Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 16

‘Chitani Cholungama’ Poyenda ndi Mulungu

‘Chitani Cholungama’ Poyenda ndi Mulungu

1-3. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kumuchitira chinachake Yehova? (b) Kodi n’chiyani chimene Wotipulumutsa wathu wachikondi amafuna kwa ife?

TAYEREKEZANI kuti muli m’sitima yapamadzi yomwe ikumira, ndipo mukusoŵa chochita. Ndiye pamene mukuganiza kuti palibenso zopulumuka, pakufika munthu kudzakupulumutsani nakukokerani kumalo abwino. Mukumvatu kukhala womasuka kwambiri pamene wokupulumutsaniyo akupita nanu kutali ndi ngoziyo nanena kuti: “Muli pabwino tsopano”! Kodi simungamve kuti mufunika kumuchitira chinachake munthu ameneyo? Ndithudi, muli moyo chifukwa cha iye.

2 M’mbali zina, zimenezi zikufanana ndi zimene Yehova watichitira. Ndithudi tifunika kumuchitira chinachake. Ndi iko komwe, iye analinganiza dipo lomwe lapangitsa kukhala kotheka kuti tilanditsidwe ku mphamvu ya uchimo ndi imfa. Timamva kukhala osungika podziŵa kuti malinga ngati tikukhulupirira nsembe yamtengo wapatali imeneyo, machimo athu amakhululukidwa, ndipo n’zotsimikizika kuti tili ndi tsogolo losatha. (1 Yohane 1:7; 4:9) Monga tinaonera m’Mutu 14, dipo ndi njira yapamwamba kwambiri imene Yehova anasonyezera chikondi chake ndi chilungamo chake. Kodi tiyenera kuchitanji?

3 Kuli koyenera kulingalira zimene Wotipulumutsa wathu wachikondi mwiniyo amafuna kwa ife. Mwa mneneri Mika, Yehova anati: “Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” (Mika 6:8) Taonani kuti chimodzi mwa zinthu zimene Yehova amafuna kwa ife ndi chakuti ‘tichite cholungama.’ Kodi tingazichite bwanji zimenezi?

Kutsata “Chilungamo Chenicheni”

4. Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amayembekezera kuti tizitsatira miyezo yake yolungama?

4 Yehova amatiyembekezera kutsatira miyezo yake ya chabwino  ndi choipa. Popeza kuti miyezo yake ndi yolungama, timatsata chilungamo pamene tiitsatira. Yesaya 1:17 amati: “Phunzirani kuchita zabwino, funani chiweruzo.” Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ‘kufunafuna chilungamo.’ (Zefaniya 2:3) Amatilimbikitsanso “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwa chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni.” (Aefeso 4:24, NW) Chilungamo chenicheni—chiweruzo chenicheni—sichilola chiwawa chidetso kapena khalidwe loipa, pakuti zimenezi zimaipitsa chinthu choyera.—Salmo 11:5; Aefeso 5:3-5.

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani kutsatira miyezo ya Yehova si kolemetsa kwa ife? (b) Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti kutsata chilungamo kumachitikabe nthaŵi zonse?

5 Kodi ndi zolemetsa kwa ife kutsatira miyezo yolungama ya Yehova? Ayi. Munthu amene waika mtima wake pa Yehova saona zimene Iye amafuna kukhala zolemetsa. Chifukwa chakuti timamukonda Mulungu wathu ndi makhalidwe ake onse, timafuna kukhala ndi moyo m’njira yomukondweretsa. (1 Yohane 5:3) Kumbukirani kuti Yehova ‘amakonda zolungama.’ (Salmo 11:7) Ngati tikufuna kutsanziradi chilungamo cha Mulungu, tiyenera kukulitsa kukonda zimene Yehova amakonda ndi kudana ndi zimene iye amadana nazo.—Salmo 97:10.

6 Kutsata chilungamo n’kovuta kwa anthu opanda ungwiro. Tiyenera kuvula umunthu wakale ndi makhalidwe ake auchimo ndi kuvala watsopano. Baibulo limanena kuti umunthu watsopano ‘uli kukonzeka watsopano’ ndi chidziŵitso cholondola. (Akolose 3:9, 10) Mawu akuti “uli kukonzeka watsopano” akusonyeza kuti kuvala umunthu watsopano kumachitikabe nthaŵi zonse, ndi kuti kumafuna khama lalikulu. Ngakhale tiyesetse bwanji kuchita cholungama, pali nthaŵi zina pamene chibadwa chathu chauchimo chimatikhumudwitsa polingalira, polankhula, kapena pochita zinthu.—Aroma 7:14-20; Yakobo 3:2.

