Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 2

Kodi ‘Mungayandikiredi Kwa Mulungu’?

Kodi ‘Mungayandikiredi Kwa Mulungu’?

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chimene anthu ambiri angaone ngati chosatheka, koma kodi Baibulo limatitsimikizira za chiyani? (b) Kodi Abrahamu anapatsidwa unansi wabwino wotani, nanga n’chifukwa chiyani?

KODI mungamve bwanji ngati Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi akunena za inuyo kuti, “Uyu ndi bwenzi langa”? Anthu ambiri angalingalire kuti zimenezi n’zosatheka. Ndiponso, kodi munthu angakhale bwanji pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu? Komatu, Baibulo limatitsimikizira kuti tikhoza kuyandikana ndi Mulungu.

2 Abrahamu, yemwe anakhalapo kalekalelo, anali woyandikana naye moteromo. Polankhula za kholo limenelo Yehova anati “bwenzi langa.” (Yesaya 41:8) Ee, Yehova anamuona Abrahamu kuti anali bwenzi lake lenileni. Abrahamu anali naye pa unansi wabwino chonchi chifukwa “anakhulupirira Mulungu.” (Yakobo 2:23) Lerolinonso, Yehova amafunafuna mipata ‘yokondwera’ ndi amene amamutumikira mwachikondi. (Deuteronomo 10:15) Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Mawu ameneŵa akutiuza kuchita kanthu kena ndiponso akutipatsa lonjezo.

3. Kodi Yehova akutiuza kuchitanji, ndipo ndi lonjezo lotani lomwe akupereka mogwirizana ndi zimenezi?

3 Yehova akutiuza kuti timuyandikire. Iye ndi wokonzeka ndiponso ndi wofunitsitsa kutivomereza kuti ndife mabwenzi ake. Panthaŵi imodzimodziyo akulonjeza kuti ngati tiyamba kumuyandikira, iyenso adzatiyandikira. Motero tingapange naye chinthu chamtengo wapatali zedi, “ubwenzi ndi Yehova.” * (Salmo 25:14, NW) Mawu akuti “ubwenzi” ali ndi lingaliro la  kukhala womasuka kuuzana zakukhosi ndi bwenzi lako lapadera.

4. Kodi bwenzi lapamtima limakhala lotani, nanga Yehova amakhala bwenzi loterolo motani kwa amene amamuyandikira?

4 Kodi muli ndi bwenzi lapamtima limene mungaliuze zakukhosi kwanu? Limenelo ndi bwenzi limene limakuganizirani. Mumalidalira chifukwa lakhala lokhulupirika. Mumapitirira kusangalala pamene mukambirana naye nkhani zokusangalatsani. Mtolo wa chisoni womwe mumakhala nawo umapepuka chifukwa iye amakumvetserani mwachifundo. Iye amakumvetsetsani ngakhale pamene zikuoneka kuti palibe yemwe akukumvetsetsani. Mofananamo, mukayandikira kwa Mulungu, mumakhala ndi Bwenzi lapadera lomwe limakuyamikirani kwambiri, limakuganizirani koposa, ndi kukumvetsetsani kwabasi. (Salmo 103:14; 1 Petro 5:7) Mumamudalira ndi mtima wanu wonse popeza mumadziŵa kuti amakhala wokhulupirika kwa amene ali wokhulupirika kwa iye. (Salmo 18:25) Komabe, mwayi umenewu wokhala pa ubwenzi ndi Mulungu timaupeza kokha chifukwa chakuti iye waupanga kukhala wotheka.

Yehova Watsegula Njira

5. Kodi Yehova anachitanji kuti tithe kumuyandikira?

5 Patokha anthu ochimwafe sitikanayandikana ndi Mulungu. (Salmo 5:4) “Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife,” analemba motero mtumwi Paulo. (Aroma 5:8) Inde, Yehova anakonza kuti Yesu ‘apereke moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Timatha kuyandikira kwa Mulungu chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo imeneyo. Popeza kuti Mulungu ndiye ‘anayamba kutikonda,’ anatiyalira maziko okhala naye pa ubwenzi.—1 Yohane 4:19.

