Mutu 35
Tingauke kwa Akufa
TIKAMWALIRA, kodi Mulungu adzafuna kutiukitsa kwa akufa, kutanthauza kutipatsanso moyo?— Yobu, amene anali munthu wabwino, anakhulupirira kuti Mulungu amafuna kuchita zimenezo. Choncho pamene Yobu anaona kuti ali pafupi kumwalira, anauza Mulungu kuti: ‘Mukadzandiitana, ndidzakuyankhani.’ Yobu ananena kuti Yehova Mulungu adzakhumba, kapena kuti adzafunitsitsa, kumuukitsa kwa akufa.—Yobu 14:14, 15.
Yesu amatengera Yehova Mulungu, Atate ake, ndipo amafuna kutithandiza. Pamene munthu wodwala khate anauza Yesu kuti, ‘ngati mufuna mukhoza kundikonza,’ Yesu anayankha kuti: ‘Ndifuna.’ Ndipo anachiritsa khate la munthu uja.—Marko 1:40-42.
Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amakonda ana?
Yesu anaphunzira kwa Atate ake kukonda ana. Kale, Yehova kwa maulendo aŵiri anagwiritsa ntchito atumiki ake kuukitsa ana kwa akufa. Eliya anapempha Yehova kuti autse mwana wa mkazi wina amene anakomera mtima Eliyayo. Ndipo Yehova anachitadi zomwezo. Yehova anagwiritsanso ntchito Elisa mtumiki wake kuukitsa mnyamata wamng’ono kwa akufa.—1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37.
Luka 20:38) Baibulo limanena kuti ‘ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, sizingakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu.’—Aroma 8:38, 39.
Kodi ukusangalala kudziŵa kuti Yehova amatikonda kwambiri chonchi?— Iye sangotiganizira pamene tili ndi moyo. Amatikumbukiranso tikamwalira. Yesu ananena kuti Atate ake amaona anthu akufa amene amakonda ngati kuti ali ndi moyo! (Yesu ali padziko lapansi pano, anasonyeza kuti Yehova amasamala ana aang’ono. Ndikukhulupirira ukukumbukira kuti Yesu anapeza nthaŵi youza ana za Mulungu. Koma kodi unali kudziŵa kuti Mulungu anapatsa Yesu mphamvu youkitsa ana kwa akufa?— Tiye tikambirane za nthaŵi imene Yesu anaukitsa mwana wamkazi wa zaka 12 wa munthu wina dzina lake Yairo.
Yairo ndi mkazi wake anali ndi mwana mmodzi yekhayo, ndipo iwo anali kukhala pafupi ndi nyanja ya Galileya. Tsiku lina mtsikanayo anadwala kwambiri ndipo Yairo anaona kuti mwana ameneyo adzafa. Anayamba kuganiza za Yesu, munthu wabwino uja amene iye Yairo anamvapo kuti amachiritsa anthu. Choncho Yairo anapita kukamufunafuna. Iye anapeza Yesu m’mphepete mwa nyanja ya Galileya, akuphunzitsa anthu ambiri.
Yairo analoŵa pa khamu la anthulo mpaka anafika pamene panali Yesu ndipo anagwada pamaso pa Yesuyo. Kenako anati kwa Yesu: ‘Mwana wanga wamkazi wadwala kwambiri. Kodi mungabwere ndi kumuthandiza? Tiyeni mukaone.’ Yesu ananyamuka nthaŵi yomweyo kupita ndi Yairo. Nalonso khamu la anthu lija limene linabwera kudzaona Mphunzitsi Waluso linatsatira. Koma atayenda mtunda pang’ono, amuna ena anafika kuchokera kunyumba kwa Yairo ndi kumuuza kuti: “Mwana wako wafa. Uvutiranjinso Mphunzitsi?”
Yesu anamva zimene amunawo ananena. Iye anadziŵa kuti Yairo anali ndi chisoni kwambiri pofedwa mwana wake yekhayo. Ndiye Iye anamuuza kuti: ‘Usaope. Ingokhulupirira Mulungu, ndipo mwana
wako adzakhala bwino.’ Kenako anapitiriza ulendowo mpaka atafika panyumba pa Yairo. Kumeneko anapeza anthu akulira. Iwo anali ndi chisoni chifukwa chakuti mwana wamng’onoyo, bwenzi lawo, anali atamwalira. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Lekani kulira. Mwanayu sanafe, koma ali m’tulo.’Yesu atanena zimenezi, anthuwo anayamba kuseka, chifukwa chakuti iwo anali kudziŵa kuti mtsikanayo wamwalira. Nanga ukuganiza ndi chifukwa chiyani Yesu ananena kuti iye anali m’tulo?— Kodi ukuganiza kuti iye anafuna kuti anthu aphunzirepo chiyani?— Iye anafuna kuti iwo adziŵe kuti imfa ili ngati kugona tulo tatikulu. Anafuna kuwaphunzitsa kuti adziŵe kuti mwa mphamvu ya Mulungu, iye Yesuyo angautse munthu wakufa mosavuta kukhalanso ndi moyo monga mmene tingautsire munthu amene ali m’tulo.
