Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 15

Yesu Akhazikitsa Chilungamo M’dziko Lapansi

Yesu Akhazikitsa Chilungamo M’dziko Lapansi

1, 2. Kodi ndi panthaŵi iti pamene Yesu anakalipa, ndipo n’chifukwa chiyani?

YESU anaonekadi kuti wakalipa, ndipo zinali zomveka kuti akalipe. Kungakhale kovuta kulingalira Yesu atakalipa, chifukwatu anali munthu wofatsa zedi. (Mateyu 21:5) Inde, iye sankakwiyakwiya, pakuti mkwiyo wake ndi wolungama. * Koma kodi n’chiyani chinaputa munthu wokonda mtendereyu? Chinali chifukwa choti anthu anachita zinthu zopanda chilungamo m’pang’onong’ono pomwe.

2 Kachisi wa ku Yerusalemu anali malo apamtima kwa Yesu. Padziko lonse lapansi, anali malo okhawo amene anali opatulika omwe anapatulidwa kuti azilambirirapo Atate wake wakumwamba. Ayuda ochokera ku mayiko ambirimbiri anali kuyenda maulendo ataliatali kukalambira kumeneko. Ngakhale anthu oopa Mulungu, omwe sanali Ayuda, ankabweranso ku kachisiyu, ndipo ankakhala m’bwalo la kachisiyu limene analikonza kuti anthu otereŵa azigwiritsa ntchito. Koma koyambirira kwa utumiki wake, Yesu anafika pa kachisi ndipo anapeza kuti pakuchitika zinthu zoipa kwambiri. Malowo analitu ngati pamsika, osadziŵika kuti m’pakachisi. Panadzaza anthu amalonda ndi osinthitsa ndalama. Koma, kodi kupanda chilungamoko kunali pati? Kwa iwo, kachisi wa Mulungu anali chabe malo oti adyerepo anthu masuku pamutu, ngakhale kuwabera kumene. Motani?—Yohane 2:14.

3, 4. Kodi ndi kudyera anthu masuku pamutu kotani kumene kunali kuchitika pa nyumba ya Yehova, ndipo kodi Yesu anachitanji kuti akonze zolakwikazo?

3 Atsogoleri achipembedzo analamula kuti mtundu umodzi wokha wa ndalama ndiwo uzigwira ntchito pokhoma msonkho wa pakachisi. Alendo ankafunika kusinthitsa ndalama zawo kuti apeze ndalama za mtundu umenewo. Choncho osinthitsa ndalama anaika  matebulo awo m’kati mwenimweni mwa kachisiyo, ndipo kuti munthu asinthe ndalama zake anali kumulipiritsa. Nawonso malonda ogulitsa ziŵeto anali opindulitsa kwambiri. Alendo omwe anafuna kupereka nsembe akanatha kugula nyama yoti apereke nsembeyo kwa wogulitsa wina aliyense mu mzindawo. Koma akuluakulu a pakachisi anali kukana nsembe zoterozo, ankati zinali zosayenera. Koma anali kuvomereza zopereka zogulidwa pakachisi pomwepo. Ndiye poti anthuwo sakanachitira mwina koma kugula pakachisipo, nthaŵi zina amalondawo anali kuika mitengo yokwera kwambiri. * Kumeneku sikunali kungodulitsa malonda chabe. Kunali kuba!

“Chotsani izi muno”

4 Yesu sakanalekerera zinthu zopanda chilungamo zoterozo. Imeneyi inali nyumba ya Atate wake! Anapanga mkwapulo wazingwe ndi kutulutsa ng’ombe ndi nkhosa m’kachisimo. Ndiyeno anapita pomwe panali osinthitsa ndalama ndi kugubuduza matebulo awo. Talingalirani ndalama zambirimbiri zikumwazika pansi pomwe anapakonza ndi miyala ya nsangalabwi! Analamula mokalipa amuna amene anali kugulitsa nkhunda kuti: “Chotsani izi muno”! (Yohane 2:15, 16) Zikuoneka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anayerekeza kutsutsa mwamuna wolimba mtima ameneyu.

“Make Mbuu, Mwana Mbuu”

5-7. (a) Kodi kukhalako kwa Yesu asanakhale munthu kunakhudza motani kukonda chilungamo kwake, ndipo tingaphunzirenji pa chitsanzo chake? (b) Kodi Kristu walimbana motani ndi kupanda chilungamo kokhudza ulamuliro wa Yehova ndi dzina Lake?

