Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 120

Anali Ngati Nthambi Zobala Zipatso Komanso Anali Mabwenzi a Yesu

Anali Ngati Nthambi Zobala Zipatso Komanso Anali Mabwenzi a Yesu

YOHANE 15:1-27

  • MTENGO WA MPESA WENIWENI NDI NTHAMBI ZAKE

  • ZIMENE MUNTHU ANGACHITE KUTI APITIRIZE KUKONDEDWA NDI YESU

Yesu analimbikitsa atumwi ake okhulupirika ndipo analankhula nawo monga mabwenzi ake a pamtima. Nthawiyi unali usiku kwambiri mwinanso kupitirira 12 koloko ya usiku. Kenako Yesu anauza atumwi akewo fanizo lolimbikitsa kwambiri.

Iye anayamba kufotokoza fanizolo kuti: “Ine ndine mtengo wa mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye mlimi.” (Yohane 15:1) Fanizoli ndi lofanana ndi zimene zinafotokozedwapo zaka zambiri m’mbuyomo zokhudza mtundu wa Isiraeli womwe unkadziwika monga mtengo wa mpesa wa Yehova. (Yeremiya 2:21; Hoseya 10:1, 2) Koma pa nthawiyi Yehova anali atakana mtunduwu. (Mateyu 23:37, 38) Choncho m’fanizoli, Yesu ananena mfundo yatsopano. Ananena kuti iyeyo ndi mtengo wa mpesa umene Atate wake ankaulimira kuchokera pa nthawi imene Yesuyo anadzozedwa ndi mzimu woyera m’chaka cha 29 C.E. Koma zimene Yesu ananena zinasonyeza kuti mtengo wa mpesawo umaimiranso zinthu zina osati iye yekha. Iye ananena kuti:

“Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso [Atate wanga] amaidula, ndipo iliyonse yobala zipatso amaiyeretsa mwa kuitengulira kuti ibale zipatso zambiri. . . . Nthambi singabale zipatso payokha, pokhapokha ngati ndi yolumikizikabe kumpesawo. Chimodzimodzi inunso, simungabale zipatso mukapanda kukhala olumikizika kwa ine. Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake.”—Yohane 15:2-5.

Yesu anali atangolonjeza ophunzira ake okhulupirika kuti akadzapita kumwamba, adzawatumizira mzimu woyera womwe udzawathandize. Patapita masiku 51, atumwiwo pamodzi ndi anthu ena analandira mzimu woyera ndipo pa nthawiyi anakhala nthambi za mtengo wa mpesa. Ndipotu atumwi pamodzi ndi anthu enawo, omwe anapanga “nthambi” za mtengo wa mpesa, anayenera kukhala ogwirizana ndi Yesu. N’chifukwa chiyani zimenezi zinali zofunika?

Yesu ananena kuti: “Amene ali wolumikizika kwa ine, inenso n’kukhala wolumikizika kwa iye, ameneyo amabala zipatso zochuluka, chifukwa simungathe kuchita kalikonse popanda ine.” Choncho otsatira okhulupirika a Yesu omwe anali ngati “nthambi” za mtengo wa mpesa, akanatha kubala zipatso zambiri potsanzira makhalidwe a Yesu, kulalikira za Ufumu wa Mulungu mwakhama komanso kuthandiza anthu ambiri kuti akhale ophunzira ake. Kodi chikanachitika n’chiyani ngati munthu akanasiya kugwirizana ndi Yesu komanso kubala zipatso? Yesu ananena kuti: “Ngati munthu sakhala wolumikizika kwa ine, amaponyedwa kunja.” Komanso Yesu ananena kuti: “Ngati mukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.”—Yohane 15:5-7.

Kenako Yesu anabwerezanso mfundo yomwe anali atainenapo kawiri m’mbuyomo. Mfundoyi ndi yokhudza kusunga malamulo ake. (Yohane 14:15, 21) Iye anafotokoza zinthu zimene zikanathandiza atumwiwo kudziwa ngati ankatsatiradi malamulo ake. Ananena kuti: “Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.” Komabe munthu amene amakonda Yehova Mulungu ndi Mwana wake ayenera kuchitanso zinthu zina. Yesu ananena kuti: “Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukonderani. Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake. Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.”—Yohane 15:10-14.

Patadutsa maola ochepa Yesu anapereka moyo wake m’malo mwa anthu onse amene amamukhulupirira ndipo zimenezi zinasonyeza kuti amawakonda kwambiri. Zimene Yesu anachitazi zimalimbikitsa otsatira ake kuti azitengera chitsanzo chake posonyezana chikondi chololera kuvutikira ena. Chikondi chimenechi chidzathandiza kuti anthu adzawazindikire ngati mmene Yesu ananenera kuti: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:35.

Atumwiwo ayenera kuti anamvetsa zimene zinachititsa Yesu kuti awatchule kuti “mabwenzi.” Yesu ananena kuti: “Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.” Atumwiwa analitu ndi mwayi wapadera kwambiri wokhala pa ubwenzi ndi Yesu komanso wodziwa zimene Atate wake anamuuza. Koma kuti azigwirizanabe ndi Yesu ankafunika ‘kupitiriza kubala zipatso.’ Kenako Yesu anawauza zimene zikanachitika ngati akanatsatiradi mfundo imeneyi. Iye anati: ‘Chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa adzakupatsani.’—Yohane 15:15, 16.

Ngati ophunzirawa, omwe anali ngati nthambi za mtengo wa mpesa, akanapitiriza kukondana akanatha kupirira mavuto amene anali atatsala pang’ono kukumana nawo. Anawachenjeza kuti dziko lidzadana nawo koma anawalimbikitsanso kuti: “Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu. Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Koma popeza simuli mbali ya dzikoli, . . . pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.”—Yohane 15:18, 19.

Yesu anafotokozanso chifukwa china chimene chidzachititse dziko kudana ndi atumiki ake. Iye ananena kuti: “Adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.” Yesu ananena kuti zozizwitsa zimene ankachita zinachititsa kuti anthu amene ankadana naye akhale ndi mlandu pamaso pa Mulungu chifukwa ananena kuti: “Ndikanapanda kuchita pakati pawo ntchito zimene wina aliyense sanachitepo, akanakhala opanda tchimo, koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga.” Zimene anthu amenewa ankachita podana ndi Yesu zinkakwaniritsa ulosi.—Yohane 15:21, 24, 25; Salimo 35:19; 69:4.

Yesu anawalonjezanso kuti adzawatumizira mzimu woyera kuti udzawathandize. Mzimu woyerawu womwe ndi wamphamvu kwambiri umathandiza otsatira onse a Yesu ‘kuchitira umboni,’ komwe ndi kubala zipatso.—Yohane 15:27.