Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 22

Atumwi Ankalalikira Mopanda Mantha

Atumwi Ankalalikira Mopanda Mantha

Mpingo wachikhristu unakula mofulumira kwambiri ngakhale kuti Akhristuwo ankazunzidwa

PATAPITA masiku 10 Yesu atakwera kumwamba, ophunzira ake pafupifupi 120 anasonkhana m’nyumba ina ku Yerusalemu. Imeneyi inali nthawi ya Chikondwerero cha Ayuda cha Pentekosite m’chaka cha 33 C.E. Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu ndipo unadzadza m’nyumba yonseyo. Kenako panachitika chozizwitsa chifukwa ophunzirawo anayamba kulankhula zinenero zachilendo. Zinthu zodabwitsa zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Mulungu anapatsa ophunzirawo mzimu woyera.

Panja pa nyumbayo panali gulu la anthu chifukwa alendo anabwera kuchokera m’madera ambiri osiyanasiyana kudzachita chikondwererocho. Gulu la anthulo linadabwa kwambiri litamva ophunzira a Yesu akulankhula bwinobwino m’zinenero zawo. Pofotokoza zimene zachitikazo, Petulo anagwira mawu a mneneri Yoweli omwe analosera kuti Mulungu ‘adzatsanulira’ mzimu wake pa anthu ndipo udzawathandiza kukhala ndi mphatso yotha kuchita zinthu zozizwitsa. (Yoweli 2:28, 29) Umenewu unali umboni wamphamvu wosonyeza kuti ophunzirawo alandira mzimu woyera ndipo zinali zoonekeratu kuti zinthu zasintha chifukwa Mulungu anasiya kukonda mwapadera mtundu wa Isiraeli ndipo anayamba kugwiritsa ntchito mpingo wachikhristu, umene unali utangoyamba kumene. Tsopano anthu amene ankafuna kutumikira Mulungu m’njira yovomerezeka, anafunika kukhala otsatira a Khristu.

Pa nthawiyi, atumwi ankazunzidwa kwambiri ndipo anthu amene ankadana nawo anawatsekera m’ndende. Koma usiku wa tsiku lomwelo, mngelo wa Yehova anatsegula zitseko za ndendeyo ndipo anauza atumwiwo kuti apitirize kulalikira, ndipo m’mawa wake, iwo anapitadi kukalalikira. Atumwiwo analowa m’kachisi ndipo anayamba kuphunzitsa uthenga wabwino wonena za Yesu. Atsogoleri achipembedzo amene sankagwirizana ndi zimene atumwiwo ankaphunzitsa, anakwiya kwambiri ndipo anawalamula kuti asiye kulalikira. Mopanda mantha atumwiwo anayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:28, 29.

Anthu anapitiriza kuzunza atumwiwo, moti Ayuda ena anaimba mlandu Sitefano woti wanyoza Mulungu ndipo anamupha pomuponya miyala. Mnyamata wina wa ku Tariso dzina lake Saulo, anavomereza kuti Sitefano aphedwe ndipo ankaonerera pamene anthu ankamuponya miyala. Kenako Saulo anapita ku Damasiko kuti akagwire aliyense wotsatira Khristu. Iye ali paulendowu, kuwala kochokera kumwamba kunamuzungulira ndipo anamva mawu akuti: “Saulo, Saulo n’chifukwa chiyani ukundizunza?” Saulo anachita khungu chifukwa cha kuwalako ndipo anafunsa kuti: “Ndinu ndani kodi?” Ndipo anamuyankha kuti: “Ndine Yesu.”—Machitidwe 9:3-5.

Patapita masiku atatu, Yesu anatumiza wophunzira wina dzina lake Hananiya kuti akathandize Saulo kuti ayambenso kuona. Saulo anabatizidwa ndipo anayamba kulalikira za Yesu molimba mtima. Kenako Saulo anayamba kudziwika ndi dzina lakuti mtumwi Paulo ndipo anakhala Mkhristu wachangu.

M’mbuyomu ophunzira a Yesu ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa Ayuda ndi Asamariya okha. Koma kenako mngelo anaonekera kwa Koneliyo, kapitawo wa asilikali achiroma amene anali woopa Mulungu, ndipo anamuuza kuti atumize anthu kuti akaitane mtumwi Petulo. Petulo anapitadi limodzi ndi anthu ena ndipo analalikira Koneliyo ndiponso anthu a m’banja lake. Pamene Petulo ankalankhula, mzimu woyera unafika pa anthuwo ngakhale kuti sanali Ayuda, ndipo mtumwiyo analamula kuti anthuwo abatizidwe m’dzina la Yesu. Pamenepa njira ya kumoyo wosatha inatseguka kwa anthu a mitundu yonse. Tsopano mpingo unali wokonzeka kulalikira uthenga wabwino kwa anthu amitundu yonse.

—Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 1:1–11:21.