Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 28

“Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika”

“Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika”

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mfumu Davide anali kudziŵa bwino za kusakhulupirika kwa munthu?

MFUMU DAVIDE anali kudziŵa bwino za kusakhulupirika kwa munthu. Panthaŵi ina, anthu a mtundu wake womwe anamukonzera chiwembu choukira ulamuliro wake umene unali kukumana ndi mavuto ambiri. Ndiponso, anthu ena amene anakhala osakhulupirika kwa Davide anali anthu omwe tingawayembekezere kukhala anzake a pamtima. Taganizirani za Mikala, mkazi woyamba wa Davide. Poyambirira, iye “anakonda Davide.” Mosakayikira anali kumuthandiza pa zochita zake monga mfumu. Komabe patapita nthaŵi, Mikala anayamba ‘kupeputsa [Davide] mumtima mwake.’ Anafika ngakhale polingalira kuti Davide anali monga munthu wopanda nzeru.—1 Samueli 18:20; 2 Samueli 6:16, 20.

2 Ndiyeno panali mlangizi wa Davide, Ahitofeli. Anthu anali kuona uphungu wake monga mawu onenedwa ndi Yehova. (2 Samueli 16:23) Koma m’kupita kwa nthaŵi, bwenzi lodalirika limeneli linagwirizana ndi gulu limene linali kupandukira Davide. Kodi ndani anayambitsa chiwembucho? Anali Abisalomu, mwana wa Davideyo! Munthu wofunitsitsa kulanda ufumu ameneyu “anakopa mitima ya anthu a Israyeli,” nadziika monga mfumu yolimbana ndi Mfumu Davide. Kupanduka kwa Abisalomu kunakopa anthu ambiri moti Mfumu Davide anakakamizika kuthaŵa poopa kuphedwa.—2 Samueli 15:1-6, 12-17.

3. Kodi Davide anali n’chidaliro chotani?

3 Kodi panalibe aliyense amene anakhalabe wokhulupirika kwa Davide? M’mavuto ake onse, Davide anali kudziŵa kuti pali winawake amene ali wokhulupirika kwa iye. Kodi anali ndani? Si winanso ayi, koma Yehova Mulungu. “Kwa munthu wokhulupirika, inunso mudzakhala wokhulupirika,” Davide ananena zimenezi kwa Yehova. (2 Samueli 22:26, NW) Kodi kukhulupirika n’chiyani, nanga Yehova amapereka motani chitsanzo chapamwamba kwambiri cha khalidwe limeneli?

 Kodi Kukhulupirika N’chiyani?

4, 5. (a) Kodi “kukhulupirika” n’chiyani? (b) Kodi kukhulupirika kumene tikulongosola m’nkhani ino kukusiyana motani ndi kukhulupirika kongokhala wodalirika?

4 Mawu akuti “kukhulupirika” monga momwe agwiritsidwira ntchito m’Malemba Achihebri, amafotokoza munthu wokoma mtima amene mwachikondi amadziphatika ku chinthu chinachake ndipo sachisiya chinthucho mpaka cholinga chake pa chinthu chimenecho chitakwaniritsidwa. Kukhulupirika kumeneku si kuja kongokhala munthu wodalirika. Zili choncho chifukwa munthu wokhulupirika m’lingaliro lokhala wodalirika angamachite zimenezo popeza akudziŵa kuti ali ndi udindo umenewo. Mosiyana ndi lingaliro limeneli, kukhulupirika kumene tikulongosola m’nkhani ino kumazikidwa pa chikondi. * Ndiponso, nazo zinthu zopanda moyo zikhoza kukhala zokhulupirika m’lingaliro la kukhala zodalirika. Mwachitsanzo, wamasalmo anati mwezi ndi “mboni yokhulupirika kuthambo” chifukwa chakuti umaoneka nthaŵi zonse usiku. (Salmo 89:37) Komatu sitinganene kuti mwezi ndi wokhulupirika m’lingaliro lofanana ndi mmene munthu angakhalire wokhulupirika. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kukhulupirika kwa munthu  kungaonetse chikondi chimene munthuyo ali nacho, pamene zinthu zopanda moyo zilibe chikondi.

