Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 11

Anawayenga Kuti Akhale Ndi Makhalidwe Abwino Potsanzira Mulungu Woyera

Anawayenga Kuti Akhale Ndi Makhalidwe Abwino Potsanzira Mulungu Woyera

CHOLINGA CHA MUTUWU

Mmene Mfumu yathandizira anthu ake kumvetsa ubwino wotsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino

Tayerekezani kuti mukulowa m’bwalo lakunja la kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova

1. Fotokozani zinthu zochititsa chidwi zimene Ezekieli anaona?

KODI mukanatani mukanaona zinthu zimene Ezekieli anaona zaka pafupifupi 2,500 zapitazo? Taganizirani izi: Mwafika pakachisi wokongola komanso wamkulu kwambiri. Mngelo wamphamvu akudikirira pakachisipo kuti akuonetseni bwinobwino kachisiyo. Kenako mukukwera masitepe 7 n’kufika pa limodzi mwa zipata zitatu za kachisiyo. Mukuchita chidwi kwambiri ndi zipatazi chifukwa ndi zazitali pafupifupi mamita 30. Mutangolowa mukuona zipinda za alonda. Mukuonanso zipilala pomwe pajambulidwa zithunzi zokongola za mitengo ikuluikulu ya kanjedza.​—Ezek. 40:1-4, 10, 14, 16, 22.

2. (a) Kodi masomphenya akachisi wauzimu amaimira chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.) (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zipata komanso zipinda za alonda za pakachisiyu?

2 Amenewa anali masomphenya a kachisi wauzimu. Ezekieli anafotokoza nkhani imeneyi mwatsatanetsatane moti nkhaniyi inayambira m’chaputala 40 mpaka 48 cha buku lake la ulosi. Kachisiyu akuimira dongosolo limene Yehova anakhazikitsa kuti anthu azitsatira pomulambira. Chilichonse chimene Ezekieli anaona m’masomphenyawa chingatithandize ifeyo polambira Mulungu m’masiku otsiriza ano. * Kodi zipata zimene zinali pamalo okwera zikutanthauza chiyani? Zikutikumbutsa kuti anthu amene amayamba kulambira nawo Yehova m’njira yovomerezeka ayenera kutsatira mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino zimene Mulungu anakhazikitsa. Zithunzi za mitengo ya kanjedza zikutanthauzanso zomwezi chifukwa nthawi zina m’Baibulo mitengo ya kanjedza imatchulidwa potanthauza khalidwe labwino. (Sal. 92:12) Nanga bwanji zipinda za alonda? Apa n’zoonekeratu kuti anthu amene safuna kutsatira mfundo za Mulungu samaloledwa kulowa m’kachisi wokongola ameneyu yemwe ndi njira yolambirira Mulungu imene imathandiza anthu kuti adzapeze moyo wosatha.​—Ezek. 44:9.

3. N’chifukwa chiyani otsatira a Khristu anafunika kupitirizabe kuyengedwa?

3 Kodi masomphenya a Ezekieli akwaniritsidwa motani? Monga mmene tinaonera m’mutu 2, Yehova anagwiritsa ntchito Yesu poyenga anthu ake kuyambira m’chaka cha 1914 mpaka kumayambiriro kwa 1919. Kodi kuyengako kunathera pompo? Ayi. M’zaka 100 zapitazi, Khristu wakhala akutetezera mfundo za makhalidwe abwino za Yehova. Chifukwa cha zimenezi, otsatira ake anafunika kupitirizabe kuyengedwa. Zimenezi zinali zofunika chifukwa anthu amene Khristu wakhala akuwasonkhanitsa kuti akhale otsatira ake akuchokera m’dziko loipali komanso chifukwa chakuti Satana akupitirizabe kusokoneza anthuwo kuti ayambirenso kuchita makhalidwe  oipa. (Werengani 2 Petulo 2:20-22.) Tiyeni tikambirane mmene Akhristu oona akhala akuyengedwera pang’onopang’ono. Tikambirana zinthu zitatu. Choyamba, tikambirana mmene anthu a Mulungu akhala akuyengedwera kuti akhale ndi makhalidwe abwino, kenako tiona zimene Yehova wachita kuti mpingo usadetsedwe, ndipo pomaliza tikambirana mfundo zothandiza mabanja.

