Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 5

Mulungu Anadalitsa Abulahamu ndi Banja Lake

Mulungu Anadalitsa Abulahamu ndi Banja Lake

Mbadwa za Abulahamu zinadalitsidwa, ndipo Mulungu anateteza Yosefe ku Iguputo

YEHOVA ankadziwa kuti tsiku lina, Mwana wake amene ankamukonda kwambiri adzazunzidwa ndiponso adzaphedwa. Ulosi umene uli pa Genesis 3:15 umanena zimenezi. Kodi Mulungu anasonyeza bwanji anthu kuti imfa ya Mwana wakeyo idzakhala chinthu chamtengo wapatali kwambiri? M’Baibulo muli nkhani yofotokoza zimene zinachitikira Abulahamu ndi mwana wake, ndipo zimenezi zinali chithunzi cha zimene Mulungu adzachite. Mulungu anauza Abulahamu kuti apereke nsembe Isaki, mwana wake wamwamuna amene ankamukonda kwambiri.

Abulahamu anali ndi chikhulupiriro cholimba. Kumbukirani kuti Mulungu analonjeza kuti Mpulumutsi kapena Mbewu yolonjezedwa, idzachokera mwa Isaki. Abulahamu ankakhulupirira kuti Mulungu angaukitse Isaki ngati pangafunike kutero, choncho anali wokonzeka kupereka mwana wake nsembe pomvera zimene Mulungu anamuuza. Koma Abulahamu atatsala pang’ono kupha mwana wakeyo, mngelo wochokera kwa Mulungu anamuletsa. Mulungu anayamikira Abulahamu chifukwa ankafuna kupereka mwana wake nsembe mosanyinyirika ndipo anabwereza malonjezo amene anachita ndi mtumiki wake wokhulupirikayu.

Kenako, Isaki anabereka ana awiri aamuna, Esau ndi Yakobo. Yakobo anadalitsidwa chifukwa ankayamikira zinthu zauzimu mosiyana ndi Esau. Mulungu anasintha dzina la Yakobo n’kukhala Isiraeli, ndipo ana aamuna 12 a Isiraeli anakhala makolo a mafuko a Isiraeli. Koma kodi zinatheka bwanji kuti banja limenelo likule n’kukhala mtundu waukulu?

Zinthu zosiyanasiyana zinayamba kuchitika pamene ambiri mwa ana amenewo anayamba kuchitira nsanje Yosefe, mng’ono wawo. Iwo anam’gulitsa kuti akhale kapolo ndipo anthu amene anam’gulawo anapita naye ku Iguputo. Koma Mulungu anadalitsa Yosefe, yemwe anali mnyamata wokhulupirika komanso wolimba mtima. Yosefe anakumana ndi mavuto oopsa, koma kenako Farao, yemwe anali wolamulira wa dziko la Iguputo, anam’patsa udindo waukulu. Zimenezi zinachitika pa nthawi yoyenera chifukwa m’dziko limene Yakobo ankakhala munagwa njala ndipo iye anatumiza ana ake ena ku Iguputo kuti akagule chakudya. Pa nthawiyi n’kuti Yosefe ali ndi udindo waukulu woyang’anira zakudya zonse m’dziko la Iguputo. Abale akewo atakumana naye mosayembekezera, analapa ndipo iye anawakhululukira, kenako anakonza zoti anthu onse a m’banja lake asamukire ku Iguputo. Kumeneko anawapatsa malo abwino kwambiri ndipo anapitiriza kuchulukana. Yosefe ankadziwa kuti Mulungu ndi amene ankayendetsa zinthu kuti zichitike mwanjira imeneyo pofuna kukwaniritsa malonjezo ake.

Yakobo amene anali wokalamba, anakhala ku Iguputo masiku onse otsala a moyo wake ndipo anaona ana ake akuchulukana. Atatsala pang’ono kumwalira, Yakobo analosera kuti Mbewu yolonjezedwa, kapena kuti Mpulumutsi, adzakhala Wolamulira wamphamvu ndipo adzabadwira m’fuko la Yuda. Patapita zaka zambiri, Yosefe nayenso atatsala pang’ono kumwalira, ananeneratu kuti tsiku lina Mulungu adzatulutsa banja la Yakobo m’dziko la Iguputo.

—Nkhaniyi yachokera m’buku la Genesis chaputala 20 mpaka chaputala 50 komanso pa Aheberi 11:17-22.