Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHIGAWO 13

Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tikondweretse Mulungu?

Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tikondweretse Mulungu?

Muzipewa kuchita zinthu zoipa. 1 Akorinto 6:9, 10

Ngati timakonda Yehova, tiyenera kupewa kuchita zinthu zimene iye amadana nazo.

Yehova safuna kuti tiziba, tiziledzera kapena tizigwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Mulungu amadana ndi aliyense wopha munthu kapena wochotsa mimba, ndiponso amadana n’zoti anthu azigonana amuna kapena akazi okhaokha. Iye safuna kuti tikhale adyera kapena andewu.

Sitiyenera kulambira mafano kapena kuchita zinthu zogwirizana ndi kukhulupirira mizimu.

M’dziko lapansi la Paradaiso limene likubweralo, simudzakhala anthu ochita zoipa.

 Muzichita zinthu zabwino. Mateyu 7:12

Kuti tikondweretse Mulungu, tiyenera kuyesetsa kumutsanzira.

Muzikonda anthu ena powakomera mtima ndi kuwathandiza.

Mukhale oona mtima.

Mukhale achifundo ndipo muzikhululukira ena.

Muziuza ena za Yehova ndiponso zochita zake.​—Yesaya 43:10.