6, 7. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova si Mulungu wobisika yemwe sitingathe kumudziŵa? (b) Kodi Yehova wadziulula m’njira zotani?

6 Yehova wachitanso kanthu kena: Wadziulula kwa ife. Pa ubwenzi uliwonse, mumakhala ogwirizana kwambiri chifukwa cha kumudziŵa bwino munthu winayo ndiponso kuyamikira  khalidwe lake ndi mmene amachitira zinthu. Motero ngati Yehova anali Mulungu wobisika ndi wosatheka kudziŵika, sitikanamuyandikira. Komatu m’malo modzibisa, amafuna kuti timudziŵe. (Yesaya 45:19) Chinanso, zimene iye amadziulula n’zopezeka kwa aliyense, ngakhale ife amene tingaoneke ngati anthu otsika mwa miyezo ya dzikoli.—Mateyu 11:25.

Yehova wadziulula kudzera m’zimene analenga ndi m’Mawu ake olembedwa

7 Kodi Yehova wadziulula motani kwa ife? Zinthu zimene analenga zimatidziŵitsa mbali zina za umunthu wake—kuchuluka kwa mphamvu zake, nzeru zake, ndi chikondi chake. (Aroma 1:20) Koma Yehova sadziulula ndi zinthu zimene analenga zokha. Iye nthaŵi zonse amadziŵitsa ena zinthu m’njira yapamwamba kwambiri, motero watiuza za iye mwini m’Mawu ake olembedwa, Baibulo.

Kuona ‘Chisomo cha Yehova’

8. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo palokha ndi umboni wakuti Yehova amatikonda?

8 Baibulo palokha ndi umboni wakuti Yehova amatikonda. M’Mawu ake, amadziulula mwa mawu osavuta kumva, womwe ndi umboni osati kokha wakuti amatikonda komanso wakuti amafuna timudziŵe ndi kumukonda. Zimene timaŵerenga m’buku lamtengo wapatali limeneli zimatithandiza kuona ‘chisomo cha Yehova’ ndipo zimatilimbikitsa kufuna kuyandikana naye. (Salmo 90:17) Tiyeni tikambirane zina mwa njira zosangalatsa zimene Yehova anadziululira m’Mawu ake.

9. Kodi zitsanzo zina n’ziti za mawu a m’Baibulo amene amanena za makhalidwe a Mulungu molunjika?

9 M’Malemba muli mawu ambirimbiri amene amanena molunjika za makhalidwe a Mulungu. Taonani zitsanzo izi. “Yehova akonda chiweruzo.” (Salmo 37:28) Mulungu ndi wa “mphamvu yoposa.” (Yobu 37:23) “Ine ndili wachifundo, ati Yehova.” (Yeremiya 3:12) “Ndiye wa mtima wanzeru.” (Yobu 9:4) Iye ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 34:6) “Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5) Ndipo monga tinafotokozera m’mutu wapitawo, ali ndi khalidwe lina lomwe limaposa ena  onse: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Pamene musinkhasinkha za makhalidwe osangalatsa ameneŵa, kodi simukulakalaka kuyandikana ndi Mulungu wosayerekezeka ameneyu?

Baibulo limatithandiza kuyandikira kwa Yehova

10, 11. (a) Kuti atithandize kuona mosavuta umunthu wake, kodi Yehova waikamonso chiyani m’Mawu ake? (b) Kodi n’chitsanzo chotani cha m’Baibulo chimene chimatithandiza kuona Mulungu akugwiritsa ntchito mphamvu zake?

