Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 6

Zimene Yesu Anachita Kumapeto kwa Utumiki Wake

“Mfumu yako ikubwera kwa iwe.”—Mateyu 21:5

Zimene Yesu Anachita Kumapeto kwa Utumiki Wake

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 101

Yesu Anakadya Chakudya ku Nyumba kwa Simoni ku Betaniya

Mariya, yemwe anali mlongo wake wa Lazaro, anachita zinthu zomwe zinayambitsa mkangano koma Yesu anamuikira kumbuyo.

MUTU 102

Mfumu Inalowa mu Yerusalemu Itakwera pa Bulu

Anakwaniritsa ulosi womwe unanenedwa zaka 500 m’mbuyomo.

MUTU 103

Yesu Anayeretsanso Kachisi

Amalonda a ku Yerusalemu ankaoneka kuti sakuphwanya malamulo pochita malonda awo pakachisi, nanga n’chifukwa chiyani Yesu anawanena kuti ndi achifwamba?

MUTU 104

Kodi Ayuda Anakhulupirira Yesu Atamva Mulungu Akulankhula?

Kodi kukhulupirira Yesu ndi kuchita zinthu zosonyeza kuti umakhulupirira Yesu ndi zinthu ziwiri zosiyana?

MUTU 105

Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za Chikhulupiriro

Yesu anathandiza ophunzira ake kumvetsa zimene munthu angachite ngati ali ndi chikhulupiriro champhamvu komanso anafotokoza chifukwa chimene Mulungu anakanira mtundu wa Isiraeli.

MUTU 106

Mafanizo Awiri Onena za Munda wa Mpesa

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene fanizo la munthu amene anapempha ana ake kuti akagwire ntchito m’munda wake komanso zimene fanizo la munthu amene anasiyira antchito oipa munda wake wampesa limatanthauza.

MUTU 107

Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati

Fanizo limene Yesu ananena linkasonyeza zimene zidzachitike m’tsogolo.

MUTU 108

Yesu Analepheretsa Afarisi Kuti Amugwire

Yesu anasowetsa chonena Afarisi, Asaduki komanso gulu la anthu omwe ankamutsutsa.

MUTU 109

Anadzudzula Atsogoleri Achipembedzo Omwe Ankamutsutsa

N’chifukwa chiyani sanalekere zinthu zolakwika zimene atsogoleri achipembedzo ankachita?

MUTU 110

Tsiku Lomaliza Limene Yesu Anapezeka pa Kachisi

Anawaphunzitsa mfundo yofunika kwambiri pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mkazi wamasiye wosauka.

MUTU 111

Atumwi Anapempha Chizindikiro

Ulosi umene Yesu ananena unakwaniritsidwa koyamba m’nthawi ya atumwi. Kodi n’kutheka kuti ulosiwu udzakwaniritsidwanso m’tsogolo kuposa poyamba paja?

MUTU 112

Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru

Kodi Yesu ankatanthauza kuti hafu ya ophunzira ake ndi opusa ndipo enawo ndi ochenjera?

MUTU 113

Fanizo la Matalente Limatiphunzitsa Kufunika Kochita Zinthu Mwakhama

Fanizo la Yesu limatithandiza kumvetsa mawu akuti: “Amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri.”

MUTU 114

Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo logwira mtima pofuna kutithandiza kudziwa chimene chidzachititse kuti anthu ena aweruzidwe ngati nkhosa, ena ngati mbuzi.

MUTU 115

Yesu Anachita Mwambo Womaliza wa Pasika

N’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo anagwirizana zoti amupatse Yudasi ndalama 30 za siliva kuti amupereke Yesu?

MUTU 116

Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza

Yesu anadabwitsa ophunzira ake chifukwa anagwira ntchito yomwe ankayenera kugwira ndi antchito apakhomo.

MUTU 117

Chakudya Chamadzulo Cha Ambuye

Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake ndipo otsatira ake ayenera kuchita mwambo umenewu chaka chilichonse pa Nisani 14.

MUTU 118

Anakangananso Kuti Wamkulu Ndani

Yesu anali atangowaphunzitsa atumwi za kudzichepetsa koma usiku womwewu iwo sanachedwe kuiwala.

