Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 3

“Woyera, Woyera, Woyera, Yehova”

“Woyera, Woyera, Woyera, Yehova”

1, 2. Kodi mneneri Yesaya anaona masomphenya otani, nanga amatiphunzitsanji za Yehova?

YESAYA ananthunthumira mwaulemu ali ndi mantha aumulungu chifukwa cha zimene anali kuona, masomphenya ochokera kwa Mulungu. Zinali kuoneka ngati zenizenidi! Pambuyo pake iye analemba kuti ‘anaonadi Ambuye’ ali pa mpando Wake wachifumu wokwezeka. Zovala za Yehova zinadzaza mu kachisi wamkulu wa ku Yerusalemu.—Yesaya 6:1, 2.

2 Yesaya ananthunthumiranso mwamantha pomva kuimba kwamphamvu kwambiri komwe kunagwedeza kachisi ndi maziko ake omwe. Nyimboyo anali kuimba ndi aserafi, zolengedwa zauzimu za udindo waukulu kwambiri. Anali kuimba mwamphamvu ndi momveka bwino mawu olemekeza akuti: “Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.” (Yesaya 6:3, 4) Kutchula mawu akuti “woyera” nthaŵi zitatu kunali kuwatsindika mwapadera. Ndipo kunali koyenera kutsindika chomwechi pakuti Yehova ndi woyera kuposa wina aliyense. (Chivumbulutso 4:8) Baibulo limanena mobwerezabwereza za chiyero cha Yehova. Mavesi mazanamazana amanena dzina lake kuti n’loyera.

3. Kodi malingaliro olakwika a chiyero cha Yehova achititsa motani anthu ambiri kutalikirana ndi Mulungu m’malo momuyandikira?

3 Pamenepa, n’zachionekere kuti chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zokhudza Yehova zimene iye amafuna kuti tizidziŵe n’chakuti iye ndi woyera. Komatu, lerolino anthu ambiri sagwirizana nalo lingaliro limeneli. Ena molakwa amati kukamba za chiyero ndiko kuti munthuyo amadziyesa wolungama kapena kuti ndi wopembedza wachinyengo. Anthu amene sadziyesa kukhala ofunikira kwenikweni angaone chiyero cha Mulungu kukhala chochititsa mantha m’malo mokhala chosangalatsa. Angaope kuti sangakhale oyenerera kuyandikira kwa Mulungu woyera ameneyu. Motero, ambiri amatalikirana ndi Mulungu chifukwa cha chiyero chake. Izi n’zomvetsa chisoni chifukwa chiyero cha Mulungu ndicho chifukwa chachikulu chotilimbikitsa  kumuyandikira. Chifukwa chiyani? Tisanayankhe funso limeneli, tiyeni tione kuti chiyero chenicheni n’chiyani.

Kodi Chiyero N’chiyani?

4, 5. (a) Kodi chiyero chimatanthauza chiyani, nanga sichitanthauza chiyani? (b) Kodi Yehova ndi “wopatulika” m’njira zofunika ziŵiri ziti?

4 Pokhala woyera, si kuti Mulungu ndi wodzithemba, wodzikuza, kapenanso kuti amanyansidwa ndi ena. Iye amadana nawo makhalidwe amenewo. (Miyambo 16:5; Yakobo 4:6) Ndiyeno, kodi mawu akuti “woyera” amatanthauza chiyani kwenikweni? M’chinenero cha Chihebri cha m’Baibulo, mawuŵa akuchokera ku mawu otanthauza “patula.” Pa kulambira, “choyera” ndi chinthu chimene achiika padera kuti chisagwire ntchito wambawamba, kapena chimene chikuoneka kukhala chopatulika. Mawu akuti chiyero alinso ndi malingaliro aakulu a kukhala waudongo. Kodi mawu ameneŵa akugwira ntchito motani kwa Yehova? Kodi zikutanthauza kuti ndi “wopatulika” kwa anthu opanda ungwiro, kuti ali nafe patali kwambiri?