5 Inde, amalondawo anabweranso. Patapita pafupifupi zaka zitatu, Yesu analimbananso ndi kupanda chilungamo kofananaku; ndipo tsopano anagwira mawu a Yehova mwiniyo otsutsa anthu omwe anapanga nyumba Yake kukhala “phanga la achifwamba.” (Mateyu 21:13; Yeremiya 7:11) Inde, pamene Yesu anaona kuti anthu akudyeredwa masuku pamutu ndiponso kachisi wa Mulungu akuipitsidwa, anamva monga mmene anamvera Atate ake.  Ndipotu n’zosadabwitsa! Yesu anali ataphunzitsidwa ndi Atate wake wakumwamba kwa zaka mamiliyoni osaŵerengeka. Chotsatira chake chinali chakuti anali wokonda chilungamo mofanana ndi Yehova. Anali chitsanzo chenicheni cha mawu akuti, “Make mbuu, mwana mbuu.” Motero ngati tikufuna kukhala ndi chithunzithunzi chabwino cha mmene Yehova alili wachilungamo, njira yabwino ndiyo kulingalira chitsanzo cha Yesu Kristu.—Yohane 14:9, 10.

6 Mwana wobadwa yekha wa Yehova analipo pamene, Satana mopanda chilungamo ananena kuti Yehova Mulungu ndi wabodza, ndipo anatsutsanso zakuti amalamulira molungama. Limenelotu linali bodza lamkunkhuniza! Kenako Mwanayu anamvanso Satana akunena kuti palibe munthu angatumikire Yehova modzipereka chifukwa choti amamukonda. Ndithudi, mabodza ameneŵa anali kumupweteka mumtima Mwana wokonda chilungamoyu. Ayenera kuti anasangalala kwambiri atamva kuti adzakhala ndi mbali yaikulu kwambiri pa kulungamitsa nkhani zabodzazo! (2 Akorinto 1:20) Kodi zimenezi anazichita bwanji?

7 Monga taphunzirira m’Mutu 14, Yesu Kristu anapereka yankho limene linayankha funso lililonse lokhudza zomwe Satana ananena za kukhulupirika kwa zolengedwa za Yehova. Mwakutero, Yesu anayala maziko oti ulamuliro wa Yehova udzatsimikiziridwe komaliza kuti ndi wolungama ndiponso kuti dzina Lake lidzayeretsedwe. Monga “Nthumwi Yaikulu” ya Yehova, Yesu adzakhazikitsa chilungamo cha Mulungu m’chilengedwe chonse. (Machitidwe 5:31, NW) Moyo wake wa padziko lapansi unasonyezanso chilungamo cha Mulungu. Yehova anati za iye: “Pa iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo iye adzalalikira chiweruzo [“chimene chilungamo chili,” NW] kwa akunja.” (Mateyu 12:18) Kodi Yesu anakwaniritsa mawu amenewo motani?

Yesu Azindikiritsa “Chimene Chilungamo Chili”

8-10. (a) Kodi ndi motani mmene malamulo apakamwa a atsogoleri achipembedzo achiyuda anali kulimbikitsira kunyansidwa ndi anthu omwe sanali Ayuda ndiponso akazi? (b) Kodi malamulo apakamwa anasandutsa motani lamulo la Yehova la Sabata kukhala lolemetsa kwambiri?

8 Yesu ankakonda Chilamulo cha Yehova ndipo ankachita zimene chimanena. Koma atsogoleri achipembedzo a m’masiku ake  anapotoza ndi kugwiritsa ntchito molakwa Chilamulocho. Yesu anawauza kuti: ‘Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! . . . Musiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro.’ (Mateyu 23:23) Ndithudi, aphunzitsi a Chilamulo cha Mulungu amenewo sanali kufotokoza bwino “chimene chilungamo chili.” Komano iwo anali kuchititsa chilungamo cha Mulungu kukhala chosadziŵika bwino. Motani? Taonani zitsanzo izi.

