Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 88

Mmene Zinthu Zinasinthira kwa Munthu Wachuma Komanso kwa Lazaro

Mmene Zinthu Zinasinthira kwa Munthu Wachuma Komanso kwa Lazaro

LUKA 16:14-31

  • FANIZO LA MUNTHU WACHUMA NDI LAZARO

Yesu anali atapereka malangizo othandiza kwambiri ofotokoza mmene ophunzira ake angagwiritsire ntchito chuma. Koma pamene ankapereka malangizo amenewa panalinso Afarisi ndipo iwo ndi amene ankafunika kumvetsera kwambiri malangizo amenewa. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti Afarisi ‘ankakonda kwambiri ndalama.’ Afarisiwo atamva zimene Yesu ananena “anayamba kumunyogodola.”—Luka 15:2; 16:13, 14.

Koma Yesu sanachite mantha ndi zimenezi moti anawauza kuti: “Inu mumadzitcha olungama pamaso pa anthu, koma Mulungu akudziwa mitima yanu. Chifukwa chimene chili chapamwamba kwa anthu n’chonyansa m’maso mwa Mulungu.”—Luka 16:15.

Kwa nthawi yaitali anthu wamba ankaona Afarisi ngati anthu apamwamba koma nthawi yoti zinthu zisinthe inakwana. Anthu amene ankaoneka kuti anali apamwamba chifukwa chakuti anali atsogoleri andale, atsogoleri achipembedzo komanso chifukwa chakuti anali olemera, anatsitsidwa. Pomwe anthu wamba amene ankafuna kuphunzira zinthu zambiri zauzimu anakwezedwa. Zimene Yesu ananena zinasonyezeratu kuti pali kusintha kwakukulu. Iye anati:

“Anthu anali kulalikira Chilamulo ndi Zolemba za aneneri kudzafika m’nthawi ya Yohane. Kuchokera nthawi imeneyo, uthenga wabwino umene ukulengezedwa ndi wokhudza ufumu wa Mulungu, ndipo anthu osiyanasiyana akuyesetsa mwakhama kuti akalowemo. Ndithudi, n’chapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kusiyana n’kuti ngakhale mbali chabe ya chilembo chimodzi cha m’Chilamulo isakwaniritsidwe.” (Luka 3:18; 16:16, 17) Kodi zimene Yesu ananenazi zinasonyeza bwanji kuti panali kusintha kwakukulu?

Atsogoleri achipembedzo achiyuda ankanena monyada kuti amatsatira Chilamulo cha Mose. Mwina mungakumbukire kuti pamene Yesu anachiritsa munthu wakhungu ku Yerusalemu, Afarisi analankhula monyada kuti: “Ifetu ndife ophunzira a Mose. Tikudziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose.” (Yohane 9:13, 28, 29) Chifukwa china chimene Mulungu anaperekera Chilamulo cha Mose chinali choti athandize anthu kudziwa Mesiya, yemwe anali Yesu. Yohane M’batizi ananena kuti Yesu anali Mwanawankhosa wa Mulungu. (Yohane 1:29-34) Kuyambira pa nthawi imene Yohane anayamba utumiki wake, Ayuda odzichepetsa, makamakanso amene anali osauka, anamva za “Ufumu wa Mulungu.” Anthu onse amene ankafuna kudzakhala nzika za Ufumuwu komanso kusangalala ndi madalitso amene Ufumuwu udzabweretse, anamva “uthenga wabwino” umenewu.

Chilamulo cha Mose chinagwiradi ntchito yake. Chinathandiza anthu kuti adziwe Mesiya moti panalibenso chifukwa choti munthu azitsatirabe Chilamulochi. Mwachitsanzo, Chilamulo chinkalola munthu kuthetsa banja pa zifukwa zosiyanasiyana. Koma Yesu anafotokoza kuti “aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo, ndipo wokwatira mkazi wosiyidwayo wachita chigololo.” (Luka 16:18) Zimene Yesu ananenazi zinakwiyitsa kwambiri Afarisi omwe ankakhazikitsa malamulo pa nkhani iliyonse.

Kenako Yesu anafotokoza fanizo lomwe linasonyeza kusintha kwakukulu kumene kunkachitika. Fanizo  lake ndi lonena za anthu awiri omwe zinthu zinasintha mwadzidzidzi pa moyo wawo. Pamene mukuwerenga fanizoli, kumbukirani kuti anthu ena amene ankamvetsera anali Afarisi, omwe ankakonda kwambiri ndalama komanso anthu ankawaona kuti ndi apamwamba.