5 Ayi, si choncho. Pokhala “Woyera wa Israyeli,” Yehova anadzilongosola kuti anali kukhala “pakati” pa anthu ake, ngakhale kuti iwo anali ochimwa. (Yesaya 12:6; Hoseya 11:9) Motero chiyero chake sichimupangitsa kutalikirana ndi anthu. Nangano ndi “wopatulika” motani? Ndi wopatulika m’njira ziŵiri zofunika kwambiri. Njira yoyamba, iye ndi wopatulika ku chilengedwe chonse pakuti iye yekha ndiye Wam’mwambamwamba. Ndi waudongo kwambiri ndipo udongo wakewo ulibe malire. (Salmo 40:5; 83:18) Njira yachiŵiri n’njakuti Yehova ndi wopatulika kwambiri ku uchimo uliwonsewo, ndipo zimenezi n’zolimbikitsa. Chifukwa chiyani?

6. N’chifukwa chiyani mfundo yakuti Yehova sayandikana n’komwe ndi uchimo ili yotilimbikitsa?

6 Tikukhala m’dziko limene mukusoŵa chiyero chenicheni. Chilichonse chokhudza anthu otalikirana ndi Mulungu n’choipitsidwa mwa njira inayake, n’chodetsedwa ndi uchimo ndi kupanda ungwiro. Tonse timafunika kulimbana ndi uchimo umene tili nawo. Ndipo tonse tikhoza kugonja ku uchimo ngati tikhala osakonzekera. (Aroma 7:15-25; 1 Akorinto 10:12) Yehova sizingamuchitikire zimenezi. Pokhala wosayandikana n’komwe  ndi uchimo, sangaipitsidwe ngakhale ndi uchimo wochepetsetsa. Izi zikutsimikizanso malingaliro akuti Yehova ndiye Atate wabwino kwambiri, chifukwa zimatanthauza kuti ndi wodalirika pa kalikonse. Mosiyana ndi atate ambiri aumunthu ochimwa, Yehova sadzakhala wachinyengo, wosadziletsa, kapenanso wankhanza. Chiyero chake chimachititsa khalidwe lililonse loterolo kukhala losatheka ngakhale pang’ono. Panthaŵi zina Yehova walumbira mwa chiyero chake, ndipo mwa kutero, malumbiro ake akhala odalirika kwambiri. (Amosi 4:2) Kodi zimenezi si zokhazika mtima pansi?

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chiyero ndi umunthu wa Yehova?

7 Chiyero cha Yehova ndiwo umunthu wake weniweniwo. Kodi tikutanthauzanji? Tifanizire motere: Talingalirani mawu akuti “munthu” ndi akuti “kupanda ungwiro.” Simungafotokoze mawu oyambirirawo popanda kuganizira achiŵiriwo. Kupanda ungwiro kumatiloŵerera ndipo kumakhudza chilichonse chimene timachita. Ndiyeno lingalirani mawu ena aŵiri osiyana nawo kwambiri, “Yehova” ndi “chiyero.” Yehova ndi wachiyero paliponsepo. Chilichonse chokhudza iye n’chaudongo, ndi cholungama. Sitingamudziŵe bwino Yehova popanda kumvetsetsa mawu ofunika ameneŵa akuti “woyera.”

“Chiyero N’cha Yehova”

8, 9. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amathandiza anthu opanda ungwiro kukhala oyera pamlingo wocheperapo?

8 Popeza Yehova ndi woyera, tinganene moyenera kuti ndiye gwero la chiyero chilichonse. Sangokhala nalo yekhayekha khalidwe labwinoli; amagaŵira ena mowoloŵa manja. Pamene Mulungu analankhula ndi Mose kupyolera mwa mngelo pa chitsamba choyaka moto, malo ozungulira chitsambacho anakhala oyera chifukwa chakuti Yehova anali kulankhulira pamenepo!—Eksodo 3:5.

