Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 14

Yehova Alinganiza “Dipo la Anthu Ambiri”

Yehova Alinganiza “Dipo la Anthu Ambiri”

1, 2. Kodi Baibulo limalongosola motani mkhalidwe wa anthu, nanga njira yokha yothetsera zimenezi ndi yotani?

“CHOLENGEDWA chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi.” (Aroma 8:22) Ndi mawu amenewo, mtumwi Paulo analongosola mkhalidwe womvetsa chisoni womwe anthufe tilimo. Malinga n’kuona kwa ife anthu, zimaoneka kuti palibe njira iliyonse yothetsera kuvutika, uchimo, ndi imfa. Koma Yehova sakanika kuchita zinthu zina ngati mmene amakanikira anthu. (Numeri 23:19) Mulungu wa chilungamo watipatsa njira yothetsera mavuto athu. Njirayi imatchedwa kuti dipo.

2 Dipo ndi mphatso yaikulu zedi imene Yehova wapatsa anthu. Tikulanditsidwa ku uchimo ndi imfa chifukwa cha dipoli. (Aefeso 1:7) Ndiwo maziko a chiyembekezo cha moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padziko lapansi la paradaiso. (Luka 23:43; Yohane 3:16; 1 Petro 1:4) Koma kodi dipo n’chiyani kwenikweni? Kodi limatiphunzitsa motani za chilungamo chapamwamba cha Yehova?

Mmene Dipo Linakhalira Lofunika

3. (a) N’chifukwa chiyani dipo linakhala lofunika? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu sanangosintha chilango cha imfa pa ana a Adamu?

3 Dipo linakhala lofunika chifukwa cha tchimo la Adamu. Mwa kusamvera Mulungu, Adamu anapatsa ana ake choloŵa cha kudwala, kukhala achisoni, kumva kupweteka, ndi imfa. (Genesis 2:17; Aroma 8:20) Sizikanatheka kuti Mulungu angowamvera chisoni, ndiyeno n’kusintha chilango chake osawapatsa chilango cha imfa. Akanati achite zimenezi ndiye kuti sakanatsatira lamulo lake lakuti: “Mphoto yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Ndipo ngati Yehova akanathetsa miyezo yake ya chilungamo, m’chilengedwe chonse mukanakhala chipwirikiti chokhachokha ndi kusalamulirika!

4, 5. (a) Kodi Satana ananamizira Mulungu motani, ndipo n’chifukwa chiyani Yehova anaona kukhala kofunika kuyankha mabodza amenewo? (b) Kodi Satana anawaneneza zotani atumiki okhulupirika a Yehova?

 4 Monga taonera m’Mutu 12, kupanduka kumene kunachitika mu Edene kunadzutsa nkhani zina zikuluzikulu. Satana anaipitsa dzina labwino la Mulungu. Iye kwenikweni ananena kuti Yehova ndi wabodza ndiponso ndi wolamulira wopondereza amene sapatsa zolengedwa zake ufulu. (Genesis 3:1-5) Mwa kuoneka ngati walepheretsa cholinga cha Mulungu chodzaza dziko lapansi ndi anthu olungama, Satana anaonetsanso kuti Mulungu saatha kuchita zinthu. (Genesis 1:28; Yesaya 55:10, 11) Ngati Yehova akanati asayankhe zinenezo zimenezi, zolengedwa zake zanzeru zochuluka zikanakhala ndi chidaliro chochepa mu ulamuliro wake.

5 Satana ananamiziranso atumiki okhulupirika a Yehova. Iye anati iwo amakhala ndi zolinga zadyera potumikira Yehova ndipo ngati atati akumane ndi mavuto, palibe amene angakhale wokhulupirika kwa Mulungu. (Yobu 1:9-11) Nkhani zimenezi zinali zofunika kwambiri kuposa mavuto amene anthu anali kudzakumana nawo. Moyenerera, Yehova anaona kuti afunika kuyankha mabodza a Satana. Koma kodi Mulungu akanazithetsa bwanji nkhani zimenezi komanso n’kupulumutsa anthu?

Dipo—Chinthu Chofanana Nacho

6. Kodi ndi mawu ena ati amene agwiritsidwa ntchito m’Baibulo pofotokoza njira ya Mulungu yopulumutsira anthu?

6 Yehova anathetsa nkhanizo mwa njira yachifundo kwambiri ndiponso yachilungamo zedi; njira yomwe palibe munthu aliyense akanailingalira. Komatu, inali njira yosavuta kwambiri. Imanenedwa mosiyanasiyana kuti kuwombola, kuyanjanitsa, ndi kutetezera. (Salmo 49:8; Danieli 9:24; Agalatiya 3:13; Akolose 1:20) Koma mwinamwake mawu amene amafotokoza bwino kwambiri nkhani yonse ndi amene Yesu mwiniyo anawagwiritsa ntchito. Iye anati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo [ly ′tron, m’Chigiriki] la anthu ambiri.”—Mateyu 20:28.

