Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mutu 47

Zimene Zikutidziwitsa Kuti Aramagedo Ili Pafupi

Zimene Zikutidziwitsa Kuti Aramagedo Ili Pafupi

IWE umachidziŵa chizindikiro, kodi si choncho?— Mu Mutu 46 tinaŵerenga za chizindikiro chimene Mulungu anapereka kusonyeza kuti sadzawononganso dziko lapansi ndi chigumula. Ndiponso, atumwi anafunsapo za chizindikiro chimene chikawathandiza kudziŵa pamene Yesu adzabweranso ndi kuti dzikoli lili pafupi kutha.—Mateyu 24:3.

Popeza kuti Yesu akakhala wosaoneka kumwamba, anthu anafunika chizindikiro chooneka chosonyeza kuti iye wayamba kulamulira. Choncho Yesu anafotokoza zinthu zimene ophunzira ake anayenera kuyang’anira padziko lapansi pano. Zinthu zimenezo zikadzachitika, ndiye kuti iye adzakhala atabwera ndipo adzayamba kulamulira kumwamba monga Mfumu.

Pofuna kuphunzitsa ophunzira ake mfundo yoti afunika kukhala maso, Yesu anawauza kuti: ‘Onani mkuyu, ndi mitengo yonse; pamene iphukira,  mwa kuipenya mumazindikira panokha kuti dzinja lili pafupi pomwepo.’ Munthu umadziŵa kuti dzinja lili pafupi. Ndipo ungadziŵenso kuti Armagedo ili pafupi mwa kuona zinthu zimene Yesu ananena zikuchitika.—Luka 21:29, 30.

Kodi Yesu anali kuphunzitsa mfundo yotani polankhula za mkuyu?

Patsamba lino ndi lotsatira, tiona zithunzi za zimene Yesu anati zidzakhala zina mwa zinthu zimene zidzapanga chizindikiro chosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Zinthu zonsezi zikachitika, Ufumu wa Mulungu umene Kristu ndiye Wolamulira  wake udzaphwanya maboma ena onse, monga momwe tinaŵerengera mu Mutu 46.

Ndiye taziyang’ana bwinobwino zithunzizo zimene zili pamasamba aŵiri amene tadutsawo ndipo tikambirana zimenezo. Pa Mateyu 24:6-14 ndi Luka 21:9-11, ungaŵerenge za zimene ukuona pa zithunzipo. Ndiponso ukuona kuti chithunzi chilichonse chili ndi nambala yaing’ono. Nambala yomweyo ikupezekanso kuchiyambi kwa ndime imene ikufotokoza chithunzicho. Tsono tiye tione ngati mbali zambiri za chizindikiro chimene Yesu anapereka zikukwaniritsidwa masiku ano.

(1) Yesu ananena kuti: “Mudzayamba kumva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo; . . . mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” Kodi wakhala ukumvapo mbiri za nkhondo?— Nkhondo yoyamba ya padziko lonse inaliko kuyambira mu 1914 mpaka 1918, kenako panatsatira nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, kuyambira mu 1939 mpaka 1945. Kale kunali kusanachitikepo nkhondo za padziko lonse! Masiku ano nkhondo zili padziko lonse lapansi. Tingati masiku onse pa TV, pa wailesi, ndi m’manyuzipepala, timamva ndi kuŵerenga za nkhondo.

(2) Yesu ananenanso kuti: “Kudzakhala njala . . . m’malo akutiakuti.” Ndikhulupirira ukudziŵa kuti si anthu onse amene ali ndi chakudya chokwanira. Tsiku lililonse anthu masauzande ambiri amafa chifukwa chakuti alibe chakudya chokwanira.

(3) Yesu anawonjezera kuti: ‘Kudzakhala miliri m’malo akutiakuti.’ Kodi mliri umaudziŵa?— Ndi nthenda imene imapha anthu ambiri. Mliri wina waukulu wotchedwa fuluwenza ya ku Spain unapha anthu pafupifupi mamiliyoni 20 chaka chimodzi chokha. Masiku ano mwina anthu ambiri kuposa pamenepo adzamwalira ndi Edzi. Palinso kansa, matenda a mtima, ndi matenda ena amene akupha anthu masauzande ambiri chaka chilichonse.

