Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 1

Chinsinsi Chimene Tonsefe Timafuna Titachidziwa

Chinsinsi Chimene Tonsefe Timafuna Titachidziwa

Kodi winawake anakuuzako nkhani ya chinsinsi?— * Baibulo limanena kuti pali nkhani inayake yachinsinsi ndipo limati nkhani imeneyi ndi “chinsinsi chopatulika.” Chinsinsichi ndi chopatulika chifukwa ndi chochokera kwa Mulungu. Komanso nkhaniyi ndi chinsinsi chifukwa anthu sankaidziwa. Ngakhalenso angelo ankafuna kudziwa nkhani imeneyi. Kodi nawenso ukufuna kudziwa chinsinsi chimenechi?—

Kodi ukuganiza kuti angelo ankafuna kudziwa chiyani?

Kale kwambiri Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi oyamba. Mayina awo anali Adamu ndi Hava. Mulungu anawapatsa malo okhala abwino komanso okongola ndipo anawatchula kuti munda wa Edeni. Ngati Adamu ndi Hava akanamvera Mulungu, iwo pamodzi ndi ana awo akanachititsa kuti dziko lonse likhale ngati munda wa Edeni. Ndipo akanakhala m’Paradaiso mpaka kalekale. Koma kodi ukukumbukira zimene Adamu ndi Hava anachita?—

Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, n’chifukwa chake ifeyo sitili m’paradaiso. Koma Mulungu ananena kuti adzasintha dziko lonse kuti likhalenso lokongola ndipo aliyense azidzakhala mosangalala mpaka kalekale. Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti zimenezi zitheke? Kwa zaka zambirimbiri anthu sankadziwa yankho la funso limeneli chifukwa inali nkhani ya chinsinsi.

Yesu atabwera padziko lapansi anaphunzitsa anthu zinthu zambiri zokhudza chinsinsi chimenechi. Zimene iye anaphunzitsa zinasonyeza kuti chinsinsichi ndi Ufumu wa Mulungu chifukwa ndi umene udzasinthe dzikoli kukhala paradaiso. Yesu anauza anthu kuti azipempherera Ufumu umenewu kuti ubwere.

Kodi iweyo ukusangalala kuti wadziwa chinsinsi chimenechi?— Anthu amene amamvera Yehova ndi amene adzakhale m’Paradaiso. Baibulo limatiuza za anthu ambirimbiri amene anamvera Yehova. Kodi ungakonde kuphunzira nkhani za anthu amenewa?— Tiye tione ena mwa anthu amenewa komanso zimene tingachite kuti titengere chitsanzo chawo.

^ ndime 3 Mu nkhani iliyonse muli mafunso ndipo kumapeto kwake kuli chizindikiro ichi (—). Mukafika pamenepa muziima kaye kuti mwanayo ayankhe.