Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 5

Yesu Anakalalikira Kum’mawa kwa Yorodano Chakumapeto kwa Utumiki Wake

’Anthu ambiri anamukhulupirira.’​—Yohane 10:42

Yesu Anakalalikira Kum’mawa kwa Yorodano Chakumapeto kwa Utumiki Wake

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 82

Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankalalikira ku Pereya

Yesu anauza anthu amene ankamumvetsera kudziwa zoyenera kuchita kuti akapulumuke komanso zimene zidzalepheretse anthu ena kupulumuka. Zimene Yesu ananena zinali zothandiza nthawi imeneyo. Kodi zimene ananenazo ndi zothandizanso masiku ano?

MUTU 83

Kuitanira Anthu ku Chakudya

Yesu atapita kukadya chakudya chamadzulo kunyumba kwa Mfarisi, ananena fanizo la phwando lalikulu la chakudya chamadzulo. Anagwiritsa ntchito fanizoli pophunzitsa mfundo yofunika kwambiri kwa anthu onse a Mulungu. Kodi mfundo yake inali yoti chiyani?

MUTU 84

Kukhala Wophunzira wa Yesu Ndi Udindo Waukulu

Kukhala wophunzira wa Khristu ndi udindo waukulu kwambiri. Yesu anafotokoza zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale wotsatira wake ndipo anthu ena, omwe anadzakhala otsatira ake, anadabwa ndi zimene ananenazo.

MUTU 85

Pamakhala Chisangalalo Munthu Wochimwa Akalapa

Afarisi ndi alembi anadzudzula Yesu chifukwa chochita zinthu ndi anthu. Koma powayankha Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuwathandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera anthu ochimwa.

MUTU 86

Mwana Wotayika Anabwerera

Kodi tikuphunzira chiyani m’fanizo la Yesu la mwana wotayika?

MUTU 87

Muzichita Zinthu Mwanzeru Pokonzekera Zakutsogolo

Yesu ananena fanizo la woyang’anira amene anachita zinthu mwachinyengo pofuna kuphunzitsa mfundo yofunika kwambiri ya choonadi.

MUTU 88

Mmene Zinthu Zinasinthira kwa Munthu Wachuma Komanso kwa Lazaro

Kuti munthu amvetse fanizo la Yesuli ayenera kudziwa kuti anthu a m’fanizoli akuimira ndani.

MUTU 89

Anaphunzitsa ku Pereya Ali pa Ulendo Wopita ku Yudeya

Anafotokoza za khalidwe lomwe lingatithandize kuti tizikhululukira anthu ena ngakhale amene amatilakwira mobwerezabwereza.

MUTU 90

Yesu Ndi “Kuuka ndi Moyo”

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti onse omukhulupirira “sadzafa”?

MUTU 91

Yesu Anaukitsa Lazaro

Panali zinthu ziwiri zimene zinachititsa anthu amene ankatsutsa Yesu kuti alephere kukana zoti Yesu anaukitsa Lazaro.

MUTU 92

Pa Anthu 10 Akhate, Mmodzi Anathokoza Yesu

Munthu amene anachiritsidwa anasonyeza kuti anayamikira Yesu komanso winawake.

MUTU  93

Mwana wa Munthu Adzaonekera

Kodi kukhalapo kwa Khristu kudzaonekera bwanji ngati mphezi?

MUTU 94

Kupemphera Komanso Kudzichepetsa Ndi Zinthu Ziwiri Zofunika Kwambiri

Yesu anaphunzitsa khalidwe lina lofunika kwambiri pamene ananena fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruza woipa.

MUTU 95

Anawafotokozera Chifukwa Chothetsera Banja Komanso Kuti Azikonda Ana

N’chifukwa chiyani Yesu ankaona ana mosiyana kwambiri ndi ophunzira ake?

MUTU 96

Yesu Anayankha Wolamulira Wachinyamata Amene Anali Wolemera

N’chiyani chinachititsa Yesu kunena kuti n’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu?

MUTU 97

Fanizo la Anthu Ogwira Ntchito M’munda wa Mpesa

Kodi oyamba anakhala bwanji omaliza, nanga omaliza anakhala bwanji oyamba?

MUTU 98

Atumwi Anasonyezanso Kuti Ankafuna Udindo Wapamwamba

Yakobo ndi Yohane anapempha kuti akakhale ndi malo apadera kumwamba koma panali atumwi enanso omwe ankafuna malo apaderawa.

MUTU 99

Yesu Anachiritsa Anthu Akhungu Komanso Anathandiza Zakeyu

Kodi tingagwirizanitse bwanji nkhani za m’Baibulo zimene zimaoneka ngati zimatsutsana zomwe zimanena kuti Yesu anachiritsa munthu wakhungu pafupi ndi mzinda wa Yeriko?

CHAPTER 100

Fanizo la Ndalama 10 za Mina

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Aliyense amene ali nazo, adzamuwonjezera zochuluka, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo”?