7, 8. (a) Kodi mawu akuti “dipo” amatanthauza chiyani m’Malemba? (b) Kodi dipo limafuna chofanana nacho m’njira yotani?

 7 Kodi dipo n’chiyani? Mawu achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito pa lembali akuchokera ku verebu lotanthauza kuti “kuwonjola, kumasula.” Mawuŵa anali kuwagwiritsa ntchito polongosola ndalama zolipiridwa kuti amasule akaidi ogwidwa pankhondo. Choncho, tingatanthauzire dipo kuti ndi chinthu cholipiridwa pogulanso chinthu china. M’Malemba Achihebri, mawu otanthauza kuti “dipo” (ko′pher) amachokera ku verebu lotanthauza “kuphimba.” Mwachitsanzo, Mulungu anauza Nowa kuti ‘apake’ (mawu amodzimodziwo a kuphimba, m’Chihebri) chingalawa ndi utoto. (Genesis 6:14) Zimenezi zimatithandiza kumvetsetsa kuti kupereka dipo kumatanthauzanso kuphimba, kapena kuti kufafaniza, machimo.—Salmo 65:3.

8 Buku lotchedwa kuti Theological Dictionary of the New Testament limanena kuti mawu ameneŵa (ko′pher) “nthaŵi zonse amatanthauza chofanana nacho,” kapena kuti cholingana nacho. Motero chotetezerapo kapena kuti chophimbira chimene anali kuvundikira pa likasa la chipangano chinapangidwa mofanana ndi likasalo. Mofananamo, popereka dipo chifukwa cha machimo, kapena kuti kuphimba machimo, mtengo wolingana ndendende ndi zowonongedwazo, kapena kuti wophimba zowonongedwa zonsezo bwinobwino, uyenera kulipiridwa. Motero, Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli chinali kunena kuti: “Moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.”—Deuteronomo 19:21.

9. N’chifukwa chiyani amuna okhulupirika anali kupereka nsembe za nyama, ndipo kodi Yehova anaziona motani nsembe zimenezo?

9 Kungoyambira pa Abele, amuna okhulupirika anali kupereka nsembe za nyama kwa Mulungu. Mwa kuchita zimenezi, anasonyeza kuti anali kuzindikira uchimo ndi kufunika kwa kuwomboledwa, ndiponso kuti anali kukhulupirira lonjezo la Mulungu la kumasula anthu mwa “mbewu” yake. (Genesis 3:15; 4:1-4; Levitiko 17:11; Ahebri 11:4)  Yehova anakondwera nazo nsembe zimenezo ndipo olambira ameneŵa anawavomereza kuti anali ndi mbiri yabwino. Komabe, nsembe za nyama zinali chizindikiro chabe. Nyama sizikanaphimba kwenikweni machimo a munthu, chifukwa munthu ndi wamtengo wapatali kuposa nyamazo. (Salmo 8:4-8) Choncho, Baibulo limati: “Sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.” (Ahebri 10:1-4) Nsembe zoterozo zinali kungoimira, kapena kuti kuphiphiritsa, nsembe ya dipo yeniyeni imene inali kubwera.

“Dipo Lolingana”

10. (a) Kodi wopereka dipo anafunika kulingana ndi yani, nanga n’chifukwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani panangofunika nsembe ya munthu mmodzi yekha?

10 “Mwa Adamu onse amwalira,” anatero mtumwi Paulo. (1 Akorinto 15:22) Motero dipo linafuna kuti pafe munthu wofanana ndendende ndi Adamu, munthu wangwiro. (Aroma 5:14) Palibe cholengedwa cha mtundu wina uliwonse chimene chikanakwaniritsa chilungamo. Ndi munthu wangwiro yekha, munthu amene sanayenere kulandira chilango cha imfa choperekedwa kwa Adamu, amene akanapereka “dipo lolingana”—lolingana ndendende ndi Adamu. (1 Timoteo 2:6, NW) Sikunali kofunika kuti anthu mamiliyoni ambirimbiri aperekedwe nsembe kuti afanane ndi mbadwa zonse za Adamu. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: ‘Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo.’ (Aroma 5:12) Ndipo “monga imfa inadza mwa munthu,” Mulungu anakonza zoti anthu awomboledwe kudzera “mwa munthu.” (1 Akorinto 15:21) Anazichita motani?

