Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 91

Yesu Anaukitsa Lazaro

Yesu Anaukitsa Lazaro

YOHANE 11:38-54

  • LAZARO ANAUKITSIDWA

  • A KHOTI LA SANIHEDIRINI ANAKONZA CHIWEMBU KUTI APHE YESU

Yesu atakumana ndi Marita kenako ndi Mariya chakufupi ndi mudzi wa Betaniya, onse anapita kumanda a Lazaro. Mandawo anali phanga lomwe anatsekapo ndi chimwala. Atafika kumandako Yesu analamula kuti: “Chotsani chimwalachi.” Koma Marita anasonyeza kuti anali ndi nkhawa chifukwa sankadziwa kuti Yesu achita zotani. Iye anauza Yesu kuti: “Ambuye, pano ayenera kuti wayamba kununkha, pakuti lero ndi tsiku lachinayi chimuikireni m’manda.” Koma Yesu anamuuza kuti: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupirira udzaona ulemerero wa Mulungu?”—Yohane 11:39, 40.

Anthu aja atachotsa chimwala chija, Yesu anayang’ana kumwamba n’kuyamba kupemphera kuti: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikunena izi chifukwa cha khamu la anthu aimirira panowa, kuti akhulupirire kuti inu munandituma ine.” Chifukwa choti Yesu anapemphera pagulu, anthu onse anadziwa kuti zimene Yesu ankafuna kuchita azichita ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu. Kenako Yesu anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Pamenepo Lazaro anatuluka manja, mapazi komanso nkhope yake zili zokulunga ndi nsalu zimene ankakulungira maliro. Ndiyeno Yesu ananena kuti: “M’masuleni ndi kumuleka apite.”—Yohane 11:41-44.

Ayuda ambiri amene anabwera kudzapepesa Mariya ndi Marita ataona chozizwitsa chimenechi anakhulupirira Yesu. Koma ena ananyamuka kukauza Afarisi zimene Yesu anachita. Afarisi ndi ansembe aakulu omwe ankapanga khoti lalikulu la Ayuda, lomwe linkadziwikanso ndi dzina lakuti Sanihedirini, anapanga msonkhano. Pa gululo pankakhalanso mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa. Ena mwa oweruzawo anadandaula kuti: “Kodi tichite chiyani pamenepa, chifukwa munthu uyu akuchita zizindikiro zochuluka? Ngati timulekerera, onse adzakhulupirira mwa iye, ndipo Aroma adzabwera kudzatenga malo athu ndi mtundu wathu.” (Yohane 11:47, 48) Ngakhale kuti anthuwa anamva kwa mboni zimene zinaona ndi maso kuti Yesu ‘ankachita zizindikiro zochuluka,’ iwo sanasangalale ndi zimene Mulungu analola kuti Yesu achite. Iwo ankadera nkhawa kwambiri udindo wawo komanso ulemu umene ankapatsidwa.

Asaduki atamva kuti Lazaro waukitsidwa, anakhumudwa kwambiri chifukwa sankakhulupirira kuti akufa adzauka. Kayafa yemwe analinso Msaduki analankhula pa maso pa anthu onsewo kuti: “Palibe chimene mukudziwa inu, ndipo simukuona kuti n’kopindulitsa kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu onse, kuti mtundu wonse usawonongeke.”—Yohane 11:49, 50; Machitidwe 5:17; 23:8.

Kayafa sanalankhule zimenezi “mwa iye yekha.” Mulungu ndi amene anamuchititsa kulankhula zimenezi chifukwa Kayafa anali ndi udindo wapadera. Kayafa ankatanthauza kuti Yesu ankayenera kuphedwa kuti asapitirize kunyozetsa udindo komanso mphamvu zimene atsogoleri achiyuda anali nazo. Komabe zimene Kayafa ananenazi zinali ulosi woti imfa ya Yesu idzapereka mwayi woombola anthu ku uchimo. Imfayi inapereka mwayi osati kwa Ayuda okha komanso kwa anthu ena onse omwe anali ngati “ana a Mulungu obalalika.”—Yohane 11:51, 52.

Oweruza onse a m’khotili anagwirizana ndi maganizo a Kayafa ofuna kupha Yesu. Koma kodi Nikodemo, yemwe anali m’modzi wa oweruza a m’khotili komanso amene ankadziwana ndi Yesu, anauza Yesu zimene khotili linakonza? Kaya zinthu zinayenda bwanji koma Yesu anachoka m’dera limeneli, lomwe linali kufupi ndi Yerusalemu, kuti asaphedwe pa nthawi imene Mulungu anali asanalole.