Mmene Anthu a Mulungu Akhala Akuyengedwera

4, 5. Kodi Satana wakhala akugwiritsa ntchito njira iti, ndipo zotsatira zake zakhala zotani?

4 Nthawi zonse anthu a Yehova akhala akufunitsitsa kukhala ndi makhalidwe oyera. Choncho, akhala akutsatira malangizo alionse atsopano onena za makhalidwe abwino. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

5 Kugonana. Pamene Yehova ankalenga anthu ankafuna kuti kugonana kwa mwamuna ndi mkazi okwatirana kuzichitika moyenera komanso kuzikhala kosangalatsa. Koma Satana amafuna kuti anthu a Yehova azigwiritsa ntchito mphatso imeneyi molakwika n’cholinga chakuti akhumudwitse Mulungu. Satana anagwiritsanso ntchito njira imeneyi m’nthawi ya Balamu ndipo zinachititsa kuti anthu ambiri aphedwe. Njira imeneyi akuigwiritsanso ntchito kwambiri masiku otsiriza ano.​—Num. 25:1-3, 9; Chiv. 2:14.

6. (a) Kodi mu Nsanja ya Olonda munali lumbiro lotani ndipo linkagwiritsidwa ntchito bwanji? (b) N’chifukwa chiyani patapita nthawi anasiya kuligwiritsa ntchito? (Onaninso mawu a m’munsi.)

6 Pofuna kulepheretsa mapulani oipa a Satana, mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1908, munali lumbiro lomwe linali ndi mawu awa: “Ndikulonjeza kuti nthawi zonse komanso kwina kulikonse kumene ndingakhale ndidzachita zinthu mwaulemu kwa munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanga. Ndidzachita zimenezi kaya tili kwa awiri kapena pagulu.” * Ngakhale kuti anthu anali ndi ufulu wovomereza lumbiroli kapena ayi, anthu ambiri analivomereza ndipo anatumiza mayina awo kuti afalitsidwe mu magazini ya Zion’s Watch Tower. Ngakhale kuti lumbiroli linali lothandiza kwa anthu ambiri, patapita zaka zingapo zinaoneka kuti anthu ankangolumbira mwamwambo chabe, choncho anasiya kuligwiritsa ntchito. Komabe mfundo za makhalidwe abwino zimene zinachititsa kuti pakhale lumbiro limeneli zinkatsatiridwabe.

7. Kodi Nsanja ya Olonda ina imene inatuluka m’chaka cha 1935 inafotokoza za vuto lanji, nanga inatsindika mfundo yotani pa nkhaniyi?

7 Satana anayamba kuukira kwambiri anthu a Mulungu. Nsanja ya Olonda ya March 1, 1935, inafotokoza mosapita m’mbali za vuto limene linkasokoneza anthu a Mulungu. Ena ankaganiza kuti akhoza kumachita makhalidwe oipa akakhala kwaokha bola ngati akugwira nawo ntchito yolalikira. Nsanja ya Olonda imeneyi inanenanso kuti: “Chofunika kwa Mkhristu si kungogwira nawo ntchito yolalikira basi. Mboni za Yehova zimaimira Yehova ndipo ndi udindo wawo kuonetsetsa kuti zochita zawo zikusonyezadi kuti akuimira Yehova komanso Ufumu wake.” Kenako nkhaniyi inapereka malangizo omveka bwino okhudza banja komanso nkhani zogonana, zomwe zinathandiza anthu a Mulungu ‘kuthawa dama.’​—1 Akor. 6:18.

8. N’chifukwa chiyani Nsanja ya Olonda inafotokoza mobwerezabwereza tanthauzo loyenera la mawu achigiriki omwe amamasuliridwa kuti dama?