9 Yehova analamula anthu ake kusayanjana ndi mitundu yachikunja imene inawazungulira. (1 Mafumu 11:1, 2) Komabe, atsogoleri ena achipembedzo okokomeza zinthu ankalimbikitsa anthu kuti azinyansidwa ndi onse amene sanali Ayuda. M’buku la Mishnah munali ngakhale lamulo ili: “Osasiya ng’ombe pa nyumba ya alendo ya anthu achikunja popeza kuti amaganiziridwa kuti amagona nyama.” Kukhala ndi malingaliro olakwika otereŵa okhudza anthu onse amene sanali Ayuda kunali kosayenera ndi kosemphana zedi ndi mzimu wa Chilamulo cha Mose. (Levitiko 19:34) Malamulo ena amene anthu anapanga anali kupeputsa akazi. Chilamulo cha pakamwa chinali kunena kuti mkazi ayenera kuyenda kumbuyo kwa mwamuna wake, osati pambali pake. Mwamuna anali kuchenjezedwa kuti sayenera kucheza ndi mkazi pagulu, ngakhale mkazi wake weniweniyo. Mofanana ndi akapolo, akazi sanali kuloledwa kupereka umboni m’khoti. Panalinso pemphero lolembedwa limene amuna anali kuthokoza Mulungu kuti anabadwa amuna osati akazi.

10 Atsogoleri achipembedzo anakwirira Chilamulo cha Mulungu mu malamulo ambirimbiri omwe anthu anapanga. Mwachitsanzo, lamulo lonena za Sabata linali kungoletsa kugwira ntchito tsiku la Sabata kuti anthu pa tsikulo azilambira, azitsitsimulidwa mwauzimu, ndi kupumula. Koma Afarisi anapanga lamulo limenelo kukhala lolemetsa kwambiri. Iwo paokha anangodzisankhira kuti n’chiyani kwenikweni chinali “ntchito.” Anatchula zinthu 39 kuti ngati munthu azichita ndiye kuti wagwira ntchito, zinthu monga ngati kukolola kaya kusaka nyama. Izi zinadzutsa mafunso ambirimbiri. Ngati munthu anapha nthata pa Sabata, kodi anali kusaka? Ngati pamene anali kudutsa m’munda anali kubudula ngala za tirigu kuti adye, kodi anali kukolola? Ngati anachiritsa munthu wodwala, kodi anali kugwira ntchito? Mafunso otereŵa anali kuyankhidwa  ndi malamulo osasinthika ndi ofotokozedwa mwatsatanetsatane.

11, 12. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anatsutsa miyambo ya Afarisi yomwe sinali ya m’Malemba?

11 Popeza panali zochitika zoterezi, kodi Yesu akanawathandiza motani anthu kumvetsetsa chimene chilungamo chili? Anawatsutsa molimba mtima atsogoleri achipembedzowo mwa ziphunzitso zake ndiponso mmene anali kukhalira pamoyo wake. Poyamba, taonani zina mwa ziphunzitso zake. Anatsutsa mosapita m’mbali malamulo ambirimbiriwo amene anthu anadzipangira, nati: “Muyesa achabe mawu a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka.”—Marko 7:13.

12 Yesu anaphunzitsa mwamphamvu kuti Afarisi anali kulakwitsa pa lamulo la Sabata, kuti iwo kwenikweni sanamvetsetse cholinga chake cha lamulo limenelo. Anafotokoza kuti Mesiya ndiye “mwini tsiku la Sabata” ndipo motero anali ndi ufulu wochiritsa anthu pa Sabata. (Mateyu 12:8) Pofuna kutsindika mfundo imeneyi, iye ankachiritsa anthu mozizwitsa patsiku la Sabata anthu ena akuona. (Luka 6:7-10) Kuchiritsa koteroko kunapereka chithunzithunzi cha mmene adzachiritsira anthu padziko lonse lapansi m’kati mwa Ulamuliro wake wa Zaka 1,000. Zaka 1,000 zimenezo zidzakhaladi Sabata lalikulu, pamene anthu onse okhulupirika adzathadi kupuma ntchito zimene agwira kwa zaka mazana ambirimbiri akuvutika ndi uchimo ndi imfa.

13. Kodi ndi chilamulo chiti chimene chinakhazikitsidwa chifukwa cha utumiki wa Kristu wa padziko lapansi, nanga chinasiyana bwanji ndi chimene chinalipo kale?

