Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
M’Baibulo muli mfundo zothandiza ndipo zikhoza kugwiritsidwa ntchito kulikonse. Ana ayenera kuphunzira zimene Atate wawo wakumwamba amanena osati zimene anthu ena amanena.
Zimene Ana Amafuna Kwa Makolo Awo
Cholinga cha bukuli ndi chofuna kuthandiza ana komanso amene akuwawerengera bukuli kuti azikambirana momasuka nkhani zofunika.
MUTU 1
Chifukwa Chake Yesu Anali Mphunzitsi Waluso
Kodi Yesu ankaphunzitsa zinthu zotani? Nanga zomwe ankaphunzitsazo anazitenga kuti?
MUTU 2
Kalata Yochokera kwa Mulungu
Kalatayi imapezeka m’buku lofunika kwambiri kuposa mabuku ena onse.
MUTU 3
Amene Anapanga Zinthu Zonse
Ndani analenga mbalame ndi kuziphunzitsa kuimba? Ndani analenga udzu? Ndani anakulenga?
MUTU 4
Mulungu Ali ndi Dzina Lake
Tonsefe tili ndi mayina. Kodi dzina la Mulungu umalidziwa? N’chifukwa chiyani dzina lake ndi lofunika?
MUTU 6
Mphunzitsi Waluso Anatumikira Anthu Ena
Kodi umasangalala munthu wina akakupangira chinthu chabwino? Tonse timasangalala, ndipo Mphunzitsi Waluso ankadziwa zimenezi.
MUTU 7
Kumvera Kudzakuteteza
Ana amaphunzira zinthu kuchokera kwa akuluakulu. Ndipo Mulungu akatiuza kuti tichite zinazake sitiyenera kukaikira ngati zilidi zofunika.
MUTU 9
Tifunika Kukana Ziyeso
Kodi ungachite chiyani ngati munthu wina atakuuza kuti uchite zinthu zoipa?
MUTU 10
Yesu Ali ndi Mphamvu Kuposa Ziwanda
Sitiyenera kuopa ziwanda komabe tiyenera kukhala osamala kuti zisatipusitse.
MUTU 11
Angelo a Mulungu Amatithandiza
Angelo a Mulungu amathandiza anthu omwe amakonda Yehova ndi kumutumikira.
MUTU 12
Yesu Atiphunzitsa Kupemphera
Mungathe kupemphera kwa Mulungu nthawi iliyonse ndipo iye adzamva mapemphero anu.
MUTU 14
Chifukwa Chake Tiyenera Kukhululukira Ena
Yesu anafotokoza nkhani pofuna kutiphunzitsa kufunika kokhululukira ena.
MUTU 17
Mmene Tingakhalire Osangalala
Mphunzitsi Waluso anatchula chinsinsi cha zimene zimapangitsa munthu kukhala wosangalala.
MUTU 20
Kodi Nthawi Zonse Umafuna Kukhala Woyamba?
Kodi Yesu anawauza chiyani ophunzira ake atakangana pofuna kudziwa amene anali woyamba?
MUTU 21
Kodi Tiyenera Kudzitama Tikachita Zabwino?
Yesu ananena nkhani ya Mfarisi ndi wokhometsa msonkho.
MUTU 22
Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Yehova anachita ndi Hananiya komanso Safira.
MUTU 23
Chifukwa Chake Anthufe Timadwala
Kodi zidzatheka kuti nthawi ina anthu azingokhala bwinobwino osadwala?
MUTU 24
Usakhale Wakuba
Werengani nkhaniyi yomwe ikufotokoza za anthu 4 omwe anatenga zinthu za eniake.
MUTU 25
Kodi Amene Amachita Zinthu Zoipa Angasinthe?
Tikaona zimene Saulo komanso mzimayi amene anali hule anachita, zimasonyeza kuti anthu oipa akhoza kusintha n’kukhala anthu abwino.
MUTU 26
Chifukwa Chake Kuchita Zinthu Zabwino Kumavuta
Kodi ukuganiza kuti anthu ochita zoipa angamve bwanji ngati utakana kuchita zimene iwowo akufuna?
MUTU 27
Kodi Mulungu Wako Ndani?
Anthu amalambira milungu yambiri. Kodi inuyo mungalambire mulungu uti? Zimene achinyamata atatu achiheberi anachita zingatithandize kudziwa zimene tingachite.
MUTU 28
Kudziwa Amene Uyenera Kumumvera
“Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.”
MUTU 29
Kodi Mapwando Onse Amakondweretsa Mulungu?
Kodi mukudziwa kuti Baibulo limanena za mapwando angapo omwe anthu anachita? Tikhoza kudziwa maganizo a Mulungu Tikawerenga nkhani zokhudza mapwandowa.
MUTU 30
Zimene Zingatithandize Kuthetsa Mantha
Mphunzitsi Waluso sananene kuti kutumikira Yehova n’kosavuta, koma kuti pali njira imene ingatithandize kukhala olimba mtima.
MUTU 31
Amene Angatitonthoze
Kodi ungatani ngati wakhumudwa kapena ngati ukuona kuti uli wekhawekha?
MUTU 32
Mmene Yesu Anatetezedwera
Phunzirani mmene Yehova anatetezera Yesu kwa anthu amene ankafuna kumupha ali mwana.
MUTU 33
Yesu Angatiteteze
Yesu ali padziko lapansi anasonyeza kuti anali ndi mphamvu zoteteza anthu amene ankamukonda.
MUTU 34
Kodi Chimachitika ndi Chiyani Tikamwalira?
Kodi muyenera kuopa kufa kapena kuopa anthu omwe anamwalira?
MUTU 35
Tingauke kwa Akufa
Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zoukitsa anthu omwe anamwalira kuphatikizaponso ana.
MUTU 36
Kodi Ndani Adzauka kwa Akufa? Nanga Adzakhala Kuti?
Kodi Yesu ananena zotani pa nkhani imeneyi?
MUTU 37
Kukumbukira Yehova ndi Mwana Wake
Yesu anasonyeza otsatira ake njira yapadera yokumbukira zimene Yehova komanso iyeyo anatichitira.
MUTU 38
Chifukwa Chake Tiyenera Kukonda Yesu
Yesu anapereka moyo wake wangwiro kuti tidzapeze moyo wosatha.
MUTU 40
Kukondweretsa Mulungu
Mwambi wa m’Baibulo umati: ‘Mwananga, khala wanzeru, ukondweretse mtima wanga.’
MUTU 41
Ana Amene Amakondweretsa Mulungu
Kodi ndi zinthu ziti zimene mungapange kuti musangalatse Mulungu?
MUTU 42
Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito
Ntchito imatithandiza kuti tiziganiza bwino komanso kuti matupi athu akhale amphamvu. Mukhoza kuphunzira kuti muzisangalala pogwira ntchito.
MUTU 43
Kodi Abale Athu ndi Alongo Athu Ndani?
Kodi anthu omwe si a m’banja lanu angakhalenso abale anu?
MUTU 44
Mabwenzi Athu Azikhala Okonda Mulungu
“Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”
MUTU 45
Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Chiyani? Zimene Tingachite Posonyeza Kuti Tikuufuna
Yesu akadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi, adzasintha zinthu zambiri padzikoli.
MUTU 46
Madzi Anawononga Dziko —Kodi Zidzachitikanso?
Anthu olungama adzakhala padzikoli mpaka kalekale.
MUTU 48
Ungathe Kukhala M’dziko Latsopano la Mulungu
N’chifukwa chiyani ukufuna kudzala ndi moyo wosatha m’Paradaiso?