Mwezi ukutchedwa mboni yokhulupirika, koma ndi zolengedwa zamoyo ndi zanzeru zokha zimene zingaonetsedi kukhulupirika kokhala ndi chikondi kwa Yehova

5 M’lingaliro la m’Malemba, munthu wokhulupirika ndi waubwenzi. Mawu okhawo akuti kukhulupirika amasonyeza kuti pali ubale winawake pakati pa munthu wokhulupirikayo ndi munthu yemwe akumuonetsa kukhulupirikako. Kukhulupirika kotereku sikuti kumangochitika mwa apo ndi apo. Sikuli ngati mafunde a panyanja amene amakankhidwa ndi mphepo zosinthasintha. Koma munthu wokhulupirika, kapena kuti wachikondi chokhulupirika, amakhala wokhazikika ndi wolimba kotero kuti amatha kugonjetsa mavuto aakulu kwambiri.

6. (a) Kodi anthu okhulupirika ndi ochepa motani, ndipo zimenezi zikusonyezedwa motani m’Baibulo? (b) Kodi ndi iti imene ili njira yabwino kwambiri yophunzirira zimene kukhulupirika kumatanthauza, nanga n’chifukwa chiyani?

6 N’zoona kuti lerolino si ambiri amene ali okhulupirika moteromo. Kaŵirikaŵiri anthu amene amagwirizana kwambiri ‘amawonongana.’ Nthaŵi zambiri timamva za anthu amene athaŵa akazi awo kapena amuna awo. (Miyambo 18:24; Malaki 2:14-16) Zochitika zachinyengo n’zofala kwambiri moti tikhoza kumabwereza mawu a mneneri Mika akuti: “Watha wachifundo [“wokhulupirika,” NW] m’dziko.” (Mika 7:2) Ngakhale kuti nthaŵi zambiri anthu amalephera kukhala okoma mtima mwachikondi, Yehova amaoneka mwapadera kuti ndi wokhulupirika. Ndipotu njira yabwino yophunzirira zimene kukhulupirika kumatanthauza ndiyo kuphunzira mmene Yehova amaonetsera mbali yaikulu imeneyi ya chikondi chake.

Yehova Ndi Wokhulupirika Kuposa Aliyense

7, 8. Kodi tinganene bwanji kuti Yehova yekha ndiye wokhulupirika?

7 Baibulo limanena za Yehova kuti: “Inu nokha ndinu wokhulupirika.” (Chivumbulutso 15:4, NW) Kodi zimenezi zili choncho motani? Kodi anthu ndiponso angelo nthaŵi zina sanakhalepo okhulupirika mochititsa chidwi? (Yobu 1:1; Chivumbulutso 4:8) Nanga bwanji Yesu Kristu? Kodi iye sindiye “wokhulupirika” wamkulu wa Mulungu? (Salmo 16:10, NW) Nangano Yehova akunenedwa bwanji kuti iye yekha ndiye wokhulupirika?

 8 Choyamba, kumbukirani kuti kukhulupirika ndi mbali ya chikondi. Popeza kuti “Mulungu ndiye chikondi”—iye ndiye chitsanzo chenicheni cha khalidwe limeneli—ndaninso akanakhala wokhulupirika kwambiri kuposa Yehova? (1 Yohane 4:8) Inde, angelo komanso anthu akhoza kusonyeza makhalidwe a Mulungu, komatu ndi Yehova yekha amene ndi wokhulupirika kwambiri kuposa wina aliyense. Pokhala “nkhalamba ya kale lomwe,” iye wakhala akusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa nthaŵi yaitali kuposa cholengedwa chilichonse, chapadziko lapansi kapena chakumwamba. (Danieli 7:9) Motero, kukhulupirika kwagona mwa Yehova. Ndi wokhulupirika m’njira yoti palibe cholengedwa chilichonse chingafikepo. Taonani zitsanzo izi.