13 Yesu anafotokozanso bwinobwino chimene chilungamo chili mwa njira yakuti atatsiriza utumiki wake wa padziko lapansi, chilamulo chatsopano, “chilamulo cha Kristu,” chinakhazikitsidwa. (Agalatiya 6:2) Mosiyana ndi Chilamulo cha Mose chimene chinali kuloŵedwa m’malo, chilamulo chatsopanochi chinali kwakukulukulu kudalira pa mfundo zachikhalidwe, osati pa mpambo wa malamulo olembedwa. Komabe, chinali ndi malamulo ena achindunji. Limodzi la iwo Yesu analitchula kuti “lamulo latsopano.” Yesu anaphunzitsa otsatira ake onse kuti azikondana monga mmene iye anawakondera. (Yohane 13:34, 35) Inde, chikondi chodzimana chinali kudzazindikiritsa onse okhala mogwirizana ndi “chilamulo cha Kristu.”

 Chitsanzo Chenicheni cha Chilungamo

14, 15. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kuzindikira malire a udindo wake, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zokhazika mtima pansi?

14 Yesu sanangophunzitsa za chikondi, koma anakhala ndi moyo mwa “chilamulo cha Kristu.” Chinali kuonekera m’moyo wake. Taonani njira zitatu izi zimene chitsanzo cha Yesu chinafotokozera bwino chimene chilungamo chili.

15 Yoyamba, Yesu anapeŵa mosamala kwambiri kuchita chinthu chilichonse chosalungama. Mwinamwake mwaona kuti zinthu zambiri zopanda chilungamo zimachitika pamene anthu opanda ungwiro adzikuza ndi kupitirira malire a udindo wawo. Yesu sanachite zimenezo. Tsiku lina munthu wina anafika kwa Yesu, nati: “Mphunzitsi, uzani mbale wanga agaŵane ndi ine chuma chamasiye.” Kodi Yesu anayankhanji? “Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugaŵira inu?” (Luka 12:13, 14) Kodi zimenezi si zodabwitsa? Nzeru za Yesu, kuzindikira kwake zinthu, ndipo ngakhale kukula kwa udindo umene Mulungu anamupatsa, zinaposa za munthu wina aliyense padziko lapansi. Komatu, iye sanafune kuloŵerera pankhani imeneyi chifukwa chakuti sanapatsidwe udindo wochita zimenezo. Mmenemu ndi mmene Yesu nthaŵi zonse wakhala akudziŵira polekezera pa zimene ayenera kuchita, ngakhale kwa zaka zikwizikwi zimene analiko asanakhale munthu. (Yuda 9) Timaona khalidwe lokoma ndi losiririka la Yesu m’mfundo yakuti iye modzichepetsa amadalira Yehova posankha chimene chili cholungama.

16, 17. (a) Kodi Yesu anasonyeza motani chilungamo polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi Yesu anaonetsa motani kuti anali wachifundo pa chilungamo chake?

16 Yachiŵiri, Yesu anasonyeza chilungamo mwa njira imene anali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Sanakondere anthu ena. M’malo mwake anali kuyesetsa kulankhula ndi anthu a mtundu uliwonse, kaya olemera kapena osauka. Koma Afarisi anali kukana anthu wamba osauka powanyoza ndi mawu akuti ʽam-ha·ʼa′rets, kapena kuti “anthu apansi.” Yesu molimba mtima anachita zinthu zosonyeza kuti kumeneku kunali kupanda chilungamo. Pamene anali kuphunzitsa anthu uthenga wabwino—kapenanso pofuna kuwaphunzitsabe, pamene anadya limodzi ndi anthu ena, kuwapatsa zakudya, kuwachiritsa, ngakhalenso kuwaukitsa kwa  akufa—iye anachirikiza chilungamo cha Mulungu amene amafuna kufikira “anthu onse.” *1 Timoteo 2:4.