10 Kuwonjezera pa kutiuza makhalidwe ake, mwachikondi Yehova m’Mawu ake anaikamonso zitsanzo za mmene anasonyezera makhalidwewo pochita zinthu ndi ena. Nkhani zoterozo zimatipatsa zithunzithunzi zooneka bwino m’maganizo athu zomwe zimatisonyeza mosavuta mbali zosiyanasiyana za umunthu wake. Ndiyeno zimenezi zimatithandiza kumuyandikira. Taonani chitsanzo ichi.

11 Munthu angaŵerenge kuti Mulungu ali “wolimba mphamvu.” (Yesaya 40:26) Komatu akhoza kumva mfundoyi mosiyana pamene aŵerenga za mmene Mulungu analanditsira Israyeli pa Nyanja Yofiira ndiyeno n’kukhala akusamalira mtunduwo m’chipululu kwa zaka 40. Mungathe kuona m’maganizo mwanu madzi oyenda mwamphamvu akugaŵikana. Mungauone mtunduwo, mwinamwake anthu 3,000,000 onse pamodzi, akuyenda pansi pa nyanjayo pouma, madzi oundanawo ataima ngati makoma akuluakulu kumbali zonse ziŵiri. (Eksodo 14:21; 15:8) Mukhoza kuona umboni wakuti Mulungu anali kuwasamalira bwino m’chipululu. Madzi anatuluka m’thanthwe. Chakudya, chokhala ngati zipatso zoyera, chinali kupezeka pansi. (Eksodo 16:31; Numeri 20:11) Pano Yehova akuulula kuti si kuti ali ndi mphamvu zokha, komanso kuti amazigwiritsa ntchito pothandiza anthu ake. Kodi si zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti mapemphero athu amapita kwa Mulungu wamphamvu  amene “ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso”?—Salmo 46:1.

12. Kodi Yehova amatithandiza motani “kumuona” mwa mawu amene tingamvetse?

12 Yehova, yemwe ndi mzimu, wachita zambiri potithandiza kumudziŵa. Monga anthu timangoona zinthu zooneka, motero sitingaone zomwe zili m’malo a mizimu. Ngati Mulungu akanatiuza za iye mwini mogwiritsa ntchito mawu a mizimu, kukanakhala kofanana ndi kuti inuyo mukuuza munthu yemwe anabadwa wosaona mmene maso anu kapena khungu lanu limaonekera. Komabe Yehova mokoma mtima amatithandiza “kumuona” mwa mawu amene tingamvetse. Nthaŵi zina amagwiritsa ntchito mafanizo; amadzifanizira ndi zinthu zimene timazidziŵa. Amadzilongosolanso ngati kuti ali ndi ziwalo zina za munthu. *

13. Kodi Yesaya 40:11 amapereka chithunzi chotani m’maganizo anu, nanga zimakukhudzani motani?

13 Taonani mmene Yesaya 40:11 akulongosolera Yehova: “Iye adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake [“ndi mkono wake,” NW], nadzawatengera pa chifuwa chake.” Pano Yehova akumuyerekeza ndi mbusa amene amanyamula ana a nkhosa ndi “mkono wake.” Izi zikusonyeza kuti Mulungu ndi wokhoza kuteteza ndi kuthandiza anthu ake, ngakhale amene ali ofooka kwambiri. Tingamve kukhala osungika m’manja ake amphamvu, pakuti ngati tili okhulupirika kwa iye, sadzatisiya konse. (Aroma 8:38, 39) Mbusa Wamkuluyo amanyamula ana a nkhosa “pa chifuwa chake.” Mawuŵa amafotokoza za chovala chakumtunda chomwe chapindidwa. Nthaŵi zina pa chovala chimenechi mbusa anali kunyamulirapo mwana wa nkhosa yemwe wabadwa kumene. Motero akutitsimikizira kuti Yehova amationa kukhala  amtengo wapatali ndipo amatisamalira mwachikondi. N’kwachibadwa kufuna kuyandikana naye.

‘Mwana Afuna Kumuulula Iye’

14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amadziulula bwino kwambiri kupyolera mwa Yesu?