9. Kodi Yehova ndi “wokhulupirika m’ntchito zake zonse” motani?

9 Yehova ndi “wokhulupirika m’ntchito zake zonse.” (Salmo 145:17, NW) Motani? Yankho tikulipeza mu Salmo 136. Mmenemu mukutchulidwa zochita zingapo zopulumutsa za Yehova, kuphatikizapo kulanditsidwa kochititsa kaso kwa Aisrayeli pa Nyanja Yofiira. N’zochititsa chidwi kuti vesi lililonse mu salmo limeneli likutsindikidwa ndi mawu akuti: “Pakuti chifundo chake [“kukoma mtima kwake kwachikondi,” NW] n’chosatha.” Salmo limeneli lilinso mu bokosi la Mafunso Owasinkhasinkha patsamba 289. Pamene mukuŵerenga mavesi amenewo, mudzachita chidwi kwambiri ndi njira zosiyanasiyana za momwe Yehova analili wokoma mtima mwachikondi kwa anthu ake. Inde, Yehova amasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake okhulupirika mwa kumvetsera iwo akamafuula kuti awathandize ndiponso mwa kuchitapo kanthu pa nthaŵi yake yoikika. (Salmo 34:6) Chikondi chokhulupirika cha Yehova pa atumiki ake sichisintha malinga ngati iwo akhalabe okhulupirika kwa iye.

10. Kodi Yehova amakhala wokhulupirika motani ndi miyezo yake?

10 Ndiponso, Yehova amakhala wokhulupirika kwa atumiki ake mwa kutsatira miyezo yake. Mosiyana ndi anthu amene amasinthasintha mfundo zawo, amene amangochita zinthu modzidzimukira ndiponso motengeka maganizo, Yehova sasintha kaonedwe kake ka chimene chili chabwino ndi chimene chili choipa. Kwa zaka masauzande ambirimbiri, malingaliro ake sanasinthe pa zinthu ngati kukhulupirira mizimu,  kulambira mafano, ndiponso kupha munthu. “Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine,” iye anatero kudzera mwa mneneri wake Yesaya. (Yesaya 46:4) Motero, tingakhale n’chidaliro chakuti tidzapindula mwa kutsatira malangizo omveka a makhalidwe abwino amene ali m’Mawu a Mulungu.—Yesaya 48:17-19.

11. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yehova amasunga mawu amene walonjeza.

11 Yehova alinso wokhulupirika pokwaniritsa malonjezo ake. Akanena kuti chinachake chidzachitika m’tsogolo, chimachitikadi. Choncho Yehova anati: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.” (Yesaya 55:11) Mwa kusunga mawu ake, Yehova amakhala wokhulupirika kwa anthu ake. Sawadikiriritsa chinthu chimene iye akudziŵa kuti sichichitika. Mbiri imene Yehova ali nayo pankhani imeneyi ndi yabwino kwambiri moti mtumiki wake Yoswa ananena kuti: “Sikadasoŵa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.” (Yoswa 21:45) Ndiyetu tingakhale n’chidaliro chakuti sitidzakhumudwa konse chifukwa chakuti Yehova walephera kukwaniritsa malonjezo ake.—Yesaya 49:23; Aroma 5:5.

12, 13. Kodi kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova ‘n’kosatha’ m’njira zotani?

12 Monga taonera kale, Baibulo limatiuza kuti kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova ‘n’kosatha.’ (Salmo 136:1) Kodi izi zili choncho motani? Mbali imodzi ya zimenezi ndi yakuti Yehova amakhululukira machimo kwa nthaŵi zonse. Monga tinalongosolera m’Mutu 26, Yehova sakumbutsanso zolakwa zakale zimene munthu anamukhululukira. Popeza kuti “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu,” tonsefe tiyenera kuthokoza kuti Yehova ndi wokoma mtima mwachikondi nthaŵi zonse.—Aroma 3:23.

13 Koma kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova kulinso kosatha m’lingaliro linanso. Mawu ake amanena kuti wolungama “akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:3) Talingalirani mtengo  wokula bwino umene masamba ake safota! Momwemonso ngati ife timakondadi Mawu a Mulungu, tidzakhala ndi moyo wautali, wamtendere, ndi wopindulitsa. Mokhulupirika Yehova amapereka madalitso osatha kwa atumiki ake okhulupirika. Ndithudi, m’dziko latsopano lolungama limene Yehova adzabweretsa, anthu omvera adzaona kuti iye ndi wokoma mtima mwachikondi kunthaŵi zosatha.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Yehova “Sataya Okhulupirika Ake”

14. Kodi Yehova amayamikira motani kukhulupirika kwa atumiki ake?

14 Yehova waonetsa mobwerezabwereza kuti ndi wokhulupirika. Popeza kuti zochita za Yehova nthaŵi zonse sizitsutsana, sayamba kumakhulupirika pang’ono kwa atumiki ake okhulupirika. Wamasalmo analemba kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya. Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa [“okhulupirika ake,” NW].” (Salmo 37:25, 28) N’zoona kuti timayenera kulambira Yehova popeza ndi Mlengi. (Chivumbulutso 4:11) Komabe popeza kuti iye ndi wokhulupirika, amasangalala ndi zochita zathu zachikhulupiriro.—Malaki 3:16, 17.