17 Yachitatu, Yesu anali wachifundo kwambiri pa chilungamo chake. Anali kuyesetsa kwabasi kuthandiza ochimwa. (Mateyu 9:11-13) Anali kuthandiza mofunitsitsa anthu opanda mphamvu zodzitetezera. Mwachitsanzo, Yesu sanagwirizane ndi zonena za atsogoleri achipembedzo zolimbikitsa kusakhulupirira anthu onse amene sanali Ayuda. Ena a iwo anawathandiza mwachifundo ndi kuwaphunzitsa, ngakhale kuti ntchito yake inali kwenikweni kwa anthu achiyuda. Anavomera kuchiritsa mozizwitsa mnyamata wa kapitawo wa asilikali a Roma, nati: “Ngakhale mwa Israyeli, sindinapeza chikhulupiriro chotere.”—Mateyu 8:5-13.

18, 19. (a) Kodi Yesu analimbikitsa motani kulemekeza akazi? (b) Kodi chitsanzo cha Yesu chikutithandiza motani kuona kugwirizana kwa kulimba mtima ndi chilungamo?

18 Mofananamo, Yesu sanagwirizane ndi malingaliro amene anthu panthaŵiyo anali nawo okhudza akazi. Koma iye molimba mtima anachita zolungama. Ayuda anali kukhulupirira kuti akazi achisamariya anali odetsedwa mofanana ndi anthu omwe sanali Ayuda. Koma Yesu sanazengereze kulalikira kwa mkazi wachisamariya pa chitsime cha ku Sukari. Ndipotu, kwa nthaŵi yoyamba, Yesu anadzidziŵikitsa mosapita m’mbali kwa mkazi ameneyu kuti anali Mesiya wolonjezedwayo. (Yohane 4:6, 25, 26) Afarisi anali kunena kuti akazi safunika kuwaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu, koma Yesu anathera nthaŵi yochuluka ndiponso nyonga zake akuphunzitsa akazi. (Luka 10:38-42) Ndipo pamene mwamwambo akazi sanali kuwakhulupirira kuti angapereke umboni wodalirika, Yesu analemekeza akazi angapo powapatsa mwayi wapadera kuti akhale anthu oyamba kumuona ataukitsidwa. Anawauzanso kuti akafotokozere ophunzira ake aamuna za chochitika chofunika kwambiri chimenechi!—Mateyu 28:1-10.

 19 Inde, Yesu anawafotokozera bwino anthu chimene chilungamo chili. Nthaŵi zambiri anali kuchita zimenezi modziika pangozi kwambiri. Chitsanzo cha Yesu chimatithandiza kuona kuti kuchirikiza chilungamo chenicheni kumafuna kulimba mtima. N’koyeneradi kuti anatchedwa “Mkango wochokera m’fuko la Yuda.” (Chivumbulutso 5:5) Kumbukirani kuti mkango ndi chizindikiro cha kulimba mtima posonyeza chilungamo. Komabe posachedwapa, Yesu adzabweretsa chilungamo chachikulu. Iye adzakhazikitsa chilungamo m’dziko lapansi pa chilichonse.—Yesaya 42:4.

Mfumu Yaumesiya Ikhazikitsa Chilungamo M’dziko Lapansi

20, 21. M’nthaŵi yathu ino, kodi Mfumu Yaumesiya yalimbikitsa motani chilungamo m’dziko lonse lapansi ndiponso mu mpingo wachikristu?

20 Kuchokera pamene anakhala Mfumu Yaumesiya mu 1914, Yesu walimbikitsa chilungamo m’dziko lapansi. Motani? Akuonetsetsa kuti ulosi wake wopezeka pa Mateyu 24:14 ukukwaniritsidwa. Otsatira Yesu a padziko lapansi aphunzitsa anthu m’mayiko onse choonadi cha Ufumu wa Yehova. Mofanana ndi Yesu, iwo alalikira mosakondera ndi mwachilungamo. Ayesetsa kuti munthu aliyense—wamng’ono kapena wamkulu, wolemera kapena wosauka, mwamuna kapena mkazi—amupatse mwayi wodziŵa Yehova, Mulungu wa chilungamo.

21 Yesu akulimbikitsanso chilungamo mu mpingo wachikristu, womwe iye ndiye Mutu wake. Monga kunaloseredwa, amapereka “mphatso mwa amuna,” zomwe ndi akulu achikristu okhulupirika amene amatsogolera mu mpingo. (Aefeso 4:8-12, NW) Poŵeta nkhosa za mtengo wapatali za Mulungu, amuna oterowo amatsatira chitsanzo cha Yesu Kristu cha kulimbikitsa chilungamo. Nthaŵi zonse amakumbukira kuti Yesu amafuna kuchitira zinthu nkhosa zake mwachilungamo, mosasamala kanthu za udindo, kutchuka, ngakhalenso chuma cha munthu.

