Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?

Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?

Kodi mumaliona kuti ndi . . .

  • buku la nzeru za anthu?

  • buku la nthano?

  • Mawu a Mulungu?

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.”—2 Timoteyo 3:16, Baibulo la Dziko Latsopano.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

Zikutanthauza kuti mungapeze mayankho ogwira mtima a mafunso ofunika kwambiri pa moyo wanu.—Miyambo 2:1-5.

Mungapeze malangizo odalirika othandiza pa moyo wa tsiku ndi tsiku.—Salimo 119:105.

Mungakhale ndi chiyembekezo chenicheni cha m’tsogolo.—Aroma 15:4.

 KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa zitatu izi:

  • Nkhani zake n’zogwirizana mochititsa chidwi. Baibulo linalembedwa zaka zoposa 1,600 ndi anthu osiyanasiyana okwanira 40. Ambiri mwa anthu amenewa, sanaonane n’komwe. Komabe Baibulo lonse ndi logwirizana ndipo lili ndi nkhani yaikulu imodzi.

  • Olemba Baibulo analemba moona mtima. Anthu olemba nkhani nthawi zambiri amakonda kubisa zinthu zina zimene zinachitikira anthu amtundu wawo monga kugonja pa nkhondo. Koma anthu olemba Baibulo analemba moona mtima zolephera zawo ndi za anthu a mtundu wawo.—2 Mbiri 36:15, 16; Salimo 51:1-4.

  • Nthawi zonse maulosi a m’Baibulo amakwaniritsidwa. Baibulo linaneneratu za kuwonongedwa kwa mzinda wakale wa Babulo kutatsala zaka 200 kuti izi zichitike. (Yesaya 13:17-22) Linafotokoza mmene mzindawo udzawonongedwere komanso munthu amene adzatsogolere asilikali okawononga mzindawo. —Yesaya 45:1-3.

    Maulosi ena ambirimbiri anakwaniritsidwa moti chilichonse chimene chinanenedwa m’maulosiwo chinachitikadi. Izi n’zimene tingayembekezere kuchokera m’Mawu a Mulungu.—2 Petulo 1:21.

 GANIZIRANI MFUNDO IYI

Kodi Mawu a Mulungu angakuthandizeni bwanji pa moyo wanu?

Baibulo limayankha funso limeneli pa YESAYA 48:17, 18 ndi pa 2 TIMOTEYO 3:16, 17.