15. Fotokozani mmene zomwe Yehova anachitira Aisrayeli zimasonyezera kuti ndi wokhulupirika.

15 Chifukwa chakuti ndi wokoma mtima mwachikondi, mobwerezabwereza Yehova amathandiza anthu ake pamene akuvutika. Wamasalmo anati: “Iye asunga moyo wa okondedwa [“okhulupirika,” NW] ake; awalanditsa m’manja mwa oipa.” (Salmo 97:10) Lingalirani zimene anachita ndi mtundu wa Israyeli. Atawalanditsa mozizwitsa pa Nyanja Yofiira, Aisrayeli anaimbira Yehova nyimbo, kuti: “Mwa chifundo chanu [“chikondi chanu chokhulupirika,” NW, mawu a m’munsi] mwatsogolera anthu amene mudawawombola.” (Eksodo 15:13) Ndithudi Yehova anaonetsa chikondi chokhulupirika polanditsa Aisrayeli pa Nyanja Yofiira. Motero Mose anauza Aisrayeli kuti: “Yehova sanakondwera nanu, ndi kukusankhani chifukwa cha kuchuluka kwanu koposa mitundu yonse ina ya anthu, kapena kuchepera kwanu; koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu,  ndi kukuwombolani m’nyumba ya akapolo, m’dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.”—Deuteronomo 7:7, 8.

16, 17. (a) Kodi ndi kusayamikira kodabwitsa kotani kumene Aisrayeli anaonetsa, komabe kodi Yehova anawachitira chifundo motani? (b) Kodi Aisrayeli ambiri anasonyeza motani kuti ‘panalibe chowalanditsa,’ ndipo zimenezi zikutichenjezanji?

16 N’zoona kuti monga mtundu Aisrayeli analephera kuyamikira kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova. Atalanditsidwa ‘anawonjeza kumuchimwira [Yehova], mwa kupikisana ndi Wam’mwambamwamba.’ (Salmo 78:17) Kwa zaka mazana ambiri, anali kupanduka mobwerezabwereza; anali kusiya Yehova n’kutembenukira kwa milungu yonyenga ndi kumachita zinthu zachikunja zimene zinali kungowaipitsa. Komabe Yehova sanathetse pangano lake. M’malo mwake, kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anachonderera anthu ake kuti: “Bwera iwe Israyeli wobwerera . . . sindidzakuyang’anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo [“wokhulupirika,” NW].” (Yeremiya 3:12) Komabe monga tinaonera m’Mutu 25, Aisrayeli ambiri sanakhudzike mtima. Ndipotu, iwo “ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake.” Kodi chinatsatirapo n’chiyani? ‘Ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe chowalanditsa.’—2 Mbiri 36:15, 16.

17 Kodi n’chiyani tikuphunzira pamenepa? Tikuphunzira kuti pamene Yehova ali wokhulupirika sikuti saona zolakwika kapenanso kuti akhoza kunyengeka. N’zoona kuti Yehova ndi “wa ukoma mtima wochuluka,” ndipo amasangalala kuchitira ena chifundo pakakhala zifukwa zokwanira. Koma kodi Yehova amachitanji pamene wolakwa akhala woipa kwambiri moti sangasinthe? Zikatero Yehova amatsatira miyezo yake yolungama ndi kupereka chiweruzo chokhwima. Monga momwe Mose anauzidwira, Yehova ‘samasula wopalamula.’—Eksodo 34:6, 7.

18, 19. (a) Kodi pamene Yehova walanga oipa zimasonyeza motani kuti ndi wokhulupirika? (b) Kodi Yehova adzaonetsa m’njira yotani kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake amene azunzidwa mpaka kufa?

18 Mulungu amaonekanso kuti ndi wokhulupirika pamene walanga  oipa. Motani? Umboni umodzi uli m’buku la Chivumbulutso mu nkhani imene Yehova akulamula angelo asanu ndi aŵiri kuti: “Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziŵiri za mkwiyo wa Mulungu.” Pamene mngelo wachitatu watsanulira mbale yake mu “mitsinje ndi akasupe a madzi,” zonse zasanduka magazi. Ndiyeno mngelo akuuza Yehova kuti: “Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu [“wokhulupirika Inu,” NW], chifukwa mudaweruza kotero; popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo” kutero.—Chivumbulutso 16:1-6.