22. Kodi Yehova amamva bwanji ndi kupanda chilungamo kumene kuli ponseponse m’dzikoli lerolino, ndipo kodi wasankha Mwana wake kuti achite chiyani pa zimenezi?

22 Komatu, posachedwapa m’tsogolomu Yesu akhazikitsa chilungamo m’dziko lapansi m’njira yoti sinachitikepo. M’dziko lachinyengoli kupanda chilungamo kuli ponseponse. Mwana aliyense  amene amafa ndi njala amakhala atavutika ndi kupanda chilungamo kwadzaoneni. Izi n’zoona makamaka tikalingalira kuchuluka kwa ndalama ndi nthaŵi zogwiritsidwa ntchito popanga zida za nkhondo ndi pokhutiritsa zokhumba zadyera za anthu okonda kusangalala. Imfa za anthu mamiliyoni ambirimbiri amene amafa mosayenerera chaka chilichonse zili mtundu umodzi chabe mwa mitundu yochuluka ya kupanda chilungamo, ndipotu kupanda chilungamo konseko kumaputa mkwiyo wolungama wa Yehova. Wasankha Mwana wake kuti adzamenye nkhondo yolungama yolimbana ndi dongosolo lonse lilipoli la zinthu zoipa kotero kuti athetseretu kupanda chilungamo konse.—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11-15.

23. Nkhondo ya Armagedo ikadzatha, kodi Kristu adzalimbikitsa chilungamo motani ku nthaŵi zomka muyaya?

23 Komabe, chilungamo cha Yehova chimafuna zambiri osati kungowononga oipa. Wasankhanso Mwana wake kuti alamulire monga “Kalonga wa mtendere.” Nkhondo ya Armagedo ikadzatha, ulamuliro wa Yesu udzakhazikitsa mtendere padziko lonse lapansi, ndipo adzalamulira mwa chilungamo. (Yesaya 9:6, 7) Kenako, Yesu adzasangalala ndi ntchito yothetsa zochitika zonse zopanda chilungamo zimene zachititsa ambiri m’dzikoli kukhala achisoni ndi kuwavutitsa kwambiri. Ku nthaŵi zomka muyaya, iye mokhulupirika adzachirikiza chilungamo chenicheni cha Yehova. Motero n’kofunika kwambiri kuti panopo tiyesetse kutsanzira chilungamo cha Yehova. Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 1 Posonyeza mkwiyo wolungama, Yesu anafanana ndi Yehova, amene ndi “waukali ndithu” pa choipa chilichonse. (Nahumu 1:2) Mwachitsanzo, Yehova atauza anthu ake opulupudza kuti asandutsa nyumba yake kukhala “phanga la okwatula,” kenako anati: “Mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano.”—Yeremiya 7:11, 20.

^ ndime 3 Malinga n’kunena kwa buku lotchedwa Mishnah, patapita zaka zingapo kunachitika chionetsero chotsutsa kukwera mtengo kwa nkhunda zogulitsidwa pa kachisi. Nthaŵi yomweyo mtengowo unatsitsidwa ndi pafupifupi 99 peresenti! Kodi ndani amene anali kudyerera kwambiri pa malonda opezetsa ndalama zambiri ameneŵa? Akatswiri ena a mbiri yakale amati misika ya pakachisi inali ya banja la Mkulu wa Ansembe Anasi, ndipo ndiyo inali gwero lalikulu la chuma chochuluka chimene banja la ansembelo linali nacho.—Yohane 18:13.

^ ndime 16 Afarisi anali kunena kuti anthu osauka, omwe sanali kudziŵa Chilamulo, anali ‘otembereredwa.’ (Yohane 7:49) Anali kunena kuti munthu sayenera kuwaphunzitsa anthu amenewo kaya kuchita nawo malonda kaya kudya nawo ngakhalenso kupemphera nawo. Kulola mwana wako kukwatiwa ndi mwamuna woteroyo ndi chinthu choipa zedi kuposa kumulekerera ku chilombo cham’tchire. Iwo anali kulingalira kuti osaukawo sali m’gulu la anthu odzaukitsidwa.