Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 4

Mulungu Anachita Pangano ndi Abulahamu

Mulungu Anachita Pangano ndi Abulahamu

Abulahamu ankakhulupirira Mulungu ndiponso ankamumvera, chotero Yehova anamulonjeza kuti adzamudalitsa ndiponso adzachulukitsa mbewu yake

PANALI patapita zaka pafupifupi 350 chichitikireni Chigumula cha m’nthawi ya Nowa. Pa nthawiyi, Abulahamu ankakhala mumzinda wotchuka wotchedwa Uri, dera limene masiku ano kuli dziko la Iraq. Abulahamu anali ndi chikhulupiriro cholimba, koma tsiku lina chikhulupiriro chakecho chinayesedwa.

Yehova anauza Abulahamu kuti achoke m’dziko limene anabadwira ndi kusamukira kudziko lina, limene linali la Kanani. Abulahamu anamvera mosanyinyirika ndipo iye ndi mkazi wake Sara pamodzi ndi banja lonse, komanso Loti mwana wa m’bale wake, anayenda ulendo wautali ndipo anafika ku Kanani n’kuyamba kukhala m’mahema. Mu pangano limene Yehova anachita ndi Abulahamu, anamulonjeza kuti mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu, mabanja onse a padziko lapansi adzadalitsidwa kudzera mwa iyeyo, komanso kuti ana ake adzatenga dziko la Kanani kuti likhale lawo.

Mulungu anadalitsa Abulahamu ndi Loti, ndipo iwo anakhala ndi nkhosa komanso ng’ombe zambirimbiri. Abulahamu anali wosadzikonda ndipo analola kuti Loti asankhe dera limene ankafuna. Loti anasankha dera la chonde la mphepete mwa mtsinje wa Yorodano, ndipo iye anakhazikika mumzinda wa Sodomu. Koma anthu a ku Sodomu anali a khalidwe loipa ndipo Yehova ankawaona kuti ndi anthu ochimwa kwambiri.

Kenako Yehova Mulungu anatsimikizira Abulahamu kuti ana ake adzachuluka ngati nyenyezi za kumwamba, ndipo iye anakhulupirira lonjezo limeneli. Komabe, Sara, mkazi wokondedwa wa Abulahamu anakhalabe wopanda mwana. Kenako, Abulahamu ali ndi zaka 99 ndipo Sara ali ndi zaka pafupifupi 90, Mulungu anamuuza kuti iye ndi mkazi wakeyo adzakhala ndi mwana wa mwamuna. Monga mmene Mulungu ananenera, Sara anaberekadi Isaki. Abulahamu anali ndi ana enanso, koma Mpulumutsi amene Mulungu analonjeza m’munda wa Edeni, anali woti adzabadwa kudzera mwa Isaki.

Pa nthawiyi n’kuti Loti ndi banja lake akukhala mumzinda wa Sodomu, koma iye popeza anali wolungama, sankachita nawo makhalidwe oipa amene anthu a mumzindawu ankachita. Yehova ataganiza zoti awononge mzinda wa Sodomu, anatumiza angelo kuti akachenjeze Loti. Angelowo analimbikitsa Loti ndi banja lake kuti athawe mumzindawo ndipo asayang’ane m’mbuyo. Kenako Mulungu anagwetsa moto ndi sulufule mumzinda wa Sodomu ndiponso mzinda wapafupi wa Gomora, n’kuwononga anthu onse oipa. Loti ndi ana ake aakazi awiri anapulumuka koma mkazi wake anayang’ana m’mbuyo, mwina poganizira zinthu zimene anasiya mumzindawo. Iye anafa chifukwa sanamvere malangizo amene Mulungu anapereka kudzera mwa angelo aja.

—Nkhaniyi ikuchokera pa Genesis 11:10–19:38.