“Dipo lolingana kwa onse”

11. (a) Kodi wopereka dipo ‘analaŵa imfa m’malo mwa munthu aliyense’ motani? (b) N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava ali osayenera kuwalipirira dipo? (Onani mawu a m’munsi.)

11 Yehova anakonza zoti munthu wangwiro apereke nsembe moyo wake modzifunira. Malinga n’kunena kwa Aroma 6:23, “mphoto yake ya uchimo ndi imfa.” Mwa kupereka nsembe moyo wake, wopereka dipoyo ‘analaŵa imfa m’malo mwa munthu aliyense.’ M’mawu ena tinganene kuti iye analipira mphoto ya tchimo la Adamu. (Ahebri 2:9; 2 Akorinto 5:21; 1 Petro  2:24) Zimenezi zinakhudza kwambiri malamulo. Mwa kuthetsa chilango cha imfa pa ana omvera a Adamu, ndiye kuti dipo linachotsa mphamvu yowononga ya uchimo pa gwero lake lenilenilo. *Aroma 5:16.

12. Perekani fanizo losonyeza kuti kulipira ngongole imodzi kukhoza kupindulitsa anthu ambirimbiri.

12 Tifanizire motere: Yerekezani kuti mukukhala m’tauni mmene anthu ambiri amagwira ntchito pa fakitale inayake yaikulu. Inuyo limodzi ndi anthu ena amene mwayandikana nawo mumalandira ndalama zochuluka pa ntchito yanu ndipo mumadya bwino. Zili choncho mpaka tsiku limene fakitaleyo ikutsekedwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti woyang’anira wamkulu pa fakitaleyo anayamba zakatangale, ndiye wawononga ndalama moti fakitaleyo singathenso kubweza ngongole. Mosayembekezeka mwakhala malova, ndipo inu ndi anzanu ena mukulephera kulipira ngongole zanu. Mabanja anu, ndiponso okongoletsa ndalama nonse mukuvutika chifukwa cha katangale wa munthu mmodzi. Kodi pali njira yothetsera mavutoŵa? Inde! Mpondamatiki wina waganiza zogwapo pa nkhaniyo. Akuzindikira kuti kampaniyo ndi yaphindu. Akumveranso chifundo anthu ambirimbiri ogwira ntchito pakampaniyo limodzi ndi mabanja awo. Motero wakonza zobweza ngongole ya kampaniyo ndi kutsegulanso fakitaleyo. Kulipira ngongole imodzi imeneyo kukupatsa mpumulo antchito ambirimbiriwo ndi mabanja awo ndiponso amene anawakongoza ndalamawo. Mofananamo, kulipira ngongole ya Adamu kukupindulitsa anthu mamiliyoni ochuluka.

Kodi Ndani Akulinganiza Dipo?

13, 14. (a) Kodi Yehova analinganizira anthu dipo motani? (b) Kodi dipo linalipiridwa kwa yani, ndipo n’chifukwa chiyani kulipira kumeneko kuli kofunika?

13 Ndi Yehova yekha yemwe akanapereka “Mwanawankhosa  . . . amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi.” (Yohane 1:29) Koma Mulungu sanangotuma mngelo wina aliyense kuti adzapulumutse anthu. Koma anatuma Amene akanayankha zomwe Satana ananeneza atumiki a Yehova mosasiyako funso lililonse. Inde, Yehova anadzipereka kwambiri mwa kutumiza Mwana wake wobadwa yekha, Mwana yemwe anali ‘kumusekeretsa.’ (Miyambo 8:30) Mwana wa Mulungu mofunitsitsa ‘anakhuthula’ chikhalidwe chake chakumwamba. (Afilipi 2:7) Yehova anasamutsa mozizwitsa moyo ndi umunthu wa Mwana wake wakumwamba woyamba kubadwa ndi kuuika m’mimba mwa namwali wachiyuda, wotchedwa Mariya. (Luka 1:27, 35) Monga munthu, dzina lake anatchedwa Yesu. Koma mwalamulo, anatchedwa kuti Adamu wachiŵiri, chifukwa analinganadi ndendende ndi Adamu. (1 Akorinto 15:45, 47) Motero, Yesu anatha kudzipereka nsembe monga dipo la anthu ochimwa.