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Yesu anachita mwa kuukitsa mwana wa Yairo kwa akufa?
Ndiye Yesu anauza onse kuchoka m’nyumbamo kupatulapo atumwi ake Petro, Yakobo, ndi Yohane ndi atate ndi amayi ake a mwanayo. Kenako analoŵa kumene mwanayo anali. Anagwira dzanja lake ndi kunena kuti: ‘Mwanawe, tauka!’ Nthaŵi yomweyo, mwana uja ananyamuka ndipo anayamba kuyenda! Atate ndi amayi ake anakondwera kwambiri.—Marko 5:21-24, 35-43; Luka 8:40-42, 49-56.
Tsono taganiza izi. Popeza kuti Yesu anaukitsa mwana wamkazi ameneyo, kodi angachitenso chimodzimodzi kwa ena?— Kodi ukukhulupirira kuti adzachitadi zimenezo?— Inde, adzatero. Yesu iye mwini ananena kuti: ‘Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu anga, ndi kutuluka.’—Kodi ukuganiza kuti Yesu amafuna kuukitsa anthu akufa?— Nkhani ina m’Baibulo imatithandiza kupeza yankho. Zimene zinachitika tsiku lina pafupi ndi mudzi wa Nayini zimasonyeza mmene Yesu amaonera anthu amene akulira pamaliro.
Mayi wina anali pamaliro a mwana wake pamene khamulo linali kuchoka mu mudzi wa Nayini. Mayiyu mwamuna wake anali atafa kale, koma tsopano mwana wake yekhayo anamwalira. Koma ndiye anali ndi chisoni chachikulu! Anthu ambiri a ku Nayini anali kutsatira pamene mtembo wa mwana wake anali kupita nawo kunja kwa mudziwo. Mayiyo anali kulira, ndipo anthu sanathe kumutonthoza.
Tsiku limeneli, Yesu ndi ophunzira ake anali kubwera ku mudzi wa Nayini. Atafika pafupi ndi pachipata, anakumana ndi khamulo likupita kukaika mwana wa mayiyo. Yesu ataona mayi uja akulira, anagwidwa chifundo. Mtima wake unakhudzidwa kwambiri poona kukula kwa chisoni cha mayiyo. Ndiye anafuna kumuthandiza.
Chotero, polankhula mokoma mtima koma mwamphamvu ndithu kuti mayiyo amve, Yesu anati: ‘Osalira.’ Mmene anamvekeramo ndi zochita zake zinachititsa kuti aliyense amuyang’ane mwachidwi. Pamene Yesu anali kupita pamene panali mtembo, onse angakhale anadabwa kwambiri kuti kodi iye akufuna kuchita chiyani. Kenako Yesu ananena molamula, kuti: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka”! Pamenepo, mnyamatayo anakhala tsonga! Ndipo anayamba kulankhula.—Luka 7:11-17.
Tangoganiza mmene mayiyo anamvera! Kodi iwe ungamve bwanji utalandira munthu amene umamukonda yemwe wauka kwa akufa?— 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Yesu amakonda anthu ndipo amafuna kuwathandiza?— Tangoganiza mmene zidzakomera m’dziko latsopano la Mulungu kulandira anthu amene adzauka kwa akufa kukhala ndi moyo!—Kodi kuuka kwa mwana yekhayu wa mayi uyu kumasonyeza chiyani?
Panthaŵiyo ena amene adzauka kwa akufa ndi anthu amene tinali kuwadziŵa, kuphatikizapo ana. Tidzawadziŵa ngati mmene Yairo anadziŵira mwana wake pamene Yesu anamuukitsa. Ena adzakhala anthu amene anamwalira kalelo zaka mahandiredi kapena masauzande zapitazo. Koma Mulungu sadzawaiwala ngakhale kuti ndi kale kwambiri pamene iwo anali ndi moyo.
Koma ndiye ndi zosangalatsa kudziŵa kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu, amatikonda kwambiri, eti?— Iwo akufuna kuti ife tikhale ndi moyo, osati zaka zochepa chabe, koma kosatha!
Kuti tidziŵe chiyembekezo chosangalatsa chimene Baibulo limafotokoza chokhudza akufa, tiŵerenge Yesaya 25:8; Machitidwe 24:15; ndi 1 Akorinto 15: