Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 130

Pilato Anapereka Yesu Ndipo Anthu Anamutenga Kuti Akamuphe

Pilato Anapereka Yesu Ndipo Anthu Anamutenga Kuti Akamuphe

MATEYU 27:31, 32 MALIKO 15:20, 21 LUKA 23:24-31 YOHANE 19:6-17

  • PILATO ANAYESANSO KUMASULA YESU

  • YESU ANAWERUZIDWA NDIPO ANAMUTENGA KUTI AKAMUPHE

Yesu anazunzidwa kwambiri komanso kunyozedwa moti Pilato anayesa kangapo kuti amumasule. Ngakhale kuti Pilato anachita zimenezi, ansembe aakulu komanso otsatira awo sanasinthe maganizo. Iwo ankangofuna kuti Yesu aphedwe basi. Ankangofuula kuti: “M’pachikeni! M’pachikeni!” Koma Pilato anawauza kuti: “M’tengeni mukamupachike nokha, chifukwa ine sindikupeza mlandu uliwonse mwa iye.”—Yohane 19:6.

Ayuda analephera kupereka zifukwa zomveka zomwe zikanachititsa Pilato kuweruza kuti Yesu aphedwe pa mlandu woukira boma, m’malomwake anayambanso kumuimba mlandu wokhudza chipembedzo. Anthuwa anabwerezanso mlandu womwe anamunamizira ku khoti la Sanihedirini uja, woti Yesu ankanyoza Mulungu. Iwo ananena kuti: “Tili ndi chilamulo ife, ndipo malinga ndi chilamulocho iyeyu ayenera kufa, chifukwa akudziyesa mwana wa Mulungu.” (Yohane 19:7) Umenewu unali ngati mlandu winanso watsopano womwe Pilato ankafunika kuweruza.

Pilato anabwerera m’nyumba mwake kuti akaganizirenso zomwe angachite kuti amasule Yesu. Pa nthawiyi Yesu anali atazunzika kwambiri komanso mkazi wa Pilato analota zokhudza Yesu. (Mateyu 27:19) Koma kodi Pilato anaweruza bwanji mlandu winawu womwe Ayuda ankaimba Yesu woti ndi “mwana wa Mulungu”? Pilato ankadziwa kuti Yesu ndi wa ku Galileya. (Luka 23:5-7) Komabe anamufunsa kuti: “Kodi umachokera kuti?” (Yohane 19:9) Mwina Pilato anafunsa Yesu funso limeneli poganiza kuti Yesu anakhalapo ndi moyo kalekale ndiponso kuti mwina anachokera kumwamba.

Pilato anamva Yesu akunena yekha kuti ndi mfumu koma Ufumu wake suli mbali ya dzikoli. Yesu anaona kuti sakufunika kufotokozera Pilato zinthu zambiri zokhudza ufumu zomwe anali atamuuzapo m’mbuyomo, choncho anangokhala chete. Chifukwa chakuti Yesu sanamuyankhe, Pilato anapsa mtima ndipo ananena mokwiya kuti: “Kodi sukundilankhula? Kodi sukudziwa kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula, komanso yokupachika?”—Yohane 19:10.

Koma Yesu anangoyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba. Ndiye chifukwa chake munthu amene wandipereka ine kwa inu ali ndi tchimo lalikulu kwambiri.” (Yohane 19:11) Ponena mawu amenewa, Yesu sankatanthauza kuti ndi munthu mmodzi yekha amene anali ndi mlandu womupereka. Iye ankatanthauza kuti Kayafa, anthu ena omwe ankamuthandiza kuweruza mlanduwu komanso Yudasi Isikariyoti anali ndi mlandu waukulu wopereka Yesu poyerekeza ndi Pilato.

Pilato anayesanso kumasula Yesu chifukwa chakuti anagoma kwambiri ndi zimene Yesuyo analankhula komanso mmene ankaonekera. Iye ankaopanso kuti mwina Yesu akhoza kukhala kuti anachokera kumwamba. Koma Ayuda ananenanso zinthu zina zomwe zinachititsa mantha Pilato. Iwo anamuopseza kuti: “Mukamumasula ameneyu, ndiye kuti si inu bwenzi la Kaisara. Munthu aliyense wodziyesa yekha mfumu, ameneyo ndi wotsutsana ndi Kaisara.”—Yohane 19:12.

Pilato anatulutsanso Yesu panja ndipo iye anakhala pa mpando woweruzira kenako anauza Ayudawo kuti: “Taonani! Mfumu yanu imeneyi!” Koma Ayudawo sanavomereze zimenezo moti anafuula kuti: “Muthane naye! Muthane naye! M’pachikeni!” Pilato anawafunsa kuti: “Kodi ndipachike mfumu yanu?” Ngakhale kuti Ayuda ankadana ndi ulamuliro wa Aroma koma n’zodabwitsa kuti pa nthawiyi, ansembe aakulu ananena molimba mtima kuti: “Tilibe mfumu ina koma Kaisara.”—Yohane 19:14, 15.

Chifukwa cha mantha, Pilato anachita zimene Ayudawo ankafuna. Anapereka Yesu kuti akaphedwe. Asilikali anamuvula chovala chofiira chija n’kumuveka malaya ake akunja. Pamene Yesu ankapita kumene ankati akamuphereko, ananyamula yekha mtengo wake wozunzikirapo.

Pamene asilikali ankamutenga Yesu kuti akamuphe n’kuti kuli chakum’mawa Lachisanu, pa Nisani 14. Yesu ayenera kuti anali atatopa kwambiri chifukwa sanagone kuchokera Lachinayi m’mawa ndipo kungoyambira nthawi imeneyo anakumana ndi mavuto ambiri. Chifukwa chakuti mtengowo unali wolemera kwambiri, Yesu anatopa kwambiri moti sanakwanitsenso kuyenda. Choncho asilikali omwe ankayenda naye anakakamiza munthu wina yemwe ankangodziyendera kuti anyamule mtengowo mpaka kumene ankapita. Munthuyo  anali Simoni wochokera ku Kurene, ku Africa. Anthu ambiri ankatsatira Yesu ndipo ena ankadziguguda chifukwa cha chisoni, pomwe ena ankangolira chifukwa cha zimene zinkachitikazo.

Yesu anauza azimayi ena omwe ankalira kuti: “Ana aakazi a Yerusalemu inu, lekani kundilirira. Koma mudzilirire nokha ndi ana anu. Chifukwa masiku akubwera pamene anthu adzanena kuti, ‘Odala ndi akazi osabereka, amene sanaberekepo, komanso amene mabere awo sanayamwitsepo!’ M’masiku amenewo iwo adzayamba kuuza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’ Pakuti ngati akuchita izi pamene mtengo uli wauwisi, kuli bwanji mtengowo ukadzauma?”—Luka 23:28-31.

Ponena mawu amenewa Yesu ankanena za mtundu wa Ayuda. Anayerekezera mtunduwu ndi mtengo womwe ukuuma koma udakali wauwisi pang’ono. Mtengowo unali udakali wauwisi chifukwa iye anali adakalipo komanso kuti panali Ayuda ena ochepa omwe ankamukhulupirira. Koma nthawi inafika pamene Ayuda okhulupirika anachoka pakati pa mtunduwo ndipo zinali ngati mtengowo wafa chifukwa unangokhala mtundu wakufa mwauzimu. Zinali zomvetsa chisoni pamene asilikali achiroma anabwera n’kudzawononga mtunduwu. Pa nthawiyi zinali ngati kuti Mulungu akugwiritsira ntchito Aromawo kuti alange mtundu wa Ayuda.