14 Kodi dipolo linalipiridwa kwa yani? Salmo 49:7 limanena mosapita m’mbali kuti dipo linaperekedwa “kwa Mulungu.” Koma kodi si Yehova yemwe analinganiza kuti pakhale dipo? Inde, koma zimenezi sizichepetsa kufunika kwa dipo monga ngati ndi kusinthanitsa zinthu kopanda tanthauzo ndi kosalingalira; ngati kuti mwangotulutsa ndalama m’thumba lina ndi kuziika m’thumba linanso. Tiyenera kumvetsetsa kuti dipo si kusinthanitsa zinthu zakuthupi, koma kuti ndi nkhani ya malamulo. Mwa kukonza kuti dipo lilipiridwe, ngakhale kuti zinamutengera zinthu zochuluka kwambiri, Yehova anasonyeza kuti amamamatira mosasintha ku chilungamo chake changwiro.—Genesis 22:7, 8, 11-13; Ahebri 11:17; Yakobo 1:17.

15. N’chifukwa chiyani kunali kofunika kuti Yesu avutike ndi kufa?

15 Mu ngululu ya chaka cha 33 C.E., modzifunira, Yesu Kristu analola kuzunzika kwambiri zomwe zinachititsa kuti dipo lilipiridwe. Analolera kumangidwa pa milandu yabodza, kuweruzidwa kuti anali ndi mlandu, ndi kukhomeredwa pa mtengo wophera anthu. Kodi kunalidi kofunikira kuti Yesu avutike chomwechi? Inde, kunali kofunikira, chifukwa nkhani ya kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu inafunika kuthetsedwa. N’zochititsa chidwi kuti Mulungu sanalole kuti Yesu aphedwe ali wakhanda ndi Herode. (Mateyu 2:13-18) Koma pamene Yesu  anali munthu wamkulu, anatha kupirira zonse zimene Satana anali kumuvutitsa nazo, akudziŵa bwino lomwe nkhani zomwe zinali kuphatikizidwa. * Mwa kukhalabe “woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa” ngakhale pozunzidwa mwakhanza, Yesu anasonyeza mosasiya chikayikiro chilichonse kuti Yehova ali ndi atumiki amene amakhalabe okhulupirika pokumana ndi ziyeso. (Ahebri 7:26) Choncho ndi zomveka kuti atatsala pang’ono kufa, Yesu anafuula mawu amene anasonyeza kuti anachita zonse bwino lomwe, akuti: Kwatha.”—Yohane 19:30.

Kutsiriza Ntchito Yake Yowombola Anthu

16, 17. (a) Kodi Yesu anapitiriza motani ntchito yake yowombola anthu? (b) N’chifukwa chiyani kunali kofunika kuti Yesu akaonekere “pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife”?

16 Komabe Yesu anafunika kutsiriza ntchito yake yowombola anthu. Patapita masiku atatu Yesu atafa, Yehova anamuukitsa. (Machitidwe 3:15; 10:40) Mwa chochitika chosaiwalika chimenechi, Yehova sanangofupa Mwana wake chifukwa cha utumiki wake wokhulupirika, komanso anamupatsa mpata wotsiriza ntchito yake yowombola anthu monga Mkulu wa Ansembe wa Mulungu. (Aroma 1:4; 1 Akorinto 15:3-8) Mtumwi Paulo analongosola kuti: ‘Atafika Kristu, Mkulu wa ansembe . . . , osati mwa mwazi wa mbuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analoŵa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo chiwombolo chosatha. Pakuti Kristu sanaloŵa m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m’Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.’—Ahebri 9:11, 12, 24.

17 Kristu sakanatenga mwazi wake weniweni kupita nawo  kumwamba. (1 Akorinto 15:50) Koma anatenga chimene mwaziwo unaimira: mtengo walamulo wa moyo wake wangwiro waumunthu umene anaupereka nsembe. Ndiyeno, ali pamaso pa Mulungu, anapereka mtengo wa moyowo monga dipo posinthanitsa ndi anthu ochimwa. Kodi Yehova analandira nsembeyo? Inde, ndipo zimenezi zinaonekera pa Pentekoste wa mu 33 C.E., pamene mzimu woyera unatsanulidwa pa ophunzira pafupifupi 120 ku Yerusalemu. (Machitidwe 2:1-4) Ngakhale kuti chochitika chimenecho chinali chosangalatsa kwambiri, dipo panthaŵi imeneyo linali kuyamba kumene kupereka mapindu ake ochititsa kaso zedi.

Mapindu a Dipo

18, 19. (a) Kodi ndi magulu aŵiri ati a anthu amene akupindula ndi kuyanjanitsidwa kumene kwatheka chifukwa cha mwazi wa Kristu? (b) Kwa awo a “khamu lalikulu,” kodi ena a mapindu a dipo amene akupeza tsopano lino ndiponso amene adzapeza m’tsogolo ndi ati?