14 M’Mawu ake, Yehova amadziulula bwino kwambiri kupyolera mwa Mwana wake wokondedwa, Yesu. Palibe amene akanaonetsa bwino kwambiri mmene Mulungu amaganizira ndi kumvera, kapenanso yemwe akanamulongosola momveka bwino kuposa mmene anachitira Yesu. Ndiiko komwe, Mwana woyamba kubadwa ameneyo anali ndi Atate wake zolengedwa zina zauzimu ngakhalenso chilengedwe china chonsechi chisanalengedwe. (Akolose 1:15) Yesu anali wozoloŵerana kwambiri ndi Yehova. N’chifukwa chake ananena kuti: “Palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.” (Luka 10:22) Ali padziko lapansi monga munthu, Yesu anaulula Atate wake m’njira ziŵiri zofunika kwambiri.

15, 16. Kodi Yesu anaulula Atate wake m’njira ziŵiri ziti?

15 Njira yoyamba, ziphunzitso za  Yesu zimatithandiza kudziŵa Atate wake. Yesu anafotokoza Yehova mwa mawu ogwira mtima. Mwachitsanzo, polongosola Mulungu wachifundo amene amalandiranso ochimwa olapa, Yesu anayerekeza Yehova ndi atate wokhululukira yemwe anagwidwa chifundo kwambiri ataona mwana wake wosakaza akubwerera kunyumba. Atateyo anathamangira mwana wakeyo, namukupatira pakhosi, n’kumupsopsonetsa. (Luka 15:11-24) Yesu anaonetsanso Yehova kuti ndi Mulungu amene ‘amakoka’ anthu a mitima yabwino chifukwa amawakonda aliyense payekha. (Yohane 6:44) Amadziŵa ngakhale pamene mpheta yagwa pansi. “Musamaopa,” anatero Yesu, “inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29, 31) Ndithudi sitingachitire mwina koma kuyandikira kwa Mulungu wosamala wotereyu.

16 Njira yachiŵiri, chitsanzo cha Yesu chimatisonyeza mmene Yehova alili. Yesu anaonetsa bwino kwambiri mmene Atate wake alili moti ananena kuti: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.” (Yohane 14:9) Motero, pamene tiŵerenga za Yesu m’Mauthenga Abwino, malingaliro amene anali nawo ndiponso mmene anali kuchitira zinthu ndi ena, timakhala tikuona chithunzithunzi chenicheni cha Atate wake. Yehova sakanatiululira momveka bwino makhalidwe ake kuposa pamenepa. Chifukwa chiyani?

17. Perekani chitsanzo cha zimene Yehova wachita potithandiza kumvetsetsa mmene iye alili.

17 Nachi chitsanzo: Yerekezani kuti mukuyesa kufotokoza kuti kukoma mtima n’chiyani. Mukhoza kupereka tanthauzo lake mwa mawu. Koma ngati mungaloze munthu wina yemwe akuchitira ena mokoma mtima ndiyeno n’kunena kuti, “Ameneyo ndiye munthu wokoma mtima,” tanthauzo la mawu akuti “kukoma mtima” limadziŵika kwambiri ndipo munthu amamvetsetsa mosavuta. Yehova wachita zofanana ndi zimenezo potithandiza kumvetsetsa mmene iye alili. Kuwonjezera pa kudzilongosola mwa mawu ake, watipatsanso chitsanzo chabwino cha Mwana wake. Mwa Yesu, timaona makhalidwe a Mulungu pochita zinthu ndi anthu. Kupyolera m’nkhani za m’Mauthenga Abwino zonena za Yesu, Yehova kwenikweni akunena kuti:  “Ndimo mmene ine ndilili.” Kodi nkhani zouziridwazo zimamulongosola motani Yesu pamene anali padziko lapansi?

