Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mutu 16

Kodi Chofunika Kwambiri Ndi Chiyani?

Kodi Chofunika Kwambiri Ndi Chiyani?

Kodi ndi vuto lanji limene munthu uyu anali nalo?

TSIKU lina mwamuna wina anakaonana ndi Yesu. Iye anali kudziŵa kuti Yesu anali wanzeru kwambiri. Chotero anauza Yesuyo kuti: ‘Mphunzitsi, uzani mbale wanga kuti andipatseko zinthu zimene ali nazo.’ Mwamuna ameneyu anafuna kuti akhaleko ndi zinthu zina za mbale wakeyo.

Iweyo ukanakhala Yesu, kodi ukanachita chiyani?— Yesu anaona kuti mwamuna ameneyu anali ndi vuto. Vuto la mwamunayu si kuti linali kufuna zinthu za mbale wakezo. Koma linali kusadziŵa chinthu chofunika kwambiri m’moyo.

Tiye tiganizire izi. Kodi chofunika kwambiri kwa ife ndi chiyani? Kodi ziyenera kukhala zinthu zoseŵeretsa, kapena zovala zatsopano, kapena zinthu zina ngati zimenezi?— Ayi, pali chinthu china chofunika kwambiri. Ndipo Yesu anafuna kuphunzitsa mfundo imeneyi. Choncho Yesu anasimba nkhani ya munthu wina amene anaiŵala Mulungu. Kodi iweyo ukufuna kuimva?—

Mwamuna ameneyu anali ndi chuma chambiri. Anali ndi minda ndiponso nkhokwe zambiri. Mbewu zimene analima zinabereka bwino zedi, moti analibe nkhokwe zokwanira zosungiramo zokolola zake. Kodi akanachita chiyani? Eya, iye mumtima mwake anati: ‘Ndidzapasula nkhokwe zanga ndi kumanganso zazikulu. Ndiye ndidzasunga mbewu zanga ndi zinthu zanga zonse zabwino m’nkhokwe zatsopanozo.’

 Munthu wachumayo anaganiza kuti chimenechi ndicho chinali chinthu chanzeru kwambiri kuchita. Anaganiza kuti anali wochenjera kwambiri posunga zinthuzo. Ndipo mumtima mwake anati: ‘Ndasunga zinthu zabwino zambiri. Zinthuzi zikhala zaka zambirimbiri. Tsopano ndi nthaŵi yoti ndipumule. Ndidzadya, kumwa, ndi kukondwera.’ Koma panali kanthu kenakake kolakwika ndi kuganiza kwa munthu wachuma ameneyu. Kodi iweyo ukudziŵa chimene chinalakwika?— Anali kungoganiza za iye mwini basi ndi kukondwera kwake. Anaiŵala Mulungu.

Kodi ndi chiyani chimene munthu wachumayu akuganiza?

Tsono Mulungu analankhula ndi munthu wachumayo. Anati: ‘Munthu wopusa iwe. Usiku omwe uno iwe udzafa. Ndani tsopano adzakhala ndi zinthu zonse zimene unazisunga?’ Kodi munthu wachumayo akanatha kugwiritsa ntchito zinthuzo atafa?— Ayi, munthu wina wake akanatenga zinthuzo. Ndiyeno Yesu anati: ‘Ndi chimodzimodzinso kwa munthu amene amadziunjikira chuma mwini yekha koma wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.’—Luka 12:13-21.

 Iwe sukufuna kukhala ngati munthu wachuma ameneyu, si choncho?— Cholinga chake chinali kupeza zinthu zakuthupi basi. Kunalitu kulakwitsa zedi. Iye anali kufuna zinthu zambiri. Koma analibe “chuma cha kwa Mulungu.”

Anthu ambiri masiku ano akufanana ndi munthu ameneyu. Iwo amangofuna zinthu zambiri, zimene zingawabweretsere mavuto. Mwachitsanzo, iweyo uli ndi zoseŵeretsa, eti?— Kodi zina za zoseŵeretsa zimene uli nazo ndi ziti? Tandiuza.— Bwanji ngati mnzako ali ndi kampira kapena chidole kaya chinachake chimene iweyo ulibe? Kodi ndi bwino kuumiriza makolo ako kuti akugulirenso kapena kuti akupezerenso zako?—

Nthaŵi zinatu zoseŵeretsa zimakhala ngati zofunika kwambiri. Koma bwanji ukakhala nazo kwa nthaŵi yaitali?— Zimakhala zakale. Mwina zimasweka, ndipo suzifunanso. Komatu iwe uli ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa zoseŵeretsa. Kodi umachidziŵa chinthu chimenechi?—

Kodi iweyo uli ndi chiyani chimene chili chofunika kwambiri kuposa zoseŵeretsa?