Yesu ananena kuti: “Munthu winawake anali wolemera, ndipo nthawi zonse anali kuvala zovala zofiirira zapamwamba ndi nsalu zabwino kwambiri. Iye anali kusangalala ndi kudyerera tsiku ndi tsiku. Koma munthu wina wopemphapempha dzina lake Lazaro, anali kumukhazika pachipata cha wachumayo, ali ndi zilonda thupi lonse. Iyeyo ankalakalaka kudya nyenyeswa zakugwa patebulo la wachuma uja. Agalu nawonso anali kubwera kudzanyambita zilonda zakezo.”—Luka 16:19-21.

Afarisi ankakonda kwambiri ndalama, choncho pamene Yesu ananena za munthu “wachuma” ankanena za iwowo. Atsogoleri achipembedzo achiyudawa ankakondanso kuvala zovala zodula komanso zapamwamba. Kuwonjezera pa chuma chomwe anali nacho zikuonekanso kuti ankasangalala ndi udindo wapamwamba komanso zinthu zina zimene ankapeza chifukwa cha udindowo. Choncho powayerekezera ndi munthu amene ankavala zovala zofiirira, Yesu ankasonyeza kuti Afarisi anali ndi udindo wosiririka ndipo nsalu zabwino zoyera kwambiri zinkasonyeza kuti ankadziona kuti ndi anthu olungama.—Danieli 5:7.

Kodi atsogoleri onyada komanso olemerawa ankawaona bwanji anthu wamba komanso osauka? Ankawanyoza kwambiri moti ankawatchula kuti “amuharetsi” kutanthauza kuti eni dziko. Atsogoleriwa ankaona kuti anthu wamba sankadziwa Chilamulo komanso sankayenera kuphunzitsidwa chilamulocho. (Yohane  7:49) Moyo wa “munthu wopemphapempha dzina lake Lazaro” unali wofanana ndi wa anthu wamba. Iye “ankalakalaka kudya nyenyeswa zakugwa patebulo la wachuma uja.” Mofanana ndi Lazaro, amene anali ndi zilonda thupi lonse, anthu wamba ankaoneka kuti ndi osafunika ngati kuti Mulungu sankasangalala nawo.

Kwa nthawi yaitali Afarisi ankanyoza anthu wamba ndipo zimenezi zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Koma Yesu ankadziwa kuti nthawi yoti zinthu zisinthe kwa anthu omwe anali ngati munthu wachuma komanso ngati Lazaro, inali itakwana.

MMENE ZINTHU ZINASINTHIRA KWA MUNTHU WACHUMA KOMANSO KWA LAZARO

Yesu anapitiriza kufotokoza mmene zinthu zinasinthira mwadzidzidzi m’fanizoli. Iye ananena kuti: “Patapita nthawi wopemphapempha uja anamwalira ndipo angelo anamutenga kukamuika pachifuwa cha Abulahamu. Munthu wachuma ujanso anamwalira ndipo anaikidwa m’manda. Ali m’Mandamo anakweza maso ake, ali mkati mozunzika, ndipo anaona Abulahamu kutali, ndipo Lazaro anali pachifuwa chake.”—Luka 16:22, 23.

Anthu amene Yesu ankawafotokozera fanizoli ankadziwa kuti Abulahamu anamwalira kalekale ndipo ali m’Manda. Malemba amanena momveka bwino kuti palibe munthu amene ali m’Manda kapena kuti Sheoli, yemwe akhoza kuona kapena kulankhula. (Mlaliki 9:5, 10) Kodi atsogoleri achipembedzowa ankaganiza kuti Yesu ankatanthauza chiyani ponena fanizoli? Kodi pofotokoza fanizoli Yesu ankasonyeza kuti anthu wamba komanso atsogoleri achipembedzo omwe anali okonda ndalama adzakumana ndi zotani?

Yesu anafotokoza mmene zinthu zinasinthira pamene ananena kuti ‘anthu anali kulalikira Chilamulo ndi Zolemba za aneneri kudzafika m’nthawi ya Yohane. Koma kuchokera nthawi imeneyo, uthenga wabwino umene ukulengezedwa ndi wokhudza ufumu wa Mulungu.’ Choncho ntchito yolalikira imene Yohane komanso Yesu Khristu anagwira ndi imene inachititsa kuti Lazaro komanso munthu wachuma akhale ngati afa ku ntchito zawo zakale kapena kuti moyo wawo wakale, n’kukhalanso ndi moyo watsopano pamaso pa Mulungu.