9 Kodi anthu opanda ungwiro angakhale oyera mothandizidwa ndi Yehova? Inde angatero mocheperapo. Mulungu anauza anthu ake, Aisrayeli, kuti adzakhala “mtundu wopatulika [“woyera,” NW].” (Eksodo 19:6) Mtunduwo anaupatsa njira ya kalambiridwe imene inali yoyera ndi yaudongo. Motero chiyero ndi nkhani yomwe Chilamulo cha Mose chimaibwerezabwereza.  Ndipotu, mkulu wa ansembe anali kuvala kachitsulo ka golidi pamaso pa nduwira yake, pomwe anthu onse anali kukaona kakunyezimira ndi kuwala. Pa kachitsuloko panalembedwa mawu akuti: “Chiyero n’cha Yehova.” (Eksodo 28:36, NW) Choncho muyezo wapamwamba wa ukhondo ndi udongo unasiyanitsa kulambira kwawo ndiponso moyo wawo. Yehova anawauza kuti: “Muzikhala oyera; pakuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.” (Levitiko 19:2) Malinga ngati Aisrayeli anali kukhala mogwirizana ndi uphungu wa Mulungu monga momwe anthu opanda ungwiro akanathera, iwo mwapang’ono pokha anali oyera.

10. Pankhani ya chiyero, kodi panali kusiyana kotani pakati pa Israyeli wakale ndi mitundu yoyandikana naye?

10 Kunenetsa kotereku kuti Aisrayeli anafunika kukhala oyera kunawasiyanitsa kwambiri ndi kulambira kwa mitundu yowazungulira. Mitundu yachikunjayo inali kulambira milungu yomwe kunena kuti inali yamoyo linali bodza komanso chinyengo, milungu imene amaisonyeza kukhala yachiwawa, yadyera, ndi ya khalidwe lonyansa. Sinali yoyera pa kalikonse. Kulambira milungu yotereyi kunachititsa anthu kuti asakhale oyera. N’chifukwa chake Yehova anachenjeza atumiki ake kuti alekane ndi olambira achikunja limodzi ndi zochita zawo zachipembedzo zoipitsidwazo.—Levitiko 18:24-28; 1 Mafumu 11:1, 2.

11. Kodi ndi motani mmene chiyero cha gulu lakumwamba la Yehova chimaonekera mwa (a) angelo? (b) aserafi? (c) Yesu?

11 Ngakhale pamene Israyeli wakale anali kuchita bwino kwambiri, mtundu wosankhika wa Yehova umenewo unali kungoonetsa pang’ono chabe chiyero cha gulu lakumwamba la Mulungu. Miyandamiyanda ya zolengedwa zauzimu zomwe zimatumikira Mulungu mokhulupirika zimatchedwa kuti “oyera ake zikwi makumi.” (Yuda 14; Deuteronomo 33:2) Zimaonetsa bwino kwambiri kukongola kosangalatsa kwa chiyero cha Mulungu. Ndiponso kumbukirani aserafi amene Yesaya anaona m’masomphenya ake. Mawu a nyimbo yawo akuonetsa kuti zolengedwa zauzimu zamphamvu zimenezi zimachita mbali yofunika kwambiri podziŵitsa chilengedwe chonse za chiyero cha Yehova. Komabe, pali cholengedwa chauzimu china chimene chimaposa zonsezi. Cholengedwachi ndi Mwana wobadwa  yekha wa Mulungu. Yesu ndiye amaonetsa chiyero cha Yehova kuposa wina aliyense. M’poyenera kuti amadziŵika monga “Woyera wa Mulungu.”—Yohane 6:68, 69.

Dzina Loyera, Mzimu Woyera

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani dzina la Mulungu likuyenerera kunenedwa kuti loyera? (b) N’chifukwa chiyani dzina la Mulungu liyenera kuyeretsedwa?

12 Bwanji za dzina lake la Mulungu? Monga tinaonera m’Mutu Woyamba, dzinali si laudindo chabe kapenanso chizindikiro wamba. Limaimira Yehova Mulungu, limodzi ndi makhalidwe ake onse. Motero Baibulo limatiuza kuti ‘dzina lake ndi loyera.’ (Yesaya 57:15) Chilamulo cha Mose chinali kunena kuti aliyense wonyoza dzina la Mulungu anayenera kuphedwa. (Levitiko 24:16) Ndipo taonani chimene Yesu anati chiyenera kukhala choyamba popemphera: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Kuyeretsa chinachake kumatanthauza kuchipanga kukhala chopanda chodetsa. Koma n’chifukwa chiyani chinthu chimene chili kale cha udongo monga dzina la Mulungu chifunikira kuyeretsedwa?

