Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mutu 6

Mphunzitsi Waluso Anatumikira Anthu Ena

Mphunzitsi Waluso Anatumikira Anthu Ena

KODI umasangalala munthu wina akakuchitira zabwino?— Eya, anthu ena amasangalala wina akawachitira zabwino. Tonse timasangalala. Mphunzitsi Waluso anali kudziŵa zimenezi, ndipo nthaŵi zonse anali kuchitira anthu zinthu. Anati: ‘Ndinabwera kuno kudzatumikira anthu, osati kuti iwo anditumikire.’—Mateyu 20:28.

Kodi ophunzira a Yesu anali kukangana za chiyani?

Ndiye ngati tikufuna kukhala monga Mphunzitsi Waluso, kodi tiyenera kuchita chiyani?— Tiyenera kutumikira ena. Tiyenera kuwachitira zabwino. Ndi zoona kuti anthu ambiri sachita zimenezi. Anthu ambiri amangofuna kuti nthaŵi zonse ena aziwatumikira. Panthaŵi ina ngakhale ophunzira a Yesu anali kuganiza choncho. Aliyense anafuna kukhala wamkulu kapena munthu wofunika kwambiri.

Tsiku lina Yesu anali kuyenda ndi ophunzira ake. Atafika m’mudzi wa Kapernao, kufupi ndi nyanja ya Galileya, onse analoŵa m’nyumba inayake. M’nyumbamo Yesu anawafunsa kuti: ‘Munali kukangana chiyani panjira?’ Iwo sanayankhe chifukwa m’njira anali kukangana kuti wamkulu ndani.—Marko 9:33, 34.

 Yesu anadziŵa kuti si bwino kuti aliyense wa ophunzira ake aziganiza kuti ndiye wamkulu pa onse. Motero, monga tinaphunzirira m’mutu woyamba wa buku lino, iye anaimika mwana wamng’ono pakati pawo ndi kuwauza kuti ayenera kukhala odzichepetsa monga mwanayo. Komabe iwo sanaphunzirepo kalikonse. Choncho Yesu ali pafupi kufa, anawapatsa phunziro limene sanaliiwale. Kodi anachita chiyani?—

Eya, pamene onse anali kudya pamodzi, Yesu ananyamuka pathebulopo natenga thawulobafa ndi kulimanga m’chiuno mwake. Kenako anatenga beseni ndi kuikamo madzi. Ophunzira ake ayenera kuti anadabwa kuti akufuna kuchita chiyani. Iwo akuonerera, Yesu anazungulira mwa onsewo; anali kuŵerama ndi kumawasambitsa mapazi awo. Kenako anapukuta mapazi awowo ndi thawulobafa lija. Taganiza zimenezi! Bwanji iweyo ukanakhalapo, kodi ukanamva bwanji?—

Kodi apa Yesu anali kupatsa ophunzira ake phunziro lotani?

Ophunzira ake ataona zimenezo anaganiza kuti Mphunzitsi Walusoyo sanayenere kuwachitira zimenezi. Iwo anachita manyazi. Ndipotu Petro anafuna kukana kuti Yesu amutumikire modzichepetsa chonchi. Koma Yesu ananena kuti anafunikira kuchita zimenezi.

Masiku ano ife nthaŵi zambiri sitisambitsana mapazi. Koma zimenezi zinali kuchitika m’nthaŵi imene Yesu anali padziko lapansi. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Eya, kudziko limene Yesu ndi ophunzira ake anali kukhala, anthu anali kuvala sandasi zoonetsa phazi lonse. Ndiye akamayenda m’misewu yafumbi, mapazi awo anali kukhala ndi fumbi zedi. Kusambitsa mapazi afumbi a munthu amene wabwera kudzacheza kunyumba kunali kukoma mtima.

Koma tsiku ili palibe aliyense wa ophunzira a Yesu amene anadzipereka kuti asambitse anzake mapazi awo. Ndiye Yesu mwiniyo anawasambitsa. Mwa kuchita zimenezi, Yesu anapatsa ophunzira ake phunziro lofunika. Iwo anafunika kuphunzira zimenezi. Ndipo ifenso lerolino tifunika kuphunzira zomwezi.

