Wophunzira ameneyo anali mtumwi Yohane. (Yohane 20:2) Koma azimayi ena omwe anatsalira kumanda kuja anaona mngelo. Mkati mwa mandawo munalinso mngelo wina yemwe ‘anavala mkanjo woyera.’—Maliko 16:5.

Mmodzi wa angelowo anawauza kuti: “Musachite mantha, chifukwa ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa. Iye sali pano chifukwa wauka kwa akufa monga ananenera. Bwerani muone pamene anagona. Ndipo pitani mwamsanga mukauze ophunzira ake kuti wauka kwa akufa, moti padakali pano, watsogola kupita ku Galileya.” (Mateyu 28:5-7) Kenako azimayiwo ‘akunjenjemera ndi kunthunthumira kwambiri’ anapita kukauza ophunzira a Yesu zimene zinachitikazo.—Maliko 16:8.

Pa nthawiyi n’kuti Mariya atakumana ndi Petulo komanso Yohane. Mtima ukadali m’mwamba anauza atumwiwo kuti: “Ambuye awachotsa m’manda achikumbutso aja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.” (Yohane 20:2) Petulo ndi Yohane atangomva zimenezi analiyatsa liwiro. Yohane anathamanga kwambiri moti ndi amene anayambirira kukafika kumandako. Atafika anasuzumira m’mandamo ndipo anaonamo nsalu zomwe anakulungira Yesu koma iye anakhalabe kunja kwa mandawo.

Koma Petulo anangofikira kulowa ndipo anapeza nsalu zomwe anakulungira Yesu komanso imene anamukulungira kumutu. Kenako Yohane analowa ndipo anaona kuti zimene Mariya anawauza zija zinali zoona. Ngakhale kuti Yesu anali atawauza kale kuti adzaukitsidwa, pa nthawiyi ophunzira akewo sanazindikire kuti waukitsidwa. (Mateyu 16:21) Ophunzirawo anabwerera kwawo atasokonezeka kwambiri. Koma Mariya atabwereranso kumanda kuja sanafune kuchokako.

Mmene zimenezi zinkachitika n’kuti azimayi ena aja akupita kukauza ophunzira ena kuti Yesu waukitsidwa. Ali m’njira anakumana ndi Yesu ndipo anawapatsa  moni kuti: “Moni amayi!” Azimayiwo anagwada ‘n’kuweramitsa nkhope zawo pansi.’ Kenako Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga, kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.”—Mateyu 28:9, 10.

Asilikali omwe anali kumanda kuja “ananjenjemera ndipo anangouma gwaa ngati akufa” chifukwa cha chivomezi chomwe chinachitika komanso chifukwa chakuti anaona angelo. Koma atadzuka anapita mumzinda ndipo “anakauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitika.” Kenako ansembewo anapita kukakambirana ndi akulu ndipo anagwirizana kuti apatse ndalama asilikali omwe ankalondera kumandawo. Anachita zimenezi n’cholinga choti anthu akawafunsa za nkhaniyi azinama kuti: “Ophunzira ake anabwera usiku kudzamuba ife titagona.”—Mateyu 28:4, 11, 13.

Asilikali achiroma ankatha kuphedwa ngati apezeka akugona pa malo awo antchito, choncho ansembewo analonjeza alondawo kuti: “Bwanamkubwa akamva zimenezi [zoti amagona pa nthawi ya ntchito], tikamunyengerera ndipo inu musade naye nkhawa.” (Mateyu 28:14) Asilikaliwo analandiradi ndalamazo ndipo anachita zimene ansembewo anawauza moti nkhani yoti thupi la Yesu labedwa inafala kwa Ayuda ambiri.

Mariya Mmagadala anali adakali kumanda kuja akulira. Atasuzumira m’manda muja anaona angelo awiri atavala zovala zoyera. Mngelo mmodzi anakhala kumene kunali mutu wa Yesu ndipo wina anakhala kumene kunali mapazi ake. Angelowo anamufunsa kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira?” Mariya anayankha kuti: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.” Kenako Mariya atatembenuka anaona kuti kumbuyo kwake kuli munthu. Munthu uja anamufunsanso funso limene angelo aja anamufunsa koma anawonjezeranso funso lina kuti: “Kodi Ukufuna ndani?” Mariya ankaganiza kuti munthuyo ndi wosamalira munda ndipo anamuuza kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika, ndipo ine ndikamutenga.”—Yohane 20:13-15.

Mariya sankadziwa kuti akulankhula ndi Yesu yemwe anali ataukitsidwa. Koma atangonena kuti, “Mariya!” Mariyayo anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu chifukwa cha mmene anamuitanira. Nthawi yomweyo Mariya ananena mosangalala kuti: “Rabboni!” (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”) Iye ankaganiza kuti Yesu akwera kumwamba nthawi yomweyo choncho anamugwira mwamphamvu. Koma Yesu anamuuza kuti: “Usandikangamire. Pakuti sindinakwerebe kwa Atate. Koma pita kwa abale anga ukawauze kuti, ‘Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.’”—Yohane 20:16, 17.

Mariya anathamangira kumene atumwi komanso otsatira ena a Yesu anasonkhana. Atafika anawauza kuti: “Ambuye ndawaona ine!” Zimene Mariya anawauzazi zinangowonjezera zomwe anali atamva kale kuchokera kwa azimayi ena. (Yohane 20:18) Komabe iwo ankangoona ngati zimene azimayiwo anawauza ndi “zopanda pake.”—Luka 24:11.