18. Kodi Yesu anasonyeza motani mphamvu, chilungamo, ndi nzeru?

18 Yesu anasonyeza mosangalatsa kwambiri mbali zinayi zikuluzikulu za umunthu wa Mulungu. Anali ndi mphamvu pa matenda, njala, ngakhale imfa. Komatu, mosiyana ndi anthu adyera omwe amagwiritsa ntchito molakwa mphamvu zawo, iye sanagwiritse ntchito mphamvu podzichitira zozizwitsa kapena kupweteka nazo ena. (Mateyu 4:2-4) Yesu anakonda chilungamo. Ataona amalonda achinyengo akubera anthu, iye ananyansidwa. (Mateyu 21:12, 13) Analibe tsankhu ndi munthu aliyense; anthu osauka ndi oponderezedwa anawathandiza ‘kupeza mpumulo’ wa miyoyo yawo. (Mateyu 11:4, 5, 28-30) Ziphunzitso za Yesu, yemwe anali ‘woposa Solomo,’ zinali za nzeru zosayerekezeka. (Mateyu 12:42) Koma Yesu sanadzionetsere kuti anali wanzeru. Mawu ake ankafika anthu wamba pamtima, popeza kuti ziphunzitso zake zinali zomveka bwino, zosavuta, ndiponso zothandiza.

19, 20. (a) Kodi Yesu anali chitsanzo chapadera motani cha chikondi? (b) Pamene tikuŵerenga ndi kusinkhasinkha za chitsanzo cha Yesu, kodi tiyenera kukumbukira chiyani?

19 Yesu anali chitsanzo chapadera cha chikondi. Mu utumiki wake wonse, anasonyeza chikondi cha mitundumitundu, kuphatikizapo kumvera ena chisoni ndi chifundo. Anali kuchita chifundo akaona anthu akuvutika. Nthaŵi ndi nthaŵi, anali kuchitapo kanthu pa zosoŵa za ena chifukwa chofulumira kuzizindikira. (Mateyu 14:14) Ngakhale kuti anachiritsa odwala ndi kudyetsa anjala, Yesu anasonyeza chifundo m’njira ina yofunika kwambiri. Anathandiza anthu ena kudziŵa choonadi cha Ufumu wa Mulungu, womwe udzabweretsa madalitso osatha kwa anthu. Anawathandizanso kuvomereza choonadicho ndi kuchikonda. (Marko 6:34; Luka 4:43) Koposa zonse, Yesu anaonetsa chikondi chodzimana mwa kupereka moyo wake modzifunira m’malo mwa ena.—Yohane 15:13.

20 Ndiye kodi n’zodabwitsa kuti anthu a misinkhu yonse ndiponso achikhalidwe chosiyanasiyana anayandikira kwa  munthu wachikondi ndi wachifundo kwambiri ameneyu? (Marko 10:13-16) Komabe, pamene tiŵerenga ndi kusinkhasinkha za chitsanzo cha zochitika zenizeni za Yesu, nthaŵi zonse tiyeni tikumbukire kuti mwa Mwana ameneyu tikuona chithunzi chooneka bwino cha Atate wake.—Ahebri 1:3.

Buku Lotithandiza Kuphunzira

21, 22. Kodi kufunafuna Yehova kumaphatikizapo chiyani, nanga m’buku lothandiza kuphunzira lino muli chiyani chomwe chidzatithandiza pochita zimenezi?

21 Mwa kudziulula momveka bwino m’Mawu ake, Yehova akutitsimikizira kuti amafuna kuti timuyandikire. Panthaŵi imodzimodziyo, sakutikakamiza kuyanjana naye. Zili kwa ife kumufunafuna “popezeka Iye.” (Yesaya 55:6) Kufunafuna Yehova kumaphatikizapo kudziŵa makhalidwe ake ndiponso mmene amachitira zinthu monga zasonyezedwera m’Baibulo. Buku lothandiza kuphunzira limene mukuŵerengali lakonzedwa kuti likuthandizeni kuchita zimenezi.