8 Zaka zaposachedwapa Nsanja ya Olonda yakhala ikufotokoza mobwerezabwereza tanthauzo loyenera la mawu achigiriki akuti por·neiʹa omwe amamasuliridwa kuti dama. Mawu amenewa samangotanthauza kugonana kwenikweniko. Mawu akuti por·neiʹa amatanthauzanso makhalidwe onse onyansa ngati amene amachitika  m’nyumba za mahule. Kudziwa tanthauzo la mawuwa kwateteza Akhristu ambiri kuti asamachite nawo makhalidwe otayirira amene anthu ambiri akuchita masiku ano.​—Werengani Aefeso 4:17-19.

9, 10. (a) Kodi Nsanja ya Olonda ina imene inatuluka mu 1935 inafotokoza za khalidwe loipa liti? (b) Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kamwedwe koyenera ka mowa?

9 Kumwa kwambiri mowa. Nsanja ya Olonda ya March 1, 1935, inafotokozanso mfundo ina yofunika. Inati: “Zaonekanso kuti anthu ena akumagwira ntchito yolalikira komanso ntchito zina za gulu atamwa mowa. Koma kodi Malemba amavomereza kumwa mowa pa zochitika ziti? Kodi ndi zoyenera kumwa mowa pamene ukukagwira ntchito za gulu la Ambuye?”

10 Zimene magaziniyo inanena poyankha mafunso amenewa zinasonyeza kamwedwe koyenera ka mowa kamene Mawu a Mulungu amavomereza. Baibulo silimaletsa kumwa mowa pang’ono koma limaletseratu kuledzera. (Sal. 104:14, 15; 1 Akor. 6:9, 10) Pofuna kuwachenjeza kuti asamagwire ntchito zopatulika atamwa mowa, atumiki a Mulungu akhala akukumbutsidwa za nkhani ya ana a Aroni. Mulungu anapha ana a Aroni atayatsa moto wosaloledwa paguwa la Mulungu. Kenako nkhaniyi imafotokoza chimene mwina chinachititsa ana a Aroni kuti achite zinthu zosayenera. Tikutero chifukwa chakuti Mulungu anapereka lamulo loletsa wansembe aliyense kuti asamachite utumiki wake wopatulika atamwa mowa. (Lev. 10:1, 2, 8-11) Potsatira mfundo imeneyi, otsatira a Khristu masiku ano sachita utumiki wawo wopatulika atamwa mowa.

11. Kodi anthu a Mulungu athandizidwa bwanji chifukwa cholandira malangizo pa nkhani ya kumwa mowa mwauchidakwa?

11 Zaka zaposachedwapa, otsatira a Khristu akhala akuthandizidwa kuti asamamwe mowa mwauchidakwa, komwe ndi kumwa kwambiri komanso kulephera kuchita zinthu popanda kumwa mowa. Chifukwa cholandira chakudya chauzimu pa nthawi yake, anthu ambiri akwanitsa kuthetsa vuto limeneli moti zinthu zayamba kuyenda bwino pa moyo wawo ndipo malangizo amenewa athandizanso ena kuti asagwere m’vuto limeneli. Sitiyenera kulola kuti kumwa mowa kusokoneze moyo wathu, banja lathu komanso mwayi wathu wolambira Yehova m’njira yoyenera.

“Sitingaganize n’komwe kuona Ambuye wathu akuika m’kamwa chinthu china chilichonse chodetsa kapena akununkha fungo la fodya.”​—C. T. Russell

12. Kodi atumiki a Khristu ankaona bwanji kusuta fodya masiku otsiriza asanayambe?

12 Kusuta fodya. Atumiki a Khristu anayamba kuona kuti kusuta fodya n’kolakwika ngakhale masiku otsiriza asanayambe. Zaka zingapo zapitazi m’bale wina wachikulire, dzina lake Charles Capen, anafotokoza zimene zinachitika atakumana koyamba ndi M’bale Charles Taze Russell chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800. Pa nthawi imeneyo n’kuti M’bale Capen ali ndi zaka 13 ndipo iye ndi abale ake atatu anakhala polowera m’Nyumba ya Baibulo, ku Allegheny, Pennsylvania. Pamene M’bale Russel ankadutsa pomwe panali anyamatawo, anawafunsa kuti: “Kodi anyamata inu mukusuta fodya? Ndikumva fungo la utsi wa fodya.” Iwo anamutsimikizira kuti sankasuta fodya. Komabe zimene anawafunsazo zinawachititsa kuzindikira kuti m’baleyo ankaona kuti kusuta fodya n’kolakwika. Pofotokozera lemba la 2 Akorinto 7:1, Nsanja ya Olonda ya August 1, 1895, inafotokoza zimene M’bale Russell ananena kuti: “Sindikuona kuti kugwiritsa ntchito fodya mwanjira ina iliyonse kungalemekezetse Mulungu kapena kupindulitsa wosutayo. . . . Sitingaganize n’komwe kuona Ambuye wathu akuika m’kamwa chinthu china chilichonse chodetsa kapena akununkha fungo la fodya.”

13. Kodi Akhristu anayengedwa bwanji m’chaka cha 1973?

 13 Mu 1935, Nsanja ya Olonda ina inanena kuti fodya ndi “chinthu chonyansa” ndipo aliyense wotafuna kapena kusuta fodya sangaloledwe kupitiriza kutumikira pa Beteli kapena kuimira gulu la Mulungu pogwira ntchito yaupainiya kapena kutumikira monga woyendayenda. M’chaka cha 1973 panatulukanso malangizo ena atsopano. Nsanja ya Olonda ya June 1 inanena kuti Mkhristu aliyense wa Mboni za Yehova sangapitirize kuonedwa monga chitsanzo chabwino mumpingo ngati akupitirizabe khalidwe lowononga moyo komanso losonyeza kupanda chikondi limeneli. Anthu amene anakana kusiya kugwiritsa ntchito fodya anachotsedwa. * Apanso Khristu anayenga otsatira ake.

14. Fotokozani maganizo a Mulungu pa nkhani ya magazi komanso zimene zinachititsa kuti anthu ambiri ayambe kuthiridwa magazi.

14 Kugwiritsa ntchito magazi molakwika. M’nthawi ya Nowa, Mulungu ananena kuti kudya magazi n’kulakwa. Anaika lamulo limeneli m’Chilamulo chomwe mtundu wa Isiraeli unkatsatira ndipo anauzanso anthu a mumpingo wachikhristu kuti “apewe . . . magazi.” (Mac. 15:20, 29; Gen. 9:4; Lev. 7:26) Koma sizodabwitsa kuona kuti masiku ano Satana anapeza njira yochititsa anthu ambiri kuti azinyalanyaza mfundo ya Mulungu imeneyi. M’zaka za m’ma 1800, madokotala ankangoyeserera kuthira anthu magazi koma atazindikira kuti pali magulu a magazi, madokotala ambiri anayamba kuona kuti kuthira anthu magazi ndi njira yabwino kwambiri. Mu 1937, madokotala anayamba kutenga anthu magazi n’kumawasunga ndipo nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inachititsa kuti anthu ambiri athiridwe magazi. Kenako, mayiko ambiri padziko lonse anayamba kuthira anthu magazi akadwala.

15, 16. (a) Kodi Mboni za Yehova zinkaona bwanji nkhani yothiridwa magazi? (b) Kodi otsatira a Khristu alandira thandizo lotani pa nkhani yothiridwa magazi komanso kulandira thandizo losagwiritsa ntchito magazi, nanga zotsatira zake zakhala zotani?

15 M’chaka cha 1944, Nsanja ya Olonda ina inanena kuti kuthiridwa magazi ndi njira imodzi yodyera magazi. M’chaka chotsatira panatuluka malangizo amene anafotokoza momveka bwino mfundo ya m’Malemba imeneyi komanso kulimbikitsa Akhristu kupewa magazi. Pofika m’chaka cha 1951, panatuluka mafunso ndi mayankho amene anafalitsidwa n’cholinga chothandiza anthu a Mulungu kuti azikambirana bwinobwino ndi madokotala. Padziko lonse, otsatira a Khristu okhulupirika ankasonyeza kulimba mtima ngakhale pamene anthu ankawanyoza, kuwachitira zankhanza komanso kuwazunza. Komabe Khristu anapitiriza kutsogolera gulu lake kuti lizipereka thandizo loyenerera pa nkhaniyi. Gulu linafalitsa timabuku ndi nkhani zofufuzidwa bwino komanso zosavuta kumva.