13 Dzina loyera la Mulungu lanyozedwa ndi kuipitsidwa mwa mabodza ndi miseche. Mu Edene, Satana ananamizira Yehova naonetsa kuti Iye ndi Wolamulira wopanda chilungamo. (Genesis 3:1-5) Kuchokera nthaŵi imeneyo, Satana, wolamulira wa dziko lopanda chiyeroli, waonetsetsa kuti pali mabodza ochuluka okhudza Mulungu. (Yohane 8:44; 12:31; Chivumbulutso 12:9) Zipembedzo zasonyeza Mulungu kukhala wosalingalira ena, wosachita chidwi ndi anthu, kapenanso wankhanza. Zanena kuti Mulungu ndiye amazithandiza pankhondo zawo zomwe zapha anthu ambiri. M’malo moyamikira Mulungu pogwira ntchito yochititsa kaso yolenga, anthu kaŵirikaŵiri amati zinthu zinangokhalako zokha, kapena kuti zinachita kusinthika kuchoka ku chinthu china. Ndithudi dzina la Mulungu lasinjiriridwa kwambiri. Liyenera kuyeretsedwa; lifunika kupatsidwanso ulemerero umene liyenera kukhala nawo. Tikulakalaka kwambiri kuona dzina lake litayeretsedwa ndiponso ulamuliro wake utatsimikizidwa. Ndifetu okondwa kuchita kalikonse kamene tingathe pa chifuno chake chachikulu chimenechi.

14. N’chifukwa chiyani mzimu wa Mulungu umatchedwa woyera, nanga n’chifukwa chiyani kuchitira mwano mzimu woyera kuli koopsa kwambiri?

 14 Palinso chinachake chokhudza Yehova kwambiri chomwe pafupifupi nthaŵi zonse chimatchedwa choyera, ndicho mzimu wake, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito. (Genesis 1:2) Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu yoposa china chilichonse imeneyi pokwaniritsa zolinga zake. Chilichonse chimene Mulungu amachita, amachichita mwa njira yoyera ndi yaudongo, motero mphamvu imene amaigwiritsa ntchito ikuyenerera kutchedwa kuti mzimu woyera, kapena mzimu wa chiyero. (Luka 11:13; Aroma 1:4) Kuchitira mwano mzimu woyera, zimene zimaphatikizapo kuchita mwadala zinthu zosemphana ndi zolinga za Yehova, ndi tchimo losakhululukidwa.—Marko 3:29.

Chifukwa Chake Chiyero cha Yehova Chimatiyandikizitsa kwa Iye

15. Kodi n’chifukwa chiyani kukhala ndi mantha aumulungu kuli koyenerera polabadira chiyero cha Yehova, nanga mantha oterowo amaphatikizapo chiyani?

15 Motero m’posavuta kuona chifukwa chomwe Baibulo limanenera kuti chiyero cha Mulungu chimafuna kuti anthu aziopa Mulungu. Mwachitsanzo, Salmo 99:3 limati: “Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa; ili ndilo loyera.” Komabe, mantha ameneŵa si kuti ndi kunjenjemera poopsedwa ndi chinthu chochititsa mantha. Koma ndiwo kuopa kopereka ulemu, kulemekeza kwambiri munthu wina. M’poyenera kumva chonchi, popeza chiyero cha Mulungu n’chotiposa kwambiri. N’chaudongo ndi chaulemerero kwabasi. Ngakhale ndi choncho, sichiyenera kutilepheretsa kumuyandikira. M’malo mwake, kukhala ndi maganizo oyenera a chiyero cha Mulungu kudzatichititsa kumuyandikira. Chifukwa chiyani?

Timatengeka mtima ndi kukongola, tiyeneranso kutengeka ndi chiyero

16. (a) Kodi chiyero chimagwirizanitsidwa motani ndi kukongola? Perekani chitsanzo. (b) Kodi mmene Yehova amamulongosolera m’masomphenya kumatsindika motani udongo wake ndi kuwala kwake?

