Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 4

Anasangalatsa Bambo Ake Komanso Yehova

Anasangalatsa Bambo Ake Komanso Yehova

Kodi Yefita akumulonjeza chiyani Yehova?

Chaka chilichonse anzake a mwana wa Yefita ankapita kuchihema kukamuona

Kodi wamuona mtsikana ali pachithunzipa?—Ameneyu ndi mwana wa Yefita. Baibulo silitiuza dzina lake koma tikudziwa kuti anasangalatsa bambo ake komanso Yehova. Tiye tikambirane za mtsikanayu komanso bambo ake.

Yefita anali munthu wabwino ndipo nthawi zambiri ankaphunzitsa mwana wakeyu za Yehova. Anali munthu wamphamvu komanso mtsogoleri wabwino. Ndiyeno Aisiraeli anamupempha kuti awatsogolere pokamenya nkhondo.

Yefita anapemphera kwa Mulungu kuti awathandize kupambana nkhondoyo. Iye analonjeza kuti ngati atapambana, adzapereka kwa Yehova munthu amene adzakhale woyamba kumuchingamira pochoka kunkhondoko. Munthu ameneyu akanayenera kukakhala komanso kugwira ntchito ku chihema cha Mulungu  kwa moyo wake wonse. Chihema chinali chitenti kumene anthu a nthawi imeneyo ankapitako kukalambira Mulungu. Ndiyeno Yefita anapambanadi nkhondo ija. Kodi ukudziwa munthu amene anali woyamba kudzamuchingamira?—

Anali mwana wake. Yefita anali ndi mwana mmodzi yekhayo ndipo malinga ndi zimene analonjeza zija, anayenera kumupereka kwa Yehova. Yefita anadandaula kwambiri ndi zimenezi. Koma anayenera kumuperekabe chifukwa anali atalonjeza. Nthawi yomweyo, mtsikanayo ananena kuti: ‘Bambo, munalonjeza kwa Yehova ndiye musasinthe zimene munalonjezazo.’

Mwana wa Yefita anachita zimene bambo ake analonjeza ngakhale kuti zinali zovuta

Nayenso mwana wa Yefita anadandaula chifukwa chodziwa kuti akapita kuchihemako sakakhalanso ndi mwayi wokwatiwa komanso kukhala ndi ana. Koma analola kupita chifukwa ankafuna kuti zimene bambo ake analonjeza zichitike ndiponso ankafuna kusangalatsa Yehova. Iye anaona kuti kusangalatsa bambo ake komanso Yehova kunali kofunika kwambiri kuposa kukwatiwa kapena kukhala ndi ana. Ndiyeno mwana wa Yefita anachoka kwawo n’kumakakhala kuchihema kwa moyo wake wonse.

Kodi ukuganiza kuti bambo ake komanso Yehova anasangalala ndi zimene anachitazo?— Inde. Ngati nawenso uzimvera komanso kukonda Yehova, makolo ako ndiponso Yehova adzasangalala nawe kwambiri.