Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 86

Mwana Wotayika Anabwerera

Mwana Wotayika Anabwerera

LUKA 15:11-32

  • FANIZO LA MWANA WOTAYIKA

Yesu ayenera kuti anali ku Pereya, m’dera la kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano, pamene ankafotokoza fanizo lonena za nkhosa komanso ndalama yotayika. Mafanizo onsewa akutiphunzitsa kuti tiyenera kusangalala munthu wochimwa akalapa n’kubwerera kwa Mulungu. Afarisi ndi alembi ankaimba Yesu mlandu chifukwa choti ankagwirizana ndi anthu ochimwa. Kodi Afarisi ndi alembi anaphunzira kalikonse pa mafanizo amene Yesu ananenawa? Kodi anamvetsa mmene Atate wathu wakumwamba amamvera munthu wochimwa akalapa? Yesu ananenanso fanizo lina pofuna kuwathandiza kumvetsa mfundo yofunika kwambiri ya m’mafanizo amenewa.

Fanizo lake ndi lonena za bambo wina amene anali ndi ana aamuna awiri. M’fanizoli n’zosavuta kuona kuti nkhaniyi imanena kwambiri za mwana wamng’ono. Choncho Afarisi ndi alembi komanso anthu ena amene anamva Yesu akunena fanizoli, ankayenera kuphunzirapo kenakake pa zimene Yesu ananena za mwana wamng’onoyo. Koma ndi bwino kuganiziranso zimene Yesu ananena za bambo komanso mwana wamkulu chifukwa tikhoza kuphunzirapo kanthu pa zimene nawonso anachita. Pamene tikukambirana nkhaniyi mungachite bwino kuganizira zimene tingaphunzire kwa anthu atatuwa.

Yesu anayamba kufotokoza fanizoli kuti: “Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Wamng’ono pa awiriwo anapempha bambo ake kuti, ‘Bambo, mundipatsiretu cholowa changa pa chuma chanuchi.’ Pamenepo bamboyo anagawa chuma chakecho kwa anawo.” (Luka 15:11, 12) M’fanizoli mwanayu ankafuna kuti amugawire chuma chimene ankayenera kudzalandira ngakhale kuti bambo ake anali asanamwalire. Ankafuna kulandira gawo lake nthawi yomweyo kuti azikachita zinthu payekha komanso kuti azikachita zimene akufuna. Kodi ankafuna kuchita chiyani?

Yesu anafotokoza kuti: “Patangopita masiku owerengeka, mwana wamng’ono uja anasonkhanitsa zinthu zonse n’kupita kudziko lina lakutali. Kumeneko anasakaza chuma chake chonse mwa kulowerera m’makhalidwe oipa.” (Luka 15:13) M’malo mokhala pakhomo ndi bambo ake, omwe anali ndi antchito ambiri komanso omwe ankateteza ndi kusamalira ana awo, mwanayo anapita kudziko lina. Ali kumeneko anawononga chuma chake chonse pochita makhalidwe oipa. Ndiyeno Yesu anafotokoza kuti mwanayu anakumana ndi mavuto aakulu. Iye anati:

 “Atawononga zonse, m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu, ndipo iye anayamba kuvutika kwambiri. Moti anapita kukadziphatika kwa nzika ina ya m’dzikolo, ndipo anam’tumiza kubusa kwake kuti azikaweta nkhumba. Iye anafika pomalakalaka chakudya cha nkhumbazo, ndipo palibe amene anali kum’patsa kanthu.”—Luka 15:14-16.

Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti nkhumba zinali zodetsedwa. Koma mwanayu atavutika anayamba kugwira ntchito yoweta nyama zimenezi. Anayamba kuvutika ndi njala moti ankasirira kudya zakudya za nkhumba zomwe ankawetazo. Mwanayu anavutika kwambiri moti anasowa mtengo wogwira koma kenako ‘nzeru zinam’bwerera.’ Kodi anachita chiyani? Anayamba kuganiza kuti: “Komatu aganyu ambiri a bambo ali ndi chakudya chochuluka, koma ine kuno ndikufa ndi njala! Basi ndinyamuka ndizipita kwa bambo anga ndikawauze kuti: “Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu. Sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.”’ Kenako ananyamuka n’kubwerera kwa bambo ake.—Luka 15:17-20.

Kodi bambowo anatani atamuona? Kodi anamukwiyira komanso kumukalipira kuti sanaganize bwino pochoka pakhomopo? Kodi bambowo anamulandira? Kodi mukanakhala inuyo mukanatani? Kodi mukanamva bwanji akanakhala kuti ndi mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi?

MWANA WOTAYIKA ANAPEZEKA

Yesu anafotokoza mmene bamboyo anamvera komanso zimene anachita. Iye anati: “[Mwanayo] ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa chifundo. Pamenepo anamuthamangira ndi kumukumbatira ndipo anamupsompsona mwachikondi.” (Luka 15:20) Ngakhale kuti bambowo  anamva za makhalidwe oipa amene mwana wawo ankachita, anamulandirabe ndi manja awiri. Kodi zimenezi zinathandiza atsogoleri achiyuda, omwe ankanena kuti amalambira komanso kudziwa Yehova, kumvetsa mmene Atate wathu wakumwamba amamvera munthu wochimwa akalapa? Kodi anazindikira kuti Yesu analinso ndi mtima wolandira anthu omwe alapa ngati mmene Atate ake amachitira?