16 Chifukwa chimodzi n’chakuti Baibulo limagwirizanitsa chiyero ndi kukongola. Pa Yesaya 63:15, kumwamba kunalongosoledwa monga ‘pokhala pa Mulungu poyera ndi pa ulemerero [“pokongola,” NW].’ Timatengeka mtima ndi kukongola. Mwachitsanzo, taonani chithunzi chomwe chili patsamba 33. Kodi  malo amenewo sanakutengeni mtima? Kodi n’chiyani chikuwachititsa kukhala ochititsa kaso chonchi? Taonani mmene madziwo akuonekera aukhondo. Ngakhale mpweya uyenera kukhala kuti ndi wabwino, popeza kulibe mitambo ndipo kukuwala bwino. Tsopano ngati maloŵa atasintha—mu mtsinjewo mutadzala zinyalala, mitengoyo ndi miyalayo italembedwalembedwa mawu achabechabe, mpweya utaipa ndi utsi ndi nkhungu—sangatitengenso mtima; tinganyansidwe nawo. Mwachibadwa, timaona kukongola pamene pali ukhondo ndi kuwala. Tingagwiritse ntchito mawu omweŵa pofotokoza chiyero cha Yehova. N’zosadabwitsa kuti timasangalala ndi mmene Yehova amamulongosolera m’masomphenya! Kung’anipa chifukwa cha kuwala, kunyezimira ngati miyala yamtengo wapatali, kuwalima ngati laŵi la moto kapena ngati miyala ya m’migodi, yopanda kachitsotso kalikonse ndi yonyezimira kwabasi—ndimo mmene kulili kukongola kwa Mulungu wathu woyera.—Ezekieli 1:25-28; Chivumbulutso 4:2, 3.

17, 18. (a) Kodi poyamba Yesaya anamukhudza motani masomphenya ake? (b) Kodi ndi motani mmene Yehova anagwiritsira ntchito mserafi polimbikitsa Yesaya, nanga zimene mserafiyo anachita zinali kutanthauzanji?

17 Komano, kodi chiyero cha Mulungu chiyenera kutichititsa kumva kukhala otsika podziyerekeza ndi iye? Yankho n’lakuti inde. Ndiiko komwe, ndife otsika poyerekeza ndi Yehova; komanso kumeneku n’kuyerekeza zinthu zosagwirizana m’pang’ono pomwe. Kodi tiyenera kutalikirana naye pozindikira zimenezi? Talingalirani zimene anachita Yesaya atamva aserafi akulengeza chiyero cha Yehova. “Ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.” (Yesaya 6:5) Inde, chiyero chopanda malire cha Yehova chinakumbutsa Yesaya kuti anali wochimwa ndi wopanda ungwiro. Poyambirira, mwamuna wokhulupirika ameneyo analefukiratu. Koma Yehova sanamusiye choncho.

18 Nthaŵi yomweyo mserafi anamukhazika mtima pansi mneneriyu. Motani? Mzimu wamphamvuyo unaulukira ku guwa la nsembe n’kutengapo khala la moto, n’kulikhudzitsa pa milomo ya Yesaya. Zimenezi zingamveke kukhala zopweteka kwambiri  m’malo mokhala zolimbikitsa. Komabe kumbukirani kuti aŵa anali masomphenya, amene anali kuphiphiritsa zambiri. Yesaya, Myuda wokhulupirika, anali kudziŵa bwino kuti nsembe zinali kuperekedwa tsiku lililonse pa guwa la nsembe la pa kachisi n’cholinga choteteza machimo. Ndipo mserafiyo anakumbutsa mneneriyu mwachikondi kuti ngakhale analidi wopanda ungwiro, wa “milomo yonyansa,” akanathabe kukhala ndi khalidwe loyera pamaso pa Mulungu. * Yehova anali wofunitsitsa kuona munthu wopanda ungwiro ndi wochimwayu, monga woyera pamlingo wocheperapo.—Yesaya 6:6, 7.