 Kodi phunziro lake ukulidziŵa?— Yesu atakhalanso pathebulo paja, anafotokoza kuti: “Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake.”—Yohane 13:2-14.

N’chiyani chimene ungachite kuti uthandize ena?

Apa Mphunzitsi Waluso anasonyeza kuti anafuna kuti ophunzira ake azitumikirana. Sanafune kuti azingoganiza za iwo okha. Sanafune kuti iwo aziganiza kuti ndi ofunika kwambiri moti anthu ena ayenera kumawatumikira nthaŵi zonse. Anafuna kuti iwo akhale ofunitsitsa kutumikira ena.

Kodi limeneli silinali phunziro labwino?— Kodi iwe udzakhala ngati Mphunzitsi Waluso ndi kumatumikira anthu ena?— Tonsefe tingathe kuchitira anthu ena zinthu. Iwo adzakondwera nazo. Koma koposa zonse, zidzakondweretsa Yesu ndi Atate ake.

Kutumikira ena si kovuta. Utayang’ana zimene anthu ena amachita, ungaone zinthu zambiri zimene ukhoza kuchitira anthu ena. Tsopano taganizira: Kodi pali chilichonse chimene ungachite kuti uthandize  amayi ako? Iwe ukudziŵa kuti amayi ako amachita zinthu zambiri pokusamalira ndiponso posamalira banja lonse. Kodi ungathe kuwathandiza?— Bwanji osawafunsa zimene ungawathandize?

Mwinamwake ungaike zinthu pa thebulo pamene banja likufuna kuyamba kudya. Mwinanso ukhoza kuchotsa mbale pathebulo onse atatha kudya. Ana ena amakatunga madzi tsiku lililonse. Chilichonse chimene ungachite, udzakhala ukutumikira ena monga anachitira Yesu.

Kodi uli ndi azing’ono ako ndi azilongo ako aang’ono kwa iwe amene ungawatumikire? Kumbukira kuti Mphunzitsi Waluso, Yesu, anatumikira ophunzira ake. Mwa kutumikira azing’ono ako ndi azilongo ako ang’onoang’ono, udzakhala ngati Yesu. Kodi ukhoza kuwachitira chiyani?— Mwinamwake ungawathandize kuti adziŵe kusamba okha  bwinobwino. Mwinanso ungawathandize kuvala zovala. Kapenanso ungawathandize kuyala kapena kuyalula pogona pawo. Kodi ungaganizire zinanso zimene ukhoza kuwachitira?— Adzakukonda ukamawachitira zimenezi, monga mmene ophunzira a Yesu anamukondera iye.

Kusukulu nako ukhoza kutumikira anthu ena. Ungatumikire anzako a m’kalasi kapena aphunzitsi ako. Ngati wina wagwetsa mabuku ake, iwe ungasonyeze kukoma mtima pomuthandiza kutola mabukuwo. Ukhoza kudzipereka kufufuta pa bulakibolodi kapena kuwachitira chinthu chinachake aphunzitsi ako. Ngakhale kutsegula chitseko kuti wina aloŵe kulinso kukoma mtima.

Nthaŵi zina anthu sadzatiyamikira kuti tawachitira zabwino. Kodi ukuganiza kuti tiyenera kuleka kuchita zabwino chifukwa cha zimenezi?— Ayi! Anthu ambiri sanayamikire Yesu pa ntchito zabwino zimene anachita. Koma zimenezo sizinamusiyitse kuchita zabwino.

Ifenso tisasiye kutumikira anthu ena. Tikumbukire Mphunzitsi Waluso, Yesu, ndipo nthaŵi zonse tiyesetse kutsatira chitsanzo chake.

Kuti muŵerenge malemba enanso onena za kuthandiza anthu ena, pezani Miyambo 3:27, 28; Aroma 15:1, 2; ndi Agalatiya 6:2.