MUTU 119

Yesu Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

Yesu anaphunzitsa mfundo yamphamvu kwambiri ya choonadi yonena za zimene tingachite kuti tifike kwa Mulungu.

MUTU 120

Anali Ngati Nthambi Zobala Zipatso Komanso Anali Mabwenzi a Yesu

Kodi ophuzira a Yesu amabala bwanji zipatso?

MUTU 121

“Limbani Mtima Ndaligonjetsa Dziko”

Kodi Yesu anagonjetsa bwanji dziko popeza anthu a m’dzikoli anamupha?

MUTU 122

Pemphero Lomaliza la Yesu Ali M’chipinda Chapamwamba

Ananena kuti anachita zinthu zina zofunika kwambiri kuposa kuthandiza anthu kuti adzapulumuke.

MUTU 123

Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni Kwambiri

N’chifukwa chiyani Yesu anapemphera kuti, ‘Ndichotsereni kapu iyi’? Kodi ankafuna kuzemba zimene Mulungu anamutumizira padzikoli, zoti adzapereke moyo wake dipo?

MUTU 124

Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa

Yudasi anadziwa kumene Yesu anali ngakhale kuti panali pakati pa usiku.

MUTU 125

Atamugwira Anapita Naye kwa Anasi Kenako kwa Kayafa

Mlandu wa Yesu unaweruzidwa mopanda chilungamo.

MUTU 126

Petulo Anakana Yesu Kunyumba kwa Kayafa

N’chifukwa chiyani Petulo, munthu amene anali ndi chikhulupiriro komanso wodzipereka, anakana Yesu?

MUTU 127

Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa Pilato

Atsogoleri achipembedzo achiyuda anasonyeza kuti anali ndi maganizo olakwika.

MUTU 128

Pilato Komanso Herode Sanamupeze Yesu ndi Mlandu

N’chifukwa chiyani Pilato anatumiza Yesu kuti akaweruzidwe ndi Herode? Kodi Analibe Mphamvu Zoperekera Chilango kwa Yesu?

MUTU 129

Pilato Ananena Kuti: “Taonani! Mwamuna Uja Ndi Uyu!”

Pilato anadziwa kuti Yesu anali ndi makhalidwe abwino.

MUTU 130

Pilato Anapereka Yesu Ndipo Anthu Anamutenga Kuti Akamuphe

N’chifukwa chiyani Yesu anauza amayi omwe anali ndi chisoni kuti adzilirire okha ndi ana awo osati kulirira iyeyo?

MUTU 131

Mfumu Yosalakwa Inavutika Itapachikidwa Pamtengo

Yesu analonjeza chigawenga china kuti chidzakhala naye m’Paradaiso.

MUTU 132

“Ndithudi Munthu Uyu Analidi Mwana wa Mulungu”

Mdima wodabwitsa womwe unagwa masana, chivomerezi champhamvu komanso kung’ambika kwa nsalu, zinasonyeza kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu.

MUTU 133

Anakonza Thupi la Yesu ndi Kukaliika M’manda

N’chifukwa chiyani ankafunika kuika thupi la Yesu m’manda dzuwa lisanalowe?

MUTU 134

M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali Ataukitsidwa

Yesu ataukitsidwa, anaonekera choyamba kwa wophunzira wake wamkazi osati kwa atumwi ake.

MUTU 135

Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu Ambiri

Kodi Yesu akanawatsimikizira bwanji ophunzira ake kuti anali ataukitsidwa?

MUTU 136

Anaonekera M’mbali Mwanyanja ya Galileya

Yesu anafunsa Petulo katatu kuti anene ngati amakondadi Yesuyo.

MUTU 137

Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike

Yesu ataukitsidwa koma asanapite kumwamba, anauza ophunzira ake mobwerezabwereza kuti adzalandira mzimu woyera. Anawauzanso mmene mzimuwo udzawathandizire.

MUTU 138

Khristu Anakhala Kudzanja Lamanja la Mulungu

Kodi Yesu akutani pamene akudikira kugonjetsa adani ake?

MUTU 139

Yesu Adzabweretsa Paradaiso Kenako Adzamaliza Kugwira Ntchito Imene Anapatsidwa

Padakali zambiri zoti Yesu achite asanapereke Ufumu kwa Atate ndi Mulungu wake.