19. Kodi zingatheke bwanji kuti tikhale oyera pamlingo wocheperapo ngakhale kuti ndife opanda ungwiro?

19 Lerolinonso n’chimodzimodzi. Nsembe zonse zimene anali kupereka pa guwa la nsembe ku Yerusalemu zinali chabe kuimira nsembe ina yaikulu, nsembe yangwiro yomwe anapereka Yesu Kristu mu 33 C.E. (Ahebri 9:11-14) Ngati tilapa machimo athu moonadi, nitikonza njira yathu yolakwika, n’kukhulupirira nsembe imeneyo, Mulungu amatikhululukira. (1 Yohane 2:2) Ifenso tikhoza kukhala ndi khalidwe loyera pamaso pa Mulungu. Motero, mtumwi Petro anatikumbutsa kuti: “Kwalembedwa, Muzikhala  oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:16) Taonani kuti Yehova sananene kuti tizikhala oyera mofanana naye. Satiyembekezera kuchita zimene sitingathe. (Salmo 103:13, 14) M’malo mwake, Yehova amatiuza kuti tizikhala oyera chifukwa iye ndi woyera. “Monga ana okondedwa,” timayesetsa kumutsanzira kwambiri mmene tingathere monga anthu opanda ungwiro. (Aefeso 5:1) Choncho munthu safika pamapeto okhala woyera; nthaŵi zonse amafunafunabe chiyero. Pamene tikukula mwauzimu, timakhala tikuyesa “kutsiriza chiyero” tsiku ndi tsiku.—2 Akorinto 7:1.

20. (a) N’chifukwa chiyani kuli kofunika kumvetsetsa kuti tikhoza kukhala audongo m’maso mwa Mulungu wathu woyera? (b) Kodi Yesaya anachitanji atazindikira kuti machimo ake atetezedwa?

20 Yehova amakonda cholungama ndi chosadetsa. Amadana ndi tchimo. (Habakuku 1:13) Koma sadana nafe. Malinga ngati timaona tchimo monga mmene iye amalionera—kudana ndi choipa, kukonda chabwino—ndi kumayesetsa kulondola mapazi angwiro a Kristu Yesu, Yehova amatikhululukira machimo athu. (Amosi 5:15; 1 Petro 2:21) Pamene timvetsetsa kuti tikhoza kukhala audongo m’maso mwa Mulungu wathu woyera, zotsatira zake zimakhala zabwino zedi. Kumbukirani kuti chiyero cha Yehova poyamba chinakumbutsa Yesaya kuti anali wonyansa. Anafuula kuti: “Tsoka kwa ine!” Koma anasintha malingaliro ake atangodziŵa kuti machimo ake anatetezedwa. Pamene Yehova anafunsa munthu yemwe angadzipereke kugwira ntchito ina, Yesaya anavomera mosazengereza, ngakhale kuti sanadziŵe zomwe ntchitoyo ikaphatikizapo. Mofuula anati: “Ndine pano; munditumize ine.”—Yesaya 6:5-8.

21. Kodi n’chiyani chimene chingatipatse chidaliro chakuti tikhoza kukhala oyera?

21 Tinapangidwa m’chifanizo cha Mulungu woyera ndipo anatipatsa makhalidwe abwino ndi luso lomvetsa ndi kuzindikira zinthu zauzimu. (Genesis 1:26) Aliyense wa ife akhoza kukhala woyera. Pamene tikupitiriza kupeza chiyerocho, Yehova amasangalala kutithandiza. Pochita zimenezi tidzayandikira kwa Mulungu wathu woyera. Chinanso n’chakuti, pamene tikuphunzira makhalidwe a Yehova m’mitu yotsatirayi, tidzaona kuti tili ndi zifukwa zomveka zambirimbiri zoti timuyandikirire!

^ ndime 18 Mawu akuti “milomo yonyansa” ndi oyenera, chifukwa Baibulo kaŵirikaŵiri limagwiritsa ntchito milomo mophiphiritsa kuimira mawu kapena chinenero. Mwa anthu onse opanda ungwiro, machimo ochuluka amene timachita amachokera pa kalankhulidwe kathu.—Miyambo 10:19; Yakobo 3:2, 6.