Bamboyo ataona nkhope ya mwana wake anazindikira kuti ankadzimvera chisoni komanso anali atalapa. Chifukwa chakuti bamboyo anamulandira mwachikondi, mwanayo sanavutike kulapa machimo ake. Yesu ananena kuti: “Ndiyeno mwanayo anauza bambo akewo kuti, ‘Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu. Sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.’”—Luka 15:21.

Bamboyo anauza antchito ake kuti: “Fulumirani, tengani mkanjo wabwino kwambiri uja mumuveke! Mumuvekenso mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi kwake. Mubweretse mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa, mumuphe ndipo tidye tisangalale. Chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa koma tsopano wakhalanso ndi moyo, anatayika koma wapezeka.’ Kenako “onse anayamba kukondwerera.”—Luka 15:22-24.

Pamene zimenezi zinkachitika, mwana wamkulu wa bamboyo anali ali kumunda. Pofotokoza za mwanayu Yesu ananena kuti: “Ndiyeno pobwerako, atayandikira kunyumbako, anamva anthu akuimba nyimbo ndi kuvina. Choncho anaitana mmodzi wa antchito ndi kumufunsa chimene chinali kuchitika. Iye anamuuza kuti, ‘Mng’ono wanu wabwera, ndipo bambo anu amuphera mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa, chifukwa amulandira ali bwinobwino.’ Pamenepo iye anakwiya kwambiri moti sanafune n’komwe kulowamo. Kenako bambo akewo anatuluka ndi kuyamba kumuchonderera. Poyankha iye anauza bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ngati kapolo, ndipo sindinaphwanyepo malamulo anu n’kamodzi komwe, koma simunandipatseko ngakhale kamwana ka mbuzi kuti ndisangalale ndi mabwenzi anga. Koma atangofika mwana wanuyu, amene anadya chuma chanu ndi mahule, mwamuphera mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa bwino.’”—Luka 15:25-30.

 Alembi ndi Afarisi anasonyeza khalidwe la ngati la mwana wamkuluyu. Iwo ankamuimba Yesu mlandu chifukwa choti ankacheza komanso kuchitira chifundo anthu wamba komanso anthu ochimwa. Zimenezi n’zimene zinachititsa kuti Yesu anene fanizo limeneli. Choncho munthu aliyense amene amaimba Mulungu mlandu chifukwa chochitira chifundo anthu, ayenera kuphunzirapo kanthu pa fanizo limeneli.

Yesu anamaliza fanizoli pofotokoza zimene bambo uja anauza mwana wake wamkulu n’cholinga choti amvere chisoni m’bale wakeyo. Iye anati: “Mwana wanga, iwe wakhala nane nthawi zonse, ndipo zinthu zonse zimene ine ndili nazo ndi zako. Komatu sitikanachitira mwina, tinayeneradi kusangalala ndi kukondwera, chifukwa m’bale wakoyu anali wakufa koma tsopano ali ndi moyo, anali wotayika koma tsopano wapezeka.”—Luka 15:31, 32.

Yesu sananene kuti mwana wamkulu uja kenako anachita chiyani. Komabe Yesu atafa n’kuukitsidwa “ansembe ambirimbiri anakhala okhulupirira.” (Machitidwe 6:7) Mwina ena mwa ansembewa analipo pamene Yesu ankafotokoza fanizo la mwana wotayika lomwe linali ndi mfundo zamphamvu. Fanizoli linathandiza anthuwo kuzindikira zimene analakwitsa moti analapa ndiponso kubwerera kwa Mulungu.

Kuyambira nthawi imeneyo ophunzira a Yesu ankafunika kuganizira kwambiri mfundo zikuluzikulu komanso zothandiza zomwe zinatchulidwa m’fanizoli. Ifenso tiyenera kuganizira mfundo zimenezi. Mfundo yoyamba imene tikuphunzirapo m’fanizoli ndi yakuti ndi nzeru kukhalabe m’gulu la anthu a Mulungu lomwe ndi lotetezeka kwambiri. Ndi bwino kukhala m’gulu limeneli, lomwe akulisamalira ndi Atate wathu wachikondi amene amatipatsa zinthu zimene timafunika pamoyo wathu, m’malo mopita “kudziko lina la kutali” kukafunafuna zinthu zoipa zimene anthu ambiri amaziona ngati zosangalatsa.

Mfundo ina imene tikuphunzirapo ndi yakuti ngati titayamba kuchoka panjira ya Mulungu tiyenera kudzichepetsa n’kubwerera kwa Atate wathu kuti tikhalenso naye pa ubwenzi wabwino.

Mfundo inanso imene tingaphunzire m’fanizoli ndi kusiyana pakati pa zimene bambo uja anachita ndi zimene mwana wamkulu anachita. Bambo uja anasonyeza mtima wokhululuka komanso anamulandira bwino mwana wotayikayo, pomwe mkulu wake sanamulandire bwino komanso anamukwiyira. Zimenezi zikusonyeza kuti munthu wosochera akalapa n’kubwerera ku nyumba ya Atate, atumiki a Mulungu ayenera kumukhululukira komanso kumulandira ndi manja awiri. Tizisangalala kuti m’bale wathu amene ‘anali wakufa tsopano ali ndi moyo’ komanso amene anali ‘wotayika tsopano wapezeka.’