18 M’kalata yomwe analembera Akolose, Paulo analongosola kuti kunamukomera Mulungu kuti kupyolera mwa Kristu ayanjanitse zinthu zonse kwa Iye mwini atachita mtendere mwa mwazi umene Yesu anakhetsa pa mtengo wozunzirapo. Paulo analongosolanso kuti kuyanjanitsa kumeneku kukukhudza magulu aŵiri a anthu, omwe ndi “za m’mwamba” ndi “za padziko.” (Akolose 1:19, 20; Aefeso 1:10) Gulu loyambalo lili ndi Akristu okwanira 144,000 amene apatsidwa chiyembekezo chokatumikira monga ansembe akumwamba ndi kulamulira monga mafumu pa dziko lapansi limodzi ndi Kristu Yesu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 7:4; 14:1-3) Kupyolera mwa iwoŵa, mapindu a dipo adzaperekedwa pang’onopang’ono kwa anthu omvera kwa zaka 1,000.—1 Akorinto 15:24-26; Chivumbulutso 20:6; 21:3, 4.

19 Zinthu “za padziko” ndi anthu amene akuyembekeza kudzakhala ndi moyo wangwiro m’Paradaiso padziko lapansi. Pa Chivumbulutso 7:9-17 iwo akufotokozedwa kuti ali “khamu lalikulu” limene lidzapulumuka “chisautso chachikulu” chimene chikubwera. Komatu safunika kudikira mpaka nthaŵi imeneyo kuti adzasangalale ndi mapindu a dipo. Iwo “anatsuka [kale] zovala  zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” Popeza kuti amakhulupirira dipolo, ngakhale pakali pano, akupeza mapindu auzimu kuchokera ku makonzedwe achikondi ameneŵa. Anenedwa kuti ndi olungama pokhala mabwenzi a Mulungu! (Yakobo 2:23) Chifukwa cha nsembe ya Yesu, ‘angalimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo.’ (Ahebri 4:14-16) Pamene alakwa, machimo awo amakhululukidwadi. (Aefeso 1:7) Ngakhale kuti ndi opanda ungwiro, iwo ali ndi chikumbumtima choyera. (Ahebri 9:9; 10:22; 1 Petro 3:21) Motero sitingayembekeze kuti anthu adzayanjanitsidwa ndi Mulungu m’tsogolo, akuyanjanitsidwa lerolino! (2 Akorinto 5:19, 20) M’kati mwa Zaka 1,000, iwo pang’onopang’ono ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi’ ndipo pomalizira pake ‘adzaloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:21.

20. Kodi inu panokha mumakhudzidwa motani posinkhasinkha za dipo?

20 ‘Tiyamika Mulungu mwa Yesu Kristu’ potipatsa dipo! (Aroma 7:25) Linaperekedwa m’njira yosavuta, komatu limatikhudza kwambiri moti timakhala aulemu ndi amantha kwa Mulungu. (Aroma 11:33) Ndipo pamene tisinkhasinkha za dipo moyamikira, limakhudza mitima yathu ndi kutiyandikizitsa kwa Mulungu wa chilungamo nthaŵi zonse. Mofanana ndi wamasalmo, tili ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova monga ‘wokonda chilungamo ndi chiweruzo.’—Salmo 33:5.

^ ndime 11 Adamu ndi Hava ndi osayenera kuwalipirira dipo. Chilamulo cha Mose chinafotokoza mfundo yachikhalidwe iyi yokhudza wakupha munthu mwadala: “Musamalandira dipo la kuwombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa.” (Numeri 35:31) Mwachionekere, Adamu ndi Hava anali ofunika kufa chifukwa sanamvere Mulungu mwa kufuna kwawo ndiponso ankadziŵa zomwe akuchita. Mwa kutero iwo anataya chiyembekezo cha moyo wosatha.

^ ndime 15 Yesu anafunika kufa, osati monga mwana wangwiro, koma monga munthu wamkulu wangwiro kuti zilingane ndi tchimo la Adamu. Kumbukirani kuti Adamu anachimwa mwadala; anali kudziŵa bwino lomwe kuopsa kwa zimene anali kuchitazo ndiponso zotsatirapo zake. Choncho kuti Yesu akhale “Adamu wotsirizayo” ndi kuphimba tchimo limenelo, anafunika kusankha kukhala wokhulupirika kwa Yehova ali wamkulu ndiponso akudziŵa chimene akuchita. (1 Akorinto 15:45, 47) Motero moyo wonse wokhulupirika wa Yesu, kuphatikizapo imfa yake yansembe, unakhala “chilungamitso chimodzi.”—Aroma 5:18, 19.