Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 112

Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru

Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru

MATEYU 25:1-13

  • YESU ANANENA FANIZO LA ANAMWALI 10

Yesu anayankha funso limene atumwi ake anamufunsa pamene ankafuna kudziwa chizindikiro cha kukhalapo kwake komanso chizindikiro chakuti dziko la Satanali latsala pang’ono kutha. Chifukwa chodziwa zimene zinkadetsa nkhawa atumwi ake, Yesu ananena fanizo lina pofuna kuwapatsa malangizo othandiza. Anthu amene adzakhale ndi moyo m’nthawi ya kukhalapo kwake ndi amene adzaone kukwaniritsidwa kwa zimene Yesu ananena m’fanizoli.

Iye anayamba kunena fanizoli kuti: “Ufumu wakumwamba udzakhala ngati anamwali 10 amene anatenga nyale zawo n’kupita kukachingamira mkwati. Anamwali asanu anali opusa, ndipo asanu anali ochenjera.”—Mateyu 25:1, 2.

Yesu sankatanthauza kuti hafu ya ophunzira ake amene adzalandire nawo Ufumu wakumwamba ndi opusa ndipo enawo ndi ochenjera. Koma iye ankatanthauza kuti pa nkhani yokhudza Ufumu, wophunzira wake aliyense ayenera kusankha kukhala tcheru kapena kulola kuti asokonezedwe. Ndipotu Yesu sankakayikira kuti mtumiki wake aliyense adzakhala wokhulupirika komanso kuti adzalandira madalitso ochokera kwa Atate ake.

M’fanizoli, anamwali onse 10 anapita kukalandira mkwati komanso anakhala nawo m’gulu loperekeza mkwati. Pamene mkwatiyo akufika ndi mkwatibwi wake kunyumba imene amukonzera, anamwaliwa ankayenera kuyatsa nyale zawo kuti amuunikire njira posonyeza kuti akupereka ulemu. Koma kodi chinachitika n’chiyani?

Yesu ananena kuti: “Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta owonjezera. Koma  ochenjerawo anatenga mafuta owonjezera m’mabotolo awo limodzi ndi nyale zawo. Popeza kuti mkwati anali kuchedwa, onse anayamba kuwodzera kenako anagona.” (Mateyu 25:3-5) Mkwatiyo sanafike pa nthawi imene ankamuyembekezera moti anamwaliwo anayamba kugona poona kuti wachedwa kwambiri. Atumwiwo ayenera kuti anakumbukira fanizo limene Yesu ananena la munthu wina wa m’banja lachifumu amene anapita kudziko lakutali ndipo patapita nthawi ‘anabwerera kwawo pambuyo polandira ufumu.’—Luka 19:11-15.

M’fanizoli, Yesu ananenanso zimene zinachitika mkwati atafika. Ananena kuti: “Pakati pa usiku kunamveka mawu ofuula akuti, ‘Mkwati uja wafika! Tulukani mukam’chingamire.’” (Mateyu 25:6) Kodi anapezadi anamwaliwo ali okonzeka komanso ali tcheru?

Yesu anapitiriza kuti: “Nthawi yomweyo anamwali onsewo anadzuka ndi kukonza nyale zawo. Opusa aja anauza ochenjera kuti, ‘Tigawireniko mafuta anu, chifukwa nyale zathu zatsala pang’ono kuzima.’ Ochenjerawo anayankha kuti, ‘Mwina satikwanira tikagawana ndi inu. Pitani kwa ogulitsa kuti mukagule anu.’”—Mateyu 25:7-9.

Choncho anamwali 5 opusa aja sanakhale tcheru ndipo sanakonzekere kufika kwa mkwati. Analibe mafuta okwanira m’nyale zawo ndipo anafunika kupeza mafuta ena. Yesu ananena kuti: “Atanyamuka kupita kukagula, mkwati anafika, ndipo anamwali okonzekerawo analowa naye limodzi m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa. Pambuyo pake anamwali ena aja nawonso anafika n’kunena kuti, ‘Ambuye, ambuye, titsegulireni!’ Poyankha iye anati, ‘Kunena zoona, sindikukudziwani inu.’” (Mateyu 25:10-12) Anamwaliwo anakumana ndi zinthu zomvetsa chisoni chifukwa sanali okonzeka komanso chifukwa chakuti sanali tcheru.

Atumwiwo anadziwa kuti Yesu ndiye anali mkwati wa m’fanizoli chifukwa nthawi inanso m’mbuyomo anadziyerekezerapo ndi mkwati. (Luka 5:34, 35) Nanga anamwali ochenjerawo ankaimira ndani? Pamene Yesu ankanena za “kagulu ka nkhosa,” kamene kadzapatsidwa Ufumu ananena kuti: “Mangani m’chiuno mwanu ndipo nyale zanu zikhale chiyakire.” (Luka 12:32, 35) Choncho atumwiwo anazindikira kuti pamene Yesu ankanena fanizo la anamwali ankanena za iwowo. Ndiye kodi mfundo ya Yesu inali yoti chiyani ponena fanizoli?

Mfundo ya Yesu inali yodziwikiratu chifukwa anamaliza n’kunena kuti: “Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—Mateyu 25:13.

Pamenepatu n’zoonekeratu kuti Yesu analangiza otsatira ake okhulupirika kuti ayenera ‘kukhalabe maso’ pa nthawi ya kukhalapo kwake. Iye adzabwera ndithu ndipo otsatira akewa ayenera kukhala okonzeka komanso kuchita zinthu mwakhama mofanana ndi anamwali 5 ochenjera aja. Zimenezi zikanawathandiza kuti apitirize kukhala ndi chiyembekezo komanso kudzalandira mphoto yawo.