7. Kodi zinthu zotibwezera m’mbuyo tiyenera kuziona motani pamene tikuyesetsa kutsata chilungamo?

7 Kodi zinthu zotibwezera m’mbuyo pamene tikuyesetsa kutsata chilungamo tiyenera kuziona motani? Zoonadi,  sitifunika kuchepetsa kuopsa kwa tchimo. Komanso sitiyenera kungosiyiratu, tikumalingalira kuti ndife osayenera kutumikira Yehova popeza tikulephera kuchita zofuna zake. Mulungu wathu wokoma mtima wakonza njira yoti anthu olapa moona mtima azitha kukhalanso naye paubwenzi. Taonani mawu okhazika mtima pansi aŵa a mtumwi Yohane: “Izi ndikulemberani, kuti musachimwe.” Komano anawonjezerapo mozindikira bwino kuti: “Ndipo akachimwa wina [chifukwa cha kupanda ungwiro kobadwa nako], Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu.” (1 Yohane 2:1) Inde, Yehova analinganiza nsembe ya dipo ya Yesu kuti tithe kumutumikira movomerezeka ngakhale kuti ndife ochimwa. Kodi zimenezi sizitilimbikitsa kufuna kuchita zonse zimene tingathe kuti tisangalatse Yehova?

Kugwirizana kwa Uthenga Wabwino ndi Chilungamo cha Mulungu

8, 9. Kodi kulengeza uthenga wabwino kumasonyeza motani chilungamo cha Yehova?

8 Tingasonyeze chilungamo—kutsanzira chilungamo cha Mulungu—mwa kulalikira kwa ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chilungamo cha Yehova ndi uthenga wabwino?

9 Yehova sadzathetsa dongosolo loipali popanda kupereka chenjezo choyamba. Mu ulosi wake wonena za zimene zidzachitika m’nthaŵi ya mapeto, Yesu anati: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10; Mateyu 24:3) Kugwiritsa ntchito mawu akuti “uyambe” kukutanthauza kuti zochitika zina zidzachitika ntchito yolalikira padziko lonse itachitika. Zochitika zimenezi zikuphatikizapo chisautso chachikulu chomwe chinanenedweratu, chimene chidzawononga oipa ndi kukonza njira ya dziko latsopano lolungama. (Mateyu 24:14, 21, 22) Ndithudi, lidzakhala bodza kunena kuti Yehova sanachitire chilungamo anthu oipa. Mwa kupereka chenjezo, anthu oterowo akuwapatsa mpata wokwanira wosintha njira zawo kuti asadzawonongedwe.—Yona 3:1-10.

Timasonyeza chilungamo cha Mulungu pamene mosakondera tiuza ena uthenga wabwino

10, 11. Kodi pamene tilalikira nawo uthenga wabwino timasonyeza chilungamo cha Mulungu motani?

 10 Kodi ifeyo tikamalalikira uthenga wabwino timasonyeza chilungamo cha Mulungu motani? Choyamba, n’koyenera kuti tichite zimene tingathe pothandiza ena kupulumuka. Lingaliraninso fanizo lija lopulumutsidwa m’sitima yapamadzi imene ikumira. Pokhala kuti inuyo tsopano muli osungika m’bwato la opulumutsa, ndithudi mungafune kuthandiza ena amene adakali m’madzimo. Mofananamo, tili ndi udindo kwa anthu amene adakali kuvutika “m’madzi” a dziko loipali. N’zoona kuti ambiri amakana uthenga wathu. Koma malinga ngati Yehova akhalabe woleza mtima, tili ndi udindo wowapatsa mwayi kuti “afike kukulapa” ndipo motero n’kukhala pa mzere wokapulumuka.—2 Petro 3:9.

11 Mwa kulalikira uthenga wabwino kwa anthu onse amene timakumana nawo, timaonetsa chilungamo m’njira ina yofunika: Timasonyeza kuti tilibe tsankhu. Kumbukirani kuti “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Kuti titsanzire chilungamo Chake, sitifunika kuweruziratu anthu. Koma tifunika kuuza ena uthenga wabwino mosaganizira mtundu wawo, kaya kuti ndi anthu otani m’deralo, ngakhalenso kuti ali ndi chuma chotani. Mwa kutero, onse amene angamvetsere timawapatsa mpata wa kumva ndi kulabadira uthenga wabwino.—Aroma 10:11-13.

Zimene Timachitira Ena

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani sitifunika kufulumira kuweruza ena? (b) Kodi uphungu wa Yesu wa ‘kusaweruza’ ndi ‘kusatsutsa’ ukutanthauzanji? (Onaninso mawu a m’munsi.)

12 Tingasonyezenso chilungamo mwa kuchitira zinthu ena m’njira imene Yehova amachitira nafe. N’kosavuta kuweruza ena, kutsutsa zolakwa zawo ndi kukayikira zolinga zawo. Koma kodi ndani wa ife amene angafune kuti Yehova azifufuza mopanda chifundo zolinga zathu ndi zolakwa zathu? Si ndimo mmene Yehova amatichitira. Wamasalmo anati: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Kodi sitikuyamikira kuti Mulungu wathu  wolungama ndiponso wachifundo sasankha kumalingalira za zolephera zathu? (Salmo 103:8-10) Ndiyeno, kodi anthu ena tiyenera kuwachitira motani?

13 Ngati tizindikira kuti chilungamo cha Mulungu n’chachifundo, sitidzafulumira kuweruza ena m’nkhani zimene sizikutikhudza kapenanso pa nkhani zosafunika kwenikweni. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anachenjeza kuti: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.” (Mateyu 7:1) Malinga ndi mmene Luka analembera nkhaniyi, Yesu ananenanso kuti: “Musawatsutsa, ndipo simudzatsutsidwa.” * (Luka 6:37) Yesu anasonyeza kuti amadziŵa kuti anthu opanda ungwiro ali ndi chizoloŵezi choweruza anzawo. Aliyense wa omvetsera ake amene anali n’chizoloŵezi choweruza anzake mwankhanza anafunika kuchileka.

14. Kodi tiyenera kuleka ‘kuweruza’ ena pa zifukwa ziti?

14 N’chifukwa chiyani tiyenera kuleka ‘kuweruza’ ena? Chifukwa chimodzi n’chakuti zinthu zimene tingathe kuchita n’zochepa. Wophunzira Yakobo anatikumbutsa kuti: “Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi,” amene ndi Yehova. Motero Yakobo anafunsa mosapita m’mbali kuti: “Iwe woweruza mnzako ndiwe yani?” (Yakobo 4:12; Aroma 14:1-4) Kuwonjezera pamenepa, n’zosavuta kuweruza mokondera chifukwa ndife ochimwa. Tingamaone anthu anzathu molakwika chifukwa cha maganizo ndi zolinga zosiyanasiyana, monga ngati tsankhu, kukhumudwitsidwa, nsanje, ndi kudziona kukhala wolungama. Palinso zina zimene sitingathe kuchita, ndipo kulingalira mbali zimenezi kuyenera kutithandiza kusathamangira kupeza ena zifukwa. Sitingadziŵe za mumtima mwa munthu; ndiponso sitingadziŵe zonse zimene zimachitikira munthu wina. Motero, ndife ayani kuti tizinena okhulupirira anzathu kuti ali ndi zolinga zolakwika, kapenanso kutsutsa zimene akuyesa kuchita potumikira Mulungu? N’kwabwinotu kwambiri kutsanzira  Yehova mwa kufuna kuona zinthu zabwino zimene abale ndi alongo athu amachita m’malo momangoganizira zimene akulephera!

15. Kodi ndi mawu komanso zochita zotani zimene sizifunika kwa olambira Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani?

15 Nanga bwanji anthu a m’banja lathu? N’zachisoni kuti m’dziko lamakonoli, ziweruzo zina zankhanza kwambiri zimaperekedwa pa malo amene amafunika kukhala amtendere—panyumba. Nthaŵi ndi nthaŵi timamva za amuna, akazi, kapena makolo ovuta amene nthaŵi zonse amazazira kapena kumenya anthu a m’banja lawo. Komatu olambira Mulungu sayenera kulankhula mawu okhadzula, onyodola, ngakhalenso kuzunza ena. (Aefeso 4:29, 31; 5:33; 6:4) Uphungu wa Yesu woleka ‘kuweruza’ ndi ‘kutsutsa’ ena umagwiranso ntchito panyumba. Kumbukirani kuti kusonyeza chilungamo kumafuna kuti ife tizichitira zinthu anthu ena mofanana ndi mmene Yehova amachitira nafe. Ndipo Mulungu wathu sachita nafe mouma mtima  kapena mwankhanza. Koma “ali wodzala chikondi” kwa amene amamukonda. (Yakobo 5:11) Alitu chitsanzo chochititsa chidwi kwambiri chimene ife tingatsanzire!

Akulu Amatumikira “M’chiweruzo”

16, 17. (a) Kodi Yehova amayembekeza chiyani kwa akulu? (b) N’chiyani chimafunika kuchitika pamene wochimwa sakusonyeza kulapa koonadi, ndipo n’chifukwa chiyani?

16 Tonsefe tili ndi udindo wosonyeza chilungamo, koma makamaka akulu mu mpingo wachikristu ali ndi udindo wapadera pankhaniyi. Taonani mmene Yesaya analongosolera mwaulosi “akalonga,” kapena kuti akulu. Iye anati: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.” (Yesaya 32:1) Inde, Yehova amayembekeza akulu kutumikira mwachilungamo. Kodi zimenezi angazichite motani?

17 Amuna oyeneretsedwa mwauzimu ameneŵa amadziŵa bwino kuti chilungamo chimafuna kuti mpingo uzikhala woyera nthaŵi zonse. Panthaŵi zina akulu amakakamizika kuweruza nkhani zokhudza tchimo lalikulu. Poweruzapo iwo amakumbukira kuti chilungamo cha Mulungu chimafunafuna kuchitira munthu chifundo ngati kuli kotheka kum’chitira chifundocho. Motero iwo amayesetsa kuti wochimwayo alape. Koma bwanji ngati wochimwayo sakusonyeza kulapa koonadi ngakhale kuti ayesetsa kumuthandiza moteromo? Mwa chilungamo chenicheni, Mawu a Yehova amalangiza kuti afunika kuchitapo kanthu molimba mtima. Iwo amati: “Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” Zimenezi zikutanthauza kumuchotsa mu mpingo. (1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Akulu amamva chisoni kuti akufunika kuchita zimenezi, koma amazindikira kuti n’zofunika potetezera mpingo kuti ukhalebe woyera mwamakhalidwe ndi mwauzimu. Ngakhale zitatero, iwo amayembekeza kuti tsiku lina wochimwayo adzakumbukira mu mtima mwake nasiya zoipa zake ndi kubwereranso mu mpingo.—Luka 15:17, 18.

18. Kodi akulu amakumbukira chiyani pamene akupatsa ena uphungu wochokera m’Baibulo?

18 Kutumikira mwachilungamo kumafunanso kupereka uphungu  wa m’Baibulo kwa amene akufunika uphungu. N’zoona kuti akulu saunguza zimene ena akulakwitsa. Ndiponso salakalaka kuti azingowongolera anzawo. Koma wokhulupirira mnzathu angagwidwe nako “kulakwa kwakuti” pamene iye sakuzindikira. Pokumbukira kuti chilungamo cha Mulungu si chankhanza kaya chouma mtima, akulu adzayesa ‘kubweza wotereyo mu mzimu wa chifatso.’ (Agalatiya 6:1) Motero, akulu sangakalipire munthu wolakwa kapenanso kum’lankhula mawu okhadzula. M’malo mwake, uphungu woperekedwa mwachikondi ndiwo umalimbikitsa munthu amene akuulandirayo. Ngakhale podzudzula munthu mwachindunji—kulongosola mosapita m’mbali zotsatirapo za kuchita zinthu mopanda nzeru—akulu amakumbukira kuti wokhulupirira mnzawo amene walakwayo ndi nkhosa ya m’gulu la Yehova. * (Luka 15:7) Pamene uphungu kapena chidzudzulo chichita kuonekeratu kuti chikuperekedwa chifukwa cha chikondi ndiponso mwa chikondi, n’zosavuta kuti wolakwayo asinthe zochita zake.