 (4) Yesu anatchulanso mbali ina ya chizindikiro kuti: “Kudzakhala . . . zivomezi m’malo akutiakuti.” Kodi chivomezi ukuchidziŵa?— Chivomezi chimagwedeza nthaka imene waimapo. Nyumba zimagwa, ndipo nthaŵi zambiri anthu amafa. Kuyambira chaka cha 1914, kwachitika zivomezi zambiri chaka chilichonse. Kodi wakhala ukumvapo za zivomezi?—

(5) Yesu ananena kuti mbali ina ya chizindikiro idzakhala ‘kuchuluka kwa kuipa.’ Ndi chifukwa chake kuba ndi chiwawa zachuluka. Anthu kulikonse akuopa kuti mwina wina awaloŵera m’nyumba. Sizinachitikepo kalelonse kuti padziko lonse lapansi anthu aziphwanya malamulo ndi kuchita chiwawa ngati masiku ano.

(6) Yesu anatchula mbali yofunika kwambiri ya chizindikirocho pamene ananena kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Ngati iwe umakhulupirira “uthenga uwu wabwino,” ndiye kuti uyenera kuwauza ena. Ukatero, udzakwaniritsa nawo mbali imeneyi ya chizindikiro.

Anthu ena anganene kuti zimene Yesu ananeneratu zakhala zikuchitika kuyambira kalekale. Koma zinthu ngati zimenezi sizinachitikepo zonse m’madera ambiri padziko lapansi komanso panthaŵi imodzi ngati mmene zikuchitikira. Ndiye kodi ukumvetsa zimene chizindikiro chikutanthauza?— Chikutanthauza kuti tikaona zinthu zonsezi zikuchitika, ndiye kuti dziko loipali lichoka posachedwapa ndipo dziko latsopano la Mulungu litenga malo ake.

Pamene Yesu ananena za chizindikiro, anatchulanso za nyengo yapadera ya pachaka. Iye anati: “Pempherani kuti kuthaŵa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu.” (Mateyu 24:20) Kodi iwe ukuganiza kuti anatanthauza chiyani?—

Eya, ngati munthu akufuna kuthaŵa tsoka linalake pa nyengo yachisanu, pamene kumakhala kovuta ngakhale kwangozi kuyenda  chifukwa cha kuipa kwa nyengo, kodi chingachitike ndi chiyani?— Ngati zingachitike kuti munthu uja ndi kuthaŵa, amayamba wavutika kwambiri. Kodi sizingakhale zomvetsa chisoni munthu kumwalira atakumana ndi chimphepo chifukwa chabe chakuti anali ndi zinthu zina zambiri zochita m’malo moyamba ulendo wake?—

Pamene Yesu analankhula zothaŵa nthaŵi yachisanu, anali kuphunzitsa mfundo yotani?

Kodi ukuiona mfundo imene Yesu anali kunena pamene anafotokoza kuti munthu safunika kuyembekeza nyengo yachisanu kuti ayambe kuthaŵa?— Anali kutiuza kuti popeza tikudziŵa kuti Armagedo ili pafupi, sitifunika kuzengereza kuchitapo kanthu kuti tisonyeze kuti timakonda Mulungu mwa kumutumikira. Ngati tizengereza, tidzachedweratu. Ndipo tidzakhala ngati aja amene panthaŵi ya Chigumula chachikulu chija anamva chenjezo la Nowa koma sanaloŵe m’chingalawa.

Tsopano, tiye tikambirane mmene zinthu zidzakhalira itatha nkhondo yaikulu ya Armagedo. Tidzadziŵa zimene Mulungu watikonzera ife tonse amene tikumukonda ndi kumutumikira masiku ano.

Otsatiraŵa ndi ena mwa malemba osonyeza kuti Armagedo ili pafupi: 2 Timoteo 3:1-5 ndi 2 Petro 3:3, 4.