Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mutu 12

Yesu Atiphunzitsa Kupemphera

Yesu Atiphunzitsa Kupemphera

KODI iweyo umalankhula ndi Yehova Mulungu?— Iye amafuna kuti uzilankhula naye. Kulankhula ndi Mulungu kumatchedwa pemphero. Nthaŵi zambiri Yesu anali kulankhula ndi Atate ake amene anali kumwamba. Nthaŵi zina anali kufuna kukhala payekha polankhula ndi Mulungu. Tsiku lina, ‘anakwera m’phiri yekhayekha, kukapemphera moti ngakhale kunada, iye anali kumeneko yekha,’ limatero Baibulo.—Mateyu 14:23.

Kodi ungapite kuti ukafuna kupemphera pawekha kwa Yehova?— Mwina ungakhale pawekha kuti ulankhule ndi Yehova usanagone usiku. Yesu ananena kuti: ‘Popemphera, loŵa m’chipinda chako, utseke chitseko chako, ndi kupemphera kwa Atate ako.’ (Mateyu 6:6) Kodi umapemphera kwa Yehova usiku uliwonse usanagone?— Uyenera kumapemphera.

Yesu anali kupemphera ali yekha . . . komanso ndi ena

Yesu analinso kupemphera akakhala ndi anthu. Pamene mnzake Lazaro anamwalira, Yesu anapemphera  pamodzi ndi ena pamalo pamene anaikapo Lazaro. (Yohane 11:41, 42) Ndipo Yesu analinso kupemphera akasonkhana ndi ophunzira ake. Kodi iwe umapita ku misonkhano kumene amapemphera?— Nthaŵi zambiri amene amapemphera kumeneko ndi munthu wamkulu. Akamapemphera, uzimvetsera kwambiri chifukwa amakhala akukulankhulira kwa Mulungu. Ukamatero, ndi pamene unganene kuti “Ameni” pomaliza pemphero. Kodi ukudziŵa kuti umatanthauza chiyani ukayankha kuti “Ameni” pamapeto pa pemphero?— Umatanthauza kuti walikonda pemphero limenelo. Umatanthauzanso kuti ukulivomereza ndipo ukufuna kuti likhalenso pemphero lako.

’chifukwa chiyani uyenera kumvetsera kwambiri ena akamapemphera pamsonkhano?

Yesu anapempheranso nthaŵi ya chakudya. Anayamika Yehova chifukwa chomupatsa chakudya. Kodi iwe nthaŵi zonse umapemphera usanadye chakudya?— Ndi bwino kuti tisanayambe kudya tiyamike Yehova chifukwa chotipatsa chakudya. Ngati ukufuna kudya chakudya ndi munthu wina, mwina iyeyo angapemphere. Koma bwanji ngati uli wekha ndipo ukufuna kudya? Kapena bwanji ngati ukufuna kudya ndi anthu amene sayamika Yehova?— Pamenepo ufunika kupemphera wekha.

Kodi nthaŵi zonse mawu ako afunika kumveka popemphera? Kapena kodi Yehova akhoza kumva ngati wapemphera chamumtima?— Yankho lake tingalipeze pa zimene zinachitikira Nehemiya. Ameneyu anali kulambira  Yehova ndipo anali kugwira ntchito m’nyumba ya Mfumu Aritasasta ya ku Perisiya. Tsiku lina, Nehemiya anali wachisoni kwambiri chifukwa anamva kuti mpanda wa Yerusalemu, mudzi waukulu wa anthu akwawo, unali wakugwa.

Kodi ndi liti pamene ungapemphere chamumtima, ngati Nehemiya?

Mfumu itamufunsa Nehemiya kuti n’chifukwa chiyani anali wachisoni, iye anayamba wapemphera chamumtima. Kenako Nehemiya anauza mfumu chifukwa chake anali wachisoni ndipo anapempha kuti apite ku Yerusalemu kuti akamange mpandawo. Kodi ukuganiza kuti chinachitika n’chiyani?—

Inde, Mulungu anayankha pemphero la Nehemiya. Mfumu inamuuza kuti apite! Ndipo mfumuyo inapatsa Nehemiya mitengo yambiri yoti akamangire mpanda uja. Ndiye apa taona kuti Mulungu angayankhedi mapemphero athu, ngakhale tikamawanenera mu mtima.—Nehemiya 1:2, 3; 2:4-8.

