Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 22

Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?

Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?

Solomon Islands

Canada

South Africa

Abale ndi alongo a m’banja la Beteli amagwira ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana, ndipo utumiki wawo umathandizira pa ntchito yolalikira ya m’dziko lawo kapenanso m’mayiko ena. Ena mwa abale ndi alongo amenewa amagwira ntchito yomasulira mabuku, kusindikiza magazini ndi mabuku, kutumiza mabuku kumipingo, kujambula nyimbo, masewero ndi mavidiyo, komanso ntchito zina zofunika.

Komiti ya Nthambi imayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Bungwe Lolamulira limapatsa Komiti ya Nthambi udindo woyang’anira ntchito zonse paofesi ya Mboni za Yehova. Komiti ya Nthambi imapangidwa ndi akulu oyenerera atatu kapena kuposa. Komiti imeneyi imadziwitsa Bungwe Lolamulira mmene ntchito ikuyendera m’dziko lawo kapena m’mayiko ena amene komitiyi ikuyang’anira komanso mavuto alionse amene angakhalepo. Malipoti amenewo amathandiza Bungwe Lolamulira kudziwa nkhani zoti lilembe m’mabuku kapena m’magazini komanso nkhani zoti zidzakambidwe pamisonkhano yampingo ndi misonkhano ikuluikulu. Abale oimira Bungwe Lolamulira amatumizidwa nthawi ndi nthawi kuti akayendere nthambi zosiyanasiyana. Iwo amapereka malangizo othandiza kwa abale omwe ali m’Makomiti a Nthambi. (Miyambo 11:14) Woimira likulu la Mboni za Yehova akabwera kudzayendera nthambi, pamachitika msonkhano wapadera. Pamsonkhanowu, iye amakamba nkhani yolimbikitsa kwambiri kwa onse okhala m’dera limene nthambiyo ikuyang’anira.

Kuofesi ya Mboni za Yehova kumagwiridwa ntchito zothandiza mipingo ya m’dzikomo. Abale a udindo kuofesi ya Mboni za Yehova amavomereza kuti mipingo yatsopano ipangidwe. Abale akuofesiwa amayang’aniranso ntchito za apainiya, amishonale, ndiponso oyang’anira madera omwe ali m’gawo limene nthambi yawo imayang’anira. Iwo amakonza misonkhano ikuluikulu, amayang’anira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, komanso amaonetsetsa kuti mabuku akutumizidwa kumipingo kuti abale kumeneko azikawagwiritsa ntchito. Ntchito iliyonse imene imachitika kuofesi ya Mboni za Yehova imathandizira kuti ntchito yolalikira izichitika mwadongosolo.​—1 Akorinto 14:33, 40.

  • Kodi Makomiti a Nthambi amathandiza bwanji Bungwe Lolamulira?

  • Kodi kuofesi ya Mboni za Yehova kumachitika ntchito ziti?