22 Mudzaona kuti bukuli lagaŵidwa m’zigawo zinayi mogwirizana ndi makhalidwe ofunika kwambiri anayi a Yehova: mphamvu, chilungamo, nzeru, ndi chikondi. Chigawo chilichonse chikuyamba ndi kufotokoza khalidwelo mwachidule. Mitu yotsatira ingapo m’chigawocho ikulongosola mmene Yehova amasonyezera khalidwe limenelo m’njira zosiyanasiyana.  M’chigawo chilichonse mulinso mutu umene ukusonyeza mmene Yesu anaperekera chitsanzo pa khalidwe limenelo, ndiponso mutu winanso womwe ukufotokoza mmene ifeyo tingasonyezere khalidwelo pa moyo wathu.

23, 24. (a) Fotokozani za bokosi lapadera lakuti “Mafunso Owasinkhasinkha.” (b) Kodi kusinkhasinkha kumatithandiza motani kuyandikira kwambiri kwa Mulungu?

23 Kuyambira ndi mutu uno, pali bokosi lapadera lotchedwa “Mafunso Owasinkhasinkha.” Mwachitsanzo, taonani bokosi lomwe lili patsamba 24. Sitinalinganize kuti mubwereze za m’mutu uno mwa malemba ndi mafunsowo. Koma cholinga chake n’chokuthandizani kulingalira pa mbali zina zofunika za nkhani imene tafotokozayi. Kodi ndi motani mmene mungagwiritsire ntchito bokosi limeneli mogwira mtima? Pezani lemba lililonse limene lasonyezedwa, ndiyeno ŵerengani mavesiwo mofatsa. Kenako ŵerengani funso lomwe likutsagana ndi lemba lililonse. Sinkhasinkhani pa mayankho ake. Mukhozanso kufufuza zowonjezereka. Dzifunseni mafunso enanso monga: ‘Kodi zimenezi zikundiuza chiyani ponena za Yehova? Kodi zikukhudza motani moyo wanga? Kodi ndingazigwiritse ntchito motani pothandiza ena?’

24 Kusinkhasinkha kotereku kungatithandize kuyandikira kwambiri kwa Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Baibulo limati timasinkhasinkha mumtima. (Salmo 19:14) Pamene tilingalira moyamikira chidziŵitso cha Mulungu chimene timaphunzira, chidziŵitsocho chimaloŵerera m’mitima yathu yophiphiritsa. Ndiyeno chimakhudza mmene timaganizira, chimasonkhezera mmene timamvera, ndipo pamapeto pake chimatilimbikitsa kuchitapo kanthu. Chikondi chathu pa Mulungu chimakula, ndipo chikondi chimenecho chimatilimbikitsa kufuna kumusangalatsa monga Bwenzi lathu lapamtima. (1 Yohane 5:3) Kuti tikhale ndi unansi woterewu, tifunika kudziŵa makhalidwe a Yehova ndi kachitidwe kake ka zinthu. Komabe choyamba tiyeni tikambirane mbali ina ya umunthu wa Mulungu omwe imapereka chifukwa champhamvu chomuyandikirira, chiyero chake.

^ ndime 3 N’zopatsa chidwi kuona kuti liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “ubwenzi” linagwiritsidwa ntchito pa Amosi 3:7, pamene pamati Ambuye Mfumu Yehova amaulula “chinsinsi” chake kwa atumiki ake, kuwadziŵitsiratu zimene akulingalira kudzachita.

^ ndime 12 Mwachitsanzo, Baibulo limanena za nkhope ya Mulungu, maso ake, makutu ake, mphuno yake, pakamwa pake, mkono wake, ndi mapazi ake. (Salmo 18:15; 27:8; 44:3; Yesaya 60:13; Mateyu 4:4; 1 Petro 3:12) Mawu ophiphiritsa ameneŵa sitiyenera kuwatenga ngati kuti akutchuladi ziwalo zomwe Mulungu ali nazo, monganso mmene sitingaonere choncho mawu ena onena za Yehova monga “Thanthwe” kaya “chikopa.”—Deuteronomo 32:4; Salmo 84:11.