Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 17

Kodi Oyang’anira Dera Amatithandiza Bwanji?

Kodi Oyang’anira Dera Amatithandiza Bwanji?

Malawi

Kagulu ka utumiki

Utumiki wakumunda

Msonkhano wa akulu

Malemba Achigiriki amatchula mobwerezabwereza za Baranaba ndi mtumwi Paulo. Amuna amenewa anali oyang’anira oyendayenda ndipo ankayendera mipingo yoyambirira. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Iwo ankaganizira kwambiri za abale awo auzimu. Paulo ananena kuti ankafuna ‘kubwerera kumizinda yonse kuti akachezere abale’ ndi kuwaona kuti ali bwanji. Iye anali wokonzeka kuyenda maulendo ataliatali kuti akalimbikitse abalewo. (Machitidwe 15:36) Nawonso oyang’anira dera athu masiku ano amakhala ndi mtima umenewu.

Amabwera kumipingo yathu kudzatilimbikitsa. Woyang’anira dera aliyense amayendera mipingo 20 kapena kuposa, ndipo mpingo uliwonse amauchezera kwa mlungu umodzi, kawiri pa chaka. Timalimbikitsidwa kwambiri ndi utumiki wa abale amenewa komanso ngati ali okwatira, timalimbikitsidwa ndi utumiki wa akazi awo. Oyang’anirawa amayesetsa kudziwana ndi aliyense, ana ndi akulu omwe, ndipo amafunitsitsa kuyenda nafe mu utumiki wa kumunda komanso kupita nafe limodzi kumaphunziro athu a Baibulo. Oyang’anira amenewa amachita maulendo aubusa limodzi ndi akulu, komanso amakamba nkhani zolimbikitsa kwambiri pamisonkhano ya pampingo ndiponso ikuluikulu.​—Machitidwe 15:35.

Amalimbikitsa Akhristu onse. Cholinga cha oyang’anira dera n’kuthandiza mipingo kuti ikhale yolimba mwauzimu. Iwo amakumana ndi akulu komanso atumiki othandiza kuti aone mmene mpingo ukuyendera, ndiponso amawapatsa malangizo owathandiza pa maudindo awo. Oyang’anira dera amathandiza apainiya kuti utumiki wawo uziyenda bwino. Komanso amasangalala kudziwana ndi anthu amene angoyamba kumene kusonkhana nafe ndiponso kumva mmene akupitira patsogolo mwauzimu. Woyang’anira dera aliyense amadzipereka ndipo ‘amagwira nafe ntchito limodzi potithandiza.’ (2 Akorinto 8:23) Choncho tiyenera kutsanzira chikhulupiriro chawo komanso kudzipereka kwawo kwa Mulungu.​—Aheberi 13:7.

  • N’chifukwa chiyani oyang’anira dera amachezera mipingo?

  • Kodi mungatani kuti mupindule oyang’anira dera akamachezera mpingo?