Kwa nthawi yaitali anthu osauka komanso anthu wamba sankaphunzitsidwa zinthu zauzimu. Koma pa nthawiyi ankasangalala chifukwa chophunzira uthenga wa Ufumu umene poyamba unalalikidwa ndi Yohane M’batizi kenako ndi Yesu ndipo uthengawo unkawathandiza kwambiri. Poyamba zinali ngati kuti anthuwa ‘ankadya nyenyeswa zakugwa patebulo’ la atsogoleri achipembedzo. Koma tsopano anali ndi mwayi wophunzira zinthu zosangalatsa zimene Yesu ankawaphunzitsa zomwe ndi chakudya chenicheni chauzimu. Yehova ankawaona kuti ali ndi udindo wosiririka.

Mosiyana ndi anthu wambawo, atsogoleri achipembedzo omwe anali ngati munthu wolemera uja ankakana kumvetsera uthenga wa Ufumu womwe Yohane komanso Yesu ankalalikira m’madera osiyanasiyana. (Mateyu 3:1, 2; 4:17) Ndipotu uthengawo  unkawakwiyitsa kapena kuwavutitsa mumtima chifukwa unkanena za chiweruzo choopsa chokhala ngati moto, chomwe ankayembekezera kuchokera kwa Mulungu. (Mateyu 3:7-12) Moti atsogoleri achipembedzo okonda ndalamawo akanamva bwino ngati Yesu ndi ophunzira ake akanasiya kulalikira uthenga wochokera kwa Mulungu. Atsogoleriwa anali ngati munthu wolemera wa m’fanizo lija amene ananena kuti: “Atate Abulahamu, ndichitireni chifundo. Mutume Lazaro kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikuzunzika m’moto wolilimawu.”—Luka 16:24.

Koma zimenezi sizinatheke chifukwa atsogoleri achipembedzo ambiri sanasinthe. Iwo anakana ‘kumvera Zolemba za Mose ndi Zolemba za aneneri’ zomwe zikanawathandiza kuvomereza kuti Yesu ndi Mfumu komanso Mesiya amene Mulungu analonjeza. (Luka 16:29, 31; Agalatiya 3:24) Sanadzichepetse kuti avomereze zoti Yesu ndi Mesiya komanso sanakhudzike ataona anthu osauka akuvomereza zoti Yesu ndi Mesiya ndiponso kuti anthuwo anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Ophunzira a Yesu sakanachepetsa mphamvu kapena kupeputsa mfundo zimene ankaphunzitsa kuti angosangalatsa atsogoleri achipembedzo. Mawu amene “Atate Abulahamu” ananena kwa munthu wachuma wa m’fanizo lija, amasonyeza mfundo imeneyi. Iye anati:

“Mwanawe, kumbukira kuti unalandiriratu zabwino zako zonse pamene unali moyo, ndipo Lazaro analandiriratu zinthu zoipa. Koma tsopano akusangalala kuno ndipo iwe ukuzunzika. Komanso, paikidwa phompho lalikulu kwambiri pakati pa ife ndi anthu inu, moti ofuna kuolokera kumeneko kuchokera kuno sangathe. Komanso anthu sangaoloke kuchokera kumeneko kubwera kuno.”—Luka 16:25, 26.

N’zochititsa chidwi kuti kusinthaku kunachitika mwachilungamo ndipo ndi zimene zinkayenera kuchitika. Zinali ngati kuti atsogoleri achipembedzo onyada asinthana malo ndi anthu odzichepetsa omwe anavomereza kunyamula goli la Yesu ndipo ankatsitsimulidwa komanso kudyetsedwa mwauzimu. (Mateyu 11:28-30) Kusintha kumeneku kunaonekera kwambiri patadutsa miyezi yowerengeka pamene pangano la Chilamulo linalowedwa m’malo ndi pangano latsopano. (Yeremiya 31:31-33; Akolose 2:14; Aheberi 8:7-13) Yehova atatsanulira mzimu wake woyera pa Pentekosite wa mu 33 C.E., zinali zoonekeratu kuti ophunzira a Yesu ndi amene ankakondedwa ndi Mulungu kusiyana ndi Afarisi komanso atsogoleri ena achipembedzo.