Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 5

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Mudzasangalale Nazo Pamisonkhano Yathu Yachikhristu?

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Mudzasangalale Nazo Pamisonkhano Yathu Yachikhristu?

Argentina

Sierra Leone

Belgium

Malaysia

Anthu ambiri asiya kupita kumapemphero chifukwa amaona kuti sathandizidwa kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri pa moyo wawo kapena salimbikitsidwa mwauzimu. Nanga n’chifukwa chiyani muyenera kupita kumisonkhano yachikhristu ya Mboni za Yehova? Kodi kuchita zimenezi kuli ndi phindu lililonse?

Mukasangalala kukhala pakati pa anthu achikondi. M’nthawi ya atumwi, Akhristu ankasonkhana m’mipingo yosiyanasiyana n’cholinga choti alambire Mulungu, aphunzire Malemba ndiponso alimbikitsane. (Aheberi 10:24, 25) Akhristu akasonkhana, ankaona kuti ali pakati pa mabwenzi enieni achikondi, kapena kuti abale ndi alongo awo auzimu. (2 Atesalonika 1:3; 3 Yohane 14) Masiku ano timachita misonkhano ngati mmene ankachitira Akhristu a m’nthawi ya atumwi ndipo nafenso timasangalala.

Mudzadziwa mmene mungagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo. Mofanana ndi mmene zinkachitikira m’nthawi ya Aisiraeli, masiku anonso anthu onse amasonkhana pamodzi, kaya ndi abambo, amayi kapena ana. Anthu amene ali oyenerera kuphunzitsa mumpingo, amagwiritsa ntchito Baibulo potithandiza kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wathu watsiku ndi tsiku. (Deuteronomo 31:12; Nehemiya 8:8) Aliyense amakhala ndi mwayi wopereka ndemanga pa nkhani zokambirana ndiponso kuimba nawo nyimbo. Tikamachita zimenezi timakhala tikulengeza zimene Akhristufe tikuyembekezera.​—Aheberi 10:23.

Chikhulupiriro chanu mwa Mulungu chidzalimba. Mtumwi Paulo anauza anthu a mumpingo wina umene unalipo m’nthawiyo, kuti: “Ndikulakalaka kukuonani . . . kuti tidzalimbikitsane mwa chikhulupiriro, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Tikapita kumisonkhano yathu, timakhala pamodzi ndi Akhristu anzathu. Zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso zimatilimbikitsa kuti nthawi zonse tizichita zinthu zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.

Tikukulimbikitsani kuti mupite kumsonkhano wathu uliwonse kuti mukaone nokha zimenezi. Tikukutsimikizirani kuti tidzakulandirani ndi manja awiri. Komanso misonkhano yathu yonse ndi yaulere, ndipo sipayendetsedwa mbale ya zopereka.

  • Kodi misonkhano yathu ya mpingo imachitika motsatira chitsanzo chiti?

  • Kodi tingapindule bwanji tikamapezeka pamisonkhano yachikhristu?