Ndi moyo wako. Moyo wako ndi wofunika kwambiri chifukwa kupanda moyowo, sungachite chilichonse. Koma moyo wako umadalira kuchita chimene chimakondweretsa Mulungu, si choncho kodi?— Chotero sitiyenera kukhala ngati munthu wachuma wopusa uja amene anaiŵala Mulungu.

 Si ana okha amene angachite zinthu zopusa monga munthu wachuma uja. Anthu akuluakulu amachitanso zimenezi. Ena mwa iwo amafuna zinthu zambiri kuposa zimene ali nazo. Mwina angakhale ndi chakudya chokwanira, zovala zokwanira, ndi nyumba yokhalamo. Komabe amafuna zinanso. Amafuna zovala zambiri ndiponso nyumba zikuluzikulu. Komatu zinthu zimenezi zimafuna ndalama zambiri. Choncho amagwira ntchito zolimba kuti apeze ndalama zambirizo. Tsono akapeza ndalamazo, ndi pamenenso amafuna zinthu zambiri.

Anthu ena nthaŵi zonse amakhala akugwira ntchito kuti apeze ndalama chotero sakhalanso ndi nthaŵi yocheza ndi banja lawo. Amakhalanso alibe nthaŵi yochita zinthu za Mulungu. Koma kodi ndalamazo zingasunge moyo wawo?— Ayi, sizingausunge. Kapena kodi angathe kuzigwiritsa ntchito atafa?— Ayinso. Chifukwa chakuti akufa sangachite kanthu kalikonse.—Mlaliki 9:5, 10.

Kodi zikutanthauza kuti ndi kulakwa kukhala ndi ndalama?— Ayi. Ife tingagule chakudya ndiponso zovala ndi ndalamazo. Baibulo limanena kuti ndalama zimatchinjiriza. (Mlaliki 7: 12) Koma ngati tikonda ndalama, tingakhale m’mavuto. Tingakhale ngati munthu wachuma wopusa uja amene anadziunjikira chuma mwini yekha koma wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.

Kodi zimatanthauza chiyani kukhala ndi chuma cha kwa Mulungu?— Zimatanthauza kuika Mulungu pamalo oyamba m’moyo wathu. Anthu ena amanena kuti amakhulupirira Mulungu. Iwo amaganiza kuti kungokhulupirira kokha ndicho chinthu chofunika basi. Koma kodi anthu otereŵa alidi ndi chuma cha kwa Mulungu?— Ayi, amafanana ndi munthu wachuma uja amene anaiŵala Mulungu.

Yesu sanaiŵalepo Atate ake a kumwamba. Iye sanafune kuti akhale ndi ndalama zambiri. Ndipo analibe zinthu zochuluka. Yesu anadziŵa chimene chinali chofunika kwambiri pa moyo. Kodi ukuchidziŵa?— Ndicho kukhala ndi chuma cha kwa Mulungu.

Kodi mwana uyu akuchita chiyani chofunika kwambiri?

Tandiuza, kodi tingakhale bwanji ndi chuma cha kwa Mulungu?— Tingakhale ndi chuma cha kwa Mulungu ngati tikuchita zimene zimakondweretsa  Mulunguyo. Yesu anati: ‘Ine ndimachita zimene zimakondweretsa Mulungu.’ (Yohane 8: 29) Mulungu amakondwera tikamachita zimene iye amafuna kuti tichite. Tsopano tandiuza, ndi zinthu ziti zimene iweyo ungachite kuti ukondweretse Mulungu?— Inde, kuŵerenga Baibulo, kupita ku misonkhano yachikristu, kupemphera kwa Mulungu, ndiponso kuthandiza ena kudziŵa za Mulunguyo. Zimenezi ndi zinthu zofunika kwambiri m’moyo.

Chifukwa chakuti Yesu anali ndi chuma cha kwa Mulungu, Yehova anamusamalira kwambiri. Anamupatsa mphoto yokhala kosatha. Ife tikakhala ngati Yesu, Yehova adzatikonda ndi kutisamaliranso. Chotero tiye tikhale ngati Yesu osati ngati munthu wachuma uja amene anaiŵala Mulungu.

Naŵa malemba ena a m’Baibulo amene akusonyeza mmene tiyenera kuonera zinthu zakuthupi: ­Miyambo 23:4; 28:20; 1 Timoteo 6:6-10; ndi Ahebri 13:5.