19. Kodi akulu amafunika kupanga zosankha zotani, ndipo kodi zosankha zawo ziyenera kuzikidwa pa chiyani?

19 Kaŵirikaŵiri akulu amapanga zosankha zimene zimakhudza okhulupirira anzawo. Mwachitsanzo, nthaŵi ndi nthaŵi amakumana kuti akambirane ngati abale ena mumpingomo akuyenerera kukhala akulu kapena atumiki otumikira. Akulu amadziŵa kuti m’pofunika kukhala wopanda tsankhu. Posankha choti achite, amagwiritsa ntchito ziyeneretso zomwe Mulungu amafuna zokhudza amuna oikidwa pamaudindo amenewo; sadalira pa mmene iwo akuonera munthuyo. Motero iwo amachita zinthu ‘mopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankhu.’—1 Timoteo 5:21.

20, 21. (a) Kodi akulu amayesetsa kukhala otani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi akulu angachite chiyani kuti athandize “amantha mtima”?

20 Akulu amasonyeza chilungamo cha Mulungu m’njira  zinanso. Atanena kuti akulu adzatumikira “m’chiweruzo,” Yesaya ananenanso kuti: “Munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:2) Choncho, akulu amayesetsa kukhala olimbikitsa ndi otsitsimula olambira anzawo.

21 Lerolino, pokhala ndi mavuto ambirimbiri amene amatayitsa mtima, anthu ambiri amafuna chilimbikitso. Akulu, kodi mungachitenji kuti muthandize “amantha mtima”? (1 Atesalonika 5:14) Amvetsereni mwachifundo. (Yakobo 1:19) Iwo angafune kukambirana “nkhaŵa” imene ali nayo mumtima ndi munthu wina amene amamudalira. (Miyambo 12:25) Atsimikizireni kuti ndi ofunika, ndi amtengo wapatali, ndiponso kuti amakondedwa—inde, ndi Yehova komanso ndi abale ndi alongo awo. (1 Petro 1:22; 5:6, 7) Ndiponso, anthu oterowo mungapemphere nawo limodzi komanso mukhoza kuwapempherera.  Zingawalimbikitse kwambiri kumva mkulu akuwapempherera mochokera pansi pamtima. (Yakobo 5:14, 15) Mulungu wa chilungamo adzaona zoyesayesa zanu pothandiza mwachikondi anthu osautsidwa mumtima.

Akulu amaonetsa chilungamo cha Yehova pamene alimbikitsa anthu osautsidwa mumtima

22. Kodi tingatsanzire chilungamo cha Yehova m’njira zotani, ndipo n’chiyani chimene chingatsatirepo?

22 Ndithudi, timayandikana kwambiri ndi Yehova mwa kutsanzira chilungamo chake! Pamene tikuchirikiza miyezo yake yolungama, pamene tiuza ena uthenga wabwino wopulumutsa moyo, ndiponso pamene tisankha kulingalira zinthu zabwino zimene ena amachita m’malo momayang’ana zolakwa zawo, timaonetsa chilungamo cha Mulungu. Akulu, pamene mutetezera chiyero cha mpingo, pamene mupereka uphungu wolimbikitsa wa m’Malemba, pamene mupanga zosankha mopanda tsankhu, ndiponso pamene mulimbikitsa osautsidwa mumtima, mumasonyeza chilungamo cha Mulungu. Mtima wa Yehova umasangalalatu kwambiri pamene akuyang’ana padziko lapansi ali kumwambako ndi kuona anthu ake akuyesetsa mmene angathere ‘kuchita cholungama’ poyenda ndi Mulungu wawo!

^ ndime 13 Mawu otembenuzidwa kuti “musaweruze” ndiponso akuti “musawatsutsa” amatanthauza kuti “musayambe kuweruza” ndiponso kuti “musayambe kutsutsa.” Komabe, m’chinenero choyambiriracho, m’mavesiŵa, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu oletsa ntchito imene ikuchitikabe panthaŵi yoletsayo. Motero zimene analongosolazo zinali kuchitika panthaŵiyo koma anayenera kuzileka.

^ ndime 18 Pa 2 Timoteo 4:2, Baibulo limanena kuti nthaŵi zina akulu ayenera ‘kutsutsa, kudzudzula, kuchenjeza.’ Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “chenjeza” (pa·ra·ka·le′o) angatanthauze “kulimbikitsa.” Mawu enanso achigiriki ofanana ndi ameneŵa, akuti pa·ra′kle·tos, amanena za munthu yemwe amakhalira mnzake kumbuyo pa mlandu. Motero, ngakhale pamene akulu akupereka chidzudzulo champhamvu, afunika kuthandiza anthu amene afooka mwauzimuwo.