16 Mu 1979, akulu ena anayamba kuyenda m’zipatala n’cholinga choti azithandiza madokotala ambiri kumvetsa mmene timaonera nkhani ya magazi komanso zifukwa za m’Malemba zimene zimatichititsa kuona choncho. Anawathandizanso kudziwa njira zina zomwe angagwiritse ntchito m’malo moika anthu magazi. Mu 1980, akulu a m’mizinda 39 ya ku United States analandira maphunziro apadera pa ntchito imeneyi. Kenako Bungwe Lolamulira linavomereza kuti Makomiti Olankhulana ndi Achipatala akhazikitsidwe padziko lonse lapansi. Kodi kuchita zimenezi kwathandiza? Masiku ano madokotala ambiri, kuphatikizapo madokotala amene amapanga anthu opaleshoni, akuthandiza bwinobwino odwala omwe ndi a Mboni ndipo amalemekeza maganizo a wodwalayo  akasankha thandizo losagwiritsa ntchito magazi. Panopa zipatala zambiri zayamba kuthandiza anthu popanda kugwiritsa ntchito magazi ndipo zipatala zina zimaona kuti imeneyi ndi njira yabwino kwambiri kuposa njira yogwiritsa ntchito magazi. Kodi sizosangalatsa kuona mmene Yesu watetezera otsatira ake kuti asadetsedwe ndi Satana?​—Werengani Aefeso 5:25-27.

Panopa zipatala zambiri zayamba kuthandiza anthu popanda kugwiritsa ntchito magazi ndipo zipatala zina zimaona kuti imeneyi ndi njira yabwino kwambiri kuposa njira yogwiritsa ntchito magazi

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mmene Khristu wakhala akuyengera otsatira ake?

17 Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi timayamikira mmene Khristu wakhala akuyengera otsatira ake komanso kuwaphunzitsa kuti azitsatira mfundo zapamwamba za Yehova?’ Ngati timatero, tizikumbukira kuti Satana akufunitsitsa kuti tisamatsatire mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino n’cholinga choti ubwenzi wathu ndi Yehova komanso Yesu usokonekere. Pofuna kutithandiza kuti tisamayendere maganizo a Satana, gulu la Yehova limatikumbutsa komanso kutichenjeza mwachikondi za makhalidwe oipa a m’dzikoli. Choncho, tiyeni tipitirize kukhala tcheru, kumvera ndiponso kutsatira malangizo othandiza amene timalandira.​—Miy. 19:20.

Kuteteza Mpingo Kuti Usadetsedwe

18. Kodi masomphenya a Ezekieli amatikumbutsa mfundo iti ponena za anthu amene amasankha mwadala kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo zapamwamba za Mulungu?

18 Mbali yachiwiri imene Khristu anayengera anthu ake kuti akhale ndi makhalidwe abwino ndi kuika malangizo oteteza mpingo kuti ukhale woyera. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amene amasankha kudzipereka kwa Mulungu komanso kuvomereza  mfundo zamakhalidwe za Yehova sapitiriza kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene anasankhazo. Pakapita nthawi anthu amenewa amasintha ndipo amasankha mwadala kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo zamakhalidwe abwino. Kodi mpingo umachita chiyani ndi anthu oterewa? Yankho la funso limeneli tingalipeze m’masomphenya a kachisi wauzimu amene Ezekieli anaona, amene tawatchula kumayambiriro kwa mutuwu. Kumbukirani zipata zimene zinali pamalo okwera zija. Pachipata chilichonse panali zipinda za alonda amene ankalondera kachisi. Alonda amenewa ayenera kuti ankaletsa munthu aliyense “wosachita mdulidwe wa mtima” kuti asalowe m’kachisimo. (Ezek. 44:9) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu okhawo amene amayesetsa kutsatira mfundo za Yehova zoyera za makhalidwe abwino ndi amene amapatsidwa mwayi wolambira Mulungu. Choncho masiku anonso, mwayi wocheza komanso kuchita zinthu zauzimu ndi Akhristu ena sumaperekedwa kwa aliyense.

19, 20. (a) Kodi Khristu wakhala akuthandiza bwanji otsatira ake kumvetsa bwino mfundo zimene ayenera kutsatira poweruza munthu amene wachita tchimo lalikulu? (b) Kodi ndi zifukwa zikuluzikulu zitatu ziti zimene zimachititsa kuti munthu yemwe sakulapa achotsedwe mumpingo?

19 M’chaka cha 1892, Nsanja ya Olonda ina inanena kuti ndi “udindo wathu (monga Akhristu) kuchotsa mumpingo aliyense amene amatsutsa mfundo yoti Khristu anapereka moyo wake nsembe [malipiro okwanira ndendende] m’malo mwa onse, kaya munthuyo wachita kunena kapena wangosonyeza zimenezi mwa zochita zake.” (Werengani 2 Yohane 10.) Pofotokoza za anthu amene akupitirizabe kuchita makhalidwe oipa, buku lakuti The New Creation limene linatuluka m’chaka cha 1904, linanena kuti anthu amenewa ndi oopsa chifukwa akhoza kusokoneza mpingo. Nthawi imeneyo mpingo wonse unkaweruza nawo milandu munthu akachita tchimo lalikulu ndipo mpingo wonse unkasankha zoyenera kuchita ndi anthu amenewo. Komabe zimenezi sizinkachitika kawirikawiri. Mu 1944, Nsanja ya Olonda ina inasonyeza kuti abale audindo okha ndi amene ayenera kusamalira nkhani zimenezi. Ndipo m’chaka cha 1952, mfundo zochokera m’Baibulo zimene abale ayenera kutsatira poweruza nkhani ngati zimenezo zinafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda. Magaziniyi inafotokozanso momveka bwino kuti chifukwa chachikulu chochotsera munthu yemwe sakulapa ndi kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera.

20 Kuyambira nthawi imeneyo, Khristu wakhala akuthandiza otsatira ake kumvetsa bwino mfundo zimene ayenera kutsatira poweruza munthu amene wachita tchimo lalikulu. Akulu achikhristu amaphunzitsidwa mmene angaweruzire nkhani zimenezi moimira Yehova. Iwo amayenera kuchita zinthu mwachifundo komanso mwachilungamo. Masiku ano tikudziwa bwino kuti pali zifukwa zikuluzikulu zitatu zomwe zimachititsa kuti munthu yemwe sakulapa achotsedwe mumpingo: (1) kuteteza dzina la Yehova kuti lisanyozedwe, (2) kuteteza mpingo kuti anthu ena asatengere khalidwe loipalo, komanso (3) ngati ndi zotheka, kuthandiza wolakwayo kuti alape.

21. Kodi dongosolo lochotsa anthu mumpingo lathandiza bwanji anthu a Mulungu?

21 Dongosolo lochotsa mumpingo anthu amene sakulapa lakhala lothandiza kwambiri kwa otsatira a Khristu masiku ano. Kalekale ku Isiraeli, anthu ochita zoipa nthawi zambiri ankasokonezanso anthu ena moti nthawi zina oipawo ankachuluka kuposa anthu amene ankakonda Yehova ndipo ankafuna kuchita zinthu zabwino.  Zimenezi zinkachititsa kuti mtundu wonse unyozetse dzina la Yehova komanso kuti Yehova asiye kuukonda. (Yer. 7:23-28) Koma masiku ano, anthu amene Yehova amawaona kuti ndi anthu ake ndi ochokera m’mitundu yonse ya anthu osati mtundu umodzi wokha. Kuti munthu akhale nawo m’gulu limeneli ayenera kukhala wokonda zinthu zauzimu. Chifukwa chakuti anthu osafuna kulapa amachotsedwa, Satana sangawagwiritse ntchito kuti asokoneze komanso kudetsa mpingo wa Mulungu. Zinthu zoipa zimene anthuwa amachita zikhoza kungosokoneza anthu ochepa chabe. Koma monga gulu, ndife otsimikiza kuti Yehova akupitirizabe kutikonda. Paja Yehova analonjeza kuti: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.” (Yes. 54:17) Koma kodi timamvera mokhulupirika akulu omwe ali ndi udindo waukulu woweruza nkhani mumpingo?

Kulemekeza Amene Amapangitsa Banja Lililonse Kukhala ndi Dzina

22, 23. (a) N’chifukwa chiyani timachita chidwi tikamawerenga za atumiki a Mulungu amene anakhalapo kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti atumiki a Mulungu ankafunika kuthandizidwa pa nkhani ya banja?

22 Mbali yachitatu imene otsatira a Khristu apindula chifukwa cha kuyengedwa kumene kwakhala kukuchitika ndi yokhudza mabanja. Kodi kaonedwe kathu ka mabanja kasintha zaka zapitazi? Inde. Mwachitsanzo, tikamawerenga nkhani za atumiki a Mulungu amene anakhalapo kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, timachita chidwi komanso kugoma ndi mtima wodzimana umene anali nawo. Timayamikira kwambiri tikaona mmene ankakondera utumiki kuposa china chilichonse pa moyo wawo. Komabe, timaonanso kuti zinthu zina sizinkayenda bwino kwenikweni. N’chifukwa chiyani tikutero?

23 Nthawi zambiri abale okwatira ankapita okha kukagwira ntchito zina zampingo kapena kukagwira ntchito yoyendera mipingo kutali ndi kwawo ndipo ankakhala komweko kwa miyezi yambiri asanabwerere kwawo. Nthawi zina anthu ankauzidwa kuti sibwino kukwatira ndipo ankauzidwa zimenezi mwamphamvu kuposa mmene Baibulo limanenera. Pa nthawi imeneyo mfundo zothandiza mabanja kuti akhale olimba sizinkafalitsidwa kwenikweni. Koma kodi mmenemu ndi mmene zinthu zilili masiku ano? Ayi.

Mkhristu safunika kulephera kusamalira banja lake chifukwa chakuti akuchita utumiki

24. Kodi Khristu anathandiza bwanji atumiki ake okhulupirika kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya banja?

24 Masiku ano, Mkhristu safunika kulephera kusamalira banja lake chifukwa chakuti akuchita utumiki. (Werengani 1 Timoteyo 5:8.) Komanso Khristu waonetsetsa kuti otsatira ake okhulupirika akulandira malangizo othandiza komanso oyenera ochokera m’Malemba pa nkhani ya mabanja. (Aef. 3:14, 15) M’chaka cha 1978, kunatuluka buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Patapita zaka 18, kunatulukanso buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Kuwonjezera pamenepo, mu Nsanja ya Olonda mwakhala mukutuluka nkhani zothandiza anthu apabanja kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo kuti azikondana.

25-27. Pofuna kuthandiza ana a misinkhu yosiyanasiyana, kodi kapolo wokhulupirika wakhala akuchita zotani?

25 Pa zaka zimenezi pakhala pakutulukanso nkhani zambiri zothandiza ana. Kwa zaka zambiri gulu la Yehova lakhala likutulutsa zinthu zambiri zothandiza ana amisinkhu yosiyanasiyana, koma masiku ano zinthu zimenezi zikutulutsidwa zambiri kuposa kale. Mwachitsanzo, m’magazini ya The Golden Age munkakhala nkhani  za mutu wakuti “Juvenile Bible Study” (Phunziro la Baibulo la Ana) kuyambira mu 1919 mpaka mu 1921. Ndipo m’chaka cha 1920, kunatuluka kabuku kamutu wakuti The Golden Age ABC ndipo mu 1941 kunatuluka buku lakuti Ana. M’zaka za m’ma 1970, kunatuluka mabuku a Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkulu’yo, Your Youth—Getting the Best out of It, ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. M’chaka cha 1982, mu Galamukani! munayamba kutuluka nkhani za mutu wakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” ndipo nkhani zimenezi ndi zimene zinaphatikizidwa n’kupanga buku limene linatuluka mu 1989 lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza (lomwe masiku ano timati Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa).