Mokhulupirika Yehova adzakumbukira ndi kuukitsa amene akhala okhulupirika mpaka kufa

19 Onani kuti ali m’kati mopereka uthenga wachiweruzo umenewo, mngeloyo akunena Yehova kuti “wokhulupirika Inu.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mwa kuwononga oipa, Yehova akuonetsa kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake omwe ambiri azunzidwa mpaka kufa. Mokhulupirika, anthu oterowo Yehova amawakumbukira kwambiri monga amoyo. Iye amakhumba ataonanso okhulupirika amene anachokaŵa, ndipo Baibulo limatsimikizira kuti cholinga chake ndi kuwafupa ndi chiukiriro. (Yobu 14:14, 15) Yehova saiwala atumiki ake okhulupirika chifukwa chakuti iwo anafa. M’malo mwake, “onse akhala ndi moyo kwa Iye.” (Luka 20:37, 38) Cholinga cha Yehova  chopatsanso moyo anthu amene iye akuwakumbukira chili umboni wamphamvu wakuti iye ndi wokhulupirika.

Bernard Luimes (pamwamba) ndi Wolfgang Kusserow (pakati) anaphedwa ndi a Nazi

Gulu la ndale linabaya Moses Nyamussua ndi mkondo mpaka kumupha

Chikondi Chokhulupirika cha Yehova Chitsegula Njira ya Chipulumutso

20. Kodi “zotengera zachifundo” ndi ndani, ndipo Yehova ndi wokhulupirika motani kwa iwo?

20 M’mbiri yonse ya anthu, Yehova mochititsa chidwi kwambiri wakhala wokhulupirika kwa anthu okhulupirika. Ndipotu, kwa zaka masauzande ambiri, Yehova “analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko.” Chifukwa chiyani? “Kuti iye akadziŵitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero.” (Aroma 9:22, 23) “Zotengera zachifundo” zimenezi ndi anthu ofuna moyo wosatha amene amadzozedwa ndi mzimu woyera kuti akalamulire limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake. (Mateyu 19:28) Mwa kutsegulira zotengera zachifundo zimenezi  njira ya chipulumutso, Yehova anapitiriza kukhala wokhulupirika kwa Abrahamu, yemwe anapangana naye lonjezo ili: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga.”—Genesis 22:18.

Chifukwa chakuti Yehova ndi wokhulupirika, atumiki ake onse okhulupirika ali ndi chiyembekezo chodalirika cha m’tsogolo

21. (a) Kodi Yehova ndi wokhulupirika motani kwa “khamu lalikulu” limene likuyembekeza kudzatuluka “m’chisautso chachikulu”? (b) Kodi kukhulupirika kwa Yehova kukukulimbikitsani kuchitanji?

21 Yehova amasonyezanso kukhulupirika kofananako kwa “khamu lalikulu” limene likuyembekeza kudzatuluka “m’chisautso chachikulu” ndi kudzakhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Ngakhale kuti atumiki ake ndi opanda ungwiro, mokhulupirika Yehova akuwapatsa mwayi wokhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi la paradaiso. Kodi zimenezi akuzichita motani? Akuzichita pogwiritsa ntchito dipo, chitsanzo chachikulu chakuti Yehova ndi wokhulupirika. (Yohane 3:16; Aroma 5:8) Kukhulupirika kwa Yehova kumakopa anthu amene ali ndi njala yachilungamo m’mitima yawo. (Yeremiya 31:3) Kodi simukumva kukhala woyandikana kwambiri ndi Yehova chifukwa chakuti wakhala wokhulupirika kwambiri ndiponso kuti adzakhulupirikabe? Popeza tikulakalaka kuyandikana ndi Mulungu, tilabadiretu chikondi chake mwa kulimbitsa chosankha chathu chomutumikira mokhulupirika.

^ ndime 4 N’zochititsa chidwi kuona kuti mawu amene atembenuzidwa kuti “kukhulupirika” pa 2 Samueli 22:26 mu Baibulo la New World Translation, m’malo ena m’Baibulo lomwelo anatembenuzidwa kuti “kukoma mtima kwachikondi” kapena “chikondi chokhulupirika.”