 Tsono taganiza izi. Kodi uyenera kuŵerama mutu ukafuna kupemphera? Kodi uyenera kugwada? Ukuganiza bwanji?— Nthaŵi zina Yesu anali kugwada akafuna kupemphera. Nthaŵi zina anali kuimirira. Ndipo nthaŵi zinanso anali kuyang’ana kumwamba popemphera. Izi ndi zimene anachita popempherera Lazaro.

Ndiye zimenezi zikusonyeza chiyani?— Inde, zikusonyeza kuti mmene wakhalira popemphera si chinthu chofunika kwambiri. Nthaŵi zina ndi bwino kuŵerama mutu ndi kutseka maso popemphera. Nthaŵi zina ungagwade ndithu, ngati mmene Yesu anachitira. Koma kumbukira kuti tingapemphere kwa Mulungu nthaŵi iliyonse masana kapena usiku, ndipo iye adzatimva. Chofunika kwambiri popemphera ndi kukhulupiriradi kuti Yehova akumvetsera. Kodi umakhulupirira kuti Yehova amamva mapemphero ako?—

Kodi ungalankhule naye chiyani Mulungu m’pemphero?

Kodi tikamapemphera kwa Yehova tiyenera kunena chiyani?— Tandiuza: Iweyo ukamapemphera, umamuuza chiyani Mulungu?— Yehova amatipatsa zinthu zabwino zambiri, ndipo ndi bwino kumuyamika chifukwa cha zimenezo, si choncho?— Tingamuyamike chifukwa chotipatsa chakudya. Koma kodi unayamba wamuyamika kunja kutacha kopanda mitambo, kapena chifukwa cha mitengo yobiriŵira, ndi maluŵa okongola?— Anapanga zonsezo ndi iyeyo.

Tsiku lina ophunzira a Yesu anamupempha kuti awaphunzitse kupemphera. Ndipo Mphunzitsi Walusoyo anawaphunzitsa. Anawasonyeza zinthu zofunika kwambiri kuzipempherera. Kodi ukuzidziŵa zinthu zimenezo?— Tenga Baibulo  lako ndipo tsegula pa Mateyu chaputala 6. Pa vesi 9 mpaka 13, tikupezapo pemphero limene anthu ambiri amatcha Pemphero la Atate Wathu kapena Pemphero la Ambuye. Tiye tiŵerengere limodzi.

Apa tikuphunzirapo kuti Yesu anatiuza kupempherera dzina la Mulungu. Ananena kuti tizipemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Kodi Mulungu dzina lake ndani?— Eya, ndi Yehova, ndipo dzina limenelo tiyenera kulikonda.

Chachiŵiri, Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Ufumu umenewu ndi wofunika kwambiri chifukwa udzabweretsa mtendere padziko lapansi ndipo udzasandutsa dzikoli paradaiso.

Chachitatu, Mphunzitsi Waluso ananena kuti tizipemphera kuti kufuna kwa Mulungu kuchitike padziko lapansi pano monga kumwamba. Ndiye ngati timapempherera zimenezi, tiyenera kuchita zimene Mulungu amafuna.

Kenako, Yesu anatiphunzitsa kupempherera chakudya chimene tikufunika patsiku. Ananenanso kuti tiyenera kupepesa kwa Mulungu tikachita zinthu zoipa. Ndipo tiyenera kupempha Mulungu kuti atikhululukire. Koma kuti iye atikhululukire, ife tiyenera kukhululukira ena ngati atilakwira. Kodi ukuganiza kuti zimenezi ndi zosavuta?—

Pomaliza, Yesu ananena kuti tiyenera kupemphera kuti Yehova Mulungu atiteteze kwa woipayo, Satana Mdyerekezi. Choncho, zinthu zonsezi ndi zabwino kutchula m’pemphero kwa Mulungu.

Tiyenera kukhulupirira kuti Yehova amamva mapemphero athu. Kuwonjezera pa kumupempha kuti atithandize, tiyenera kumuyamika nthaŵi zonse. Iye amasangalala tikamalankhula naye m’pemphero zochokera pansi pa mtima ndiponso tikamapempha zinthu zoyenera. Ndipo adzatipatsa zinthuzo. Kodi ukukhulupirira zimenezo?—

Malangizo ena abwino a pemphero akupezeka pa Aroma 12:12; 1 Petro 3:12; ndi 1 Yohane 5:14.