Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 6

Yobu Anapitiriza Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika

Yobu Anapitiriza Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika

Satana anatsutsa zoti Yobu amatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, koma Yobu anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova

KODI pali munthu aliyense amene angakhalebe wokhulupirika kwa Mulungu ngati atayesedwa kwambiri ndiponso ngati zikuoneka kuti sakupindulapo chilichonse mwakuthupi chifukwa chokhala womvera? Zimene zinachitika pa moyo wa Yobu zinali zokhudza funso limeneli, ndipo iye analiyankha.

Pamene Aisiraeli anali ku Iguputo, Yobu amene anali m’bale wake wa Abulahamu, ankakhala m’dziko limene panopa limatchedwa Arabia. Nthawi ina angelo anasonkhana pamaso pa Mulungu kumwamba, ndipo Satana anali pomwepo. Pamaso pa angelo onsewo, Yehova anasonyeza kuti amakhulupirira mtumiki wake wokhulupirika Yobu. Ndipotu Yehova ananena kuti panalibe munthu wina amene ankamutumikira ndi mtima wosagawanika kuposa Yobu. Koma Satana ananena kuti Yobu amatumikira Mulungu chifukwa chakuti Mulunguyo anamudalitsa ndiponso amamuteteza. Satana ananena kuti ngati Yobu atalandidwa chilichonse chimene anali nacho, angatukwane Mulungu.

Mulungu analola kuti Satana awononge chuma cha Yobu, achititse kuti ana ake afe ndiponso kuti amudwalitse. Yobu sankadziwa kuti Satana ndi amene anachititsa mayesero amene ankakumana nawo, choncho sankamvetsa chifukwa chimene Mulungu analolera kuti iye azivutika. Komabe, Yobu sanatukwane Mulungu.

Anthu atatu amene ankaoneka ngati anzake a Yobu anabwera. M’masamba ambiri a buku la Yobu muli mawu a anthu amenewa. Iwo anali ndi maganizo olakwika ndipo anayesa kutsimikizira Yobu kuti Mulungu akumulanga chifukwa cha machimo enaake obisika amene iye anachita. Iwo ananenanso kuti Mulungu sasangalala ndi atumiki ake komanso sawakhulupirira. Koma Yobu anatsutsa maganizo awo olakwikawo, ndipo molimba mtima ananena kuti apitirizabe kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika mpaka imfa yake.

Koma Yobu analakwitsa zinthu chifukwa ankadziona ngati wolungama kwambiri. Choncho munthu wina wachinyamata wotchedwa Elihu amene ankamvetsera zonse zimene Yobu ndi anthu atatuwo ankakambirana, anadzudzula Yobu ndi anzakewo. Elihu anadzudzula Yobu chifukwa sanazindikire msanga kuti ulamuliro wa Yehova Mulungu ndiye woyenera kukwezedwa osati kukweza munthu wina aliyense. Komanso anadzudzula mwamphamvu anzake a Yobu aja omwe anali onyenga.

Kenako Yehova Mulungu analankhula ndi Yobu ndi kumuthandiza kuchotsa maganizo ake olakwikawo. Yehova anatchula zinthu zambiri zodabwitsa za m’chilengedwe pothandiza Yobu kuona kuti munthu ndi wamng’ono kwambiri pomuyerekezera ndi Mulungu. Yobu analandira modzichepetsa malangizo ochokera kwa Mulungu. Yehova, amene ndi “wachikondi chachikulu ndi wachifundo,” anachiritsa Yobu, anachulukitsa chuma chake kawiri poyerekezera ndi chimene anali nacho poyamba ndiponso anamudalitsa pomupatsa ana 10. (Yakobo 5:11) Popitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wosagawanika pa nthawi ya mayesero aakulu, Yobu anayankha bodza limene Satana ananena lakuti anthu sangakhale okhulupirika kwa Mulungu ngati atakumana ndi mayesero.

​—Nkhaniyi yachokera m’buku la Yobu.