Ana anasangalala kulandira kabuku kamutu wakuti Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo kamene kanatuluka pamsonkhano wachigawo ku Germany

26 Masiku ano tili ndi mabuku awiri a mutu wakuti Zimene Achinyamata Amafunsa, ndipo ali ndi mfundo zogwirizana ndi moyo wa achinyamata a masiku ano. Nkhani za mutu wakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” zimatulukabe ndipo zimapezeka pa webusaiti yathu ya jw.org. Tilinso ndi buku la mutu wakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Pa webusaiti yathu pali zinthu zambiri zothandiza achinyamata, monga makadi a anthu otchulidwa m’Baibulo, nkhani zothandiza ana a misinkhu yosiyanasiyana pophunzira Baibulo, mavidiyo, zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo komanso  nkhani za m’Baibulo zothandiza ana osapitirira zaka zitatu. Apa n’zoonekeratu kuti Khristu amakondabe ana ngati mmene anachitira pamene ananyamula ana aang’ono m’manja mwake pa nthawi imene anali padziko lapansi. (Maliko 10:13-16) Iye amafuna kuti ana amene tili nawo m’gululi aziona kuti amakondedwa ndiponso akudyetsedwa bwino mwauzimu.

27 Yesu amafunanso kuti ana azikhala otetezeka. Zinthu m’dziko zaipa kwambiri ndipo zachititsa kuti ana ambiri azichitiridwa chipongwe kapena nkhanza. Choncho, gulu lakhala likufalitsa nkhani zomveka bwino zothandiza makolo kuti azitetezera ana awo n’cholinga choti zinthu zimenezi zisawachitikire. *

28. (a) Malinga ndi masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

28 Kodi sizolimbikitsa kuona mmene Khristu wakhala akuyengera otsatira ake powaphunzitsa kulemekeza komanso kutsatira mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino zimene Yehova amapereka? Taganiziraninso za kachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya. Kumbukirani kuti kachisi uja anali ndi zipata zomwe zinali pamalo okwera. N’zoona kuti kachisi ameneyu ndi wauzimu. Komabe, kodi ifeyo timaona kuti kachisi ameneyu ndi weniweni? Sikuti timalowa m’kachisi ameneyu pongopita ku Nyumba ya Ufumu, kuwerenga Baibulo kapena kulowa mu utumiki. Ntchito zimenezi ndi zooneka ndi maso ndipo ngakhale munthu wonyenga akhoza kuchita zimenezi komabe sitinganene kuti walowa m’kachisi wa Yehova. Koma ngati pochita zimenezi titamayesetsanso kutsatira mfundo zapamwamba za Yehova ndiponso kulambira nawo Yehova ndi zolinga zabwino, ndiye kuti talowa m’kachisi wopatulika kwambiri ameneyu ndipo tikutumikira mkati mwake. Kachisi ameneyu akuimira dongosolo limene Yehova Mulungu anakhazikitsa kuti anthu azitsatira pomulambira. Nthawi zonse tiyenera kuona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kutumikira malo amenewa. Tiyenera kupitiriza kuyesetsa kusonyeza makhalidwe oyera a Yehova ndipo tingachite zimenezi ngati titapitirizabe kutsatira mfundo zake zolungama.

^ ndime 2 M’chaka cha 1932, Buku Lachiwiri la Vindication linafotokoza koyamba kuti ulosi wa m’Baibulo wonena za kubwezeretsa anthu a Mulungu kudziko lawo ukukwaniritsidwanso masiku ano, osati pa Aisiraeli akuthupi koma pa Isiraeli wauzimu. Maulosi amenewa ankanena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera. Nsanja ya Olonda ya March 1, 1999, inafotokoza kuti masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona unali ulosi wonena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera ndipo kukwaniritsidwa kwake kwenikweni kukuchitika masiku otsiriza ano.

^ ndime 6 Lonjezoli linkaletsa mwamuna ndi mkazi kukhala awiriwiri m’chipinda pokhapokha chitseko chikhale chotsekula kwambiri kapena ngati anthuwo ndi banja kapenanso ndi apachibale chapafupi. Kwa zaka zingapo, anthu a pa Beteli ankaloweza lonjezo limeneli n’kumalinena tsiku lililonse pa kulambira kwa m’mawa.

^ ndime 13 Kugwiritsa ntchito fodya molakwika kukuphatikizapo kusuta, kutafuna kapena kulima.

^ ndime 27 Mwachitsanzo, onani mutu 32 m’buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso; onaninso masamba 3-11 mu Galamukani! ya October 2007!.