Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 27

Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?

Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?

Israel

Czech Republic

Benin

Cayman Islands

Kodi mukufuna kufufuza nkhani zina kuti mulidziwe bwino Baibulo? Kodi mukufuna kuphunzira zambiri zokhudza lemba linalake, munthu, malo kapena china chilichonse chotchulidwa m’Baibulo? Kapena kodi mumadzifunsa ngati Mawu a Mulungu angakuthandizeni pa vuto linalake limene likukudetsani nkhawa? Ngati ndi choncho, kafufuzeni zimenezi mulaibulale ya pa Nyumba ya Ufumu.

Imakhala ndi mabuku okuthandizani kufufuza zinthu. N’kutheka kuti mulibe mabuku onse a Mboni za Yehova ofotokoza nkhani za m’Baibulo amene alipo m’chinenero chanu. Koma mulaibulale ya pa Nyumba ya Ufumu muli mabuku ambiri atsopano. Mwina mulinso Mabaibulo osiyanasiyana, buku labwino lotanthauzira mawu ndi mabuku ena othandiza. Muli ndi ufulu wowerenga mabuku a mulaibulale, misonkhano isanayambe kapena itatha. Ngati mulaibulalemo muli kompyuta, n’kutheka kuti pakompyutapo pali Watchtower Library. Imeneyi ndi laibulale ya pakompyuta ya mabuku athu ambirimbiri ndipo ndi yosavuta kugwiritsa ntchito, moti mungathe kufufuza nkhani, mawu kapena lemba.

Imathandiza pokonzekera nkhani za m’msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Mungagwiritse ntchito laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu pokonzekera nkhani zanu. Woyang’anira msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndi amene ali ndi udindo woyang’anira laibulale. Iye amaonetsetsa kuti mabuku ndi magazini atsopano aikidwa mulaibulale ndiponso kuti aikidwa madongosolo. M’baleyu kapena munthu amene amakuphunzitsani Baibulo angakusonyezeni mmene mungafufuzire nkhani iliyonse imene mukufuna. Komabe, mabuku a mulaibulale sakuyenera kutulutsidwa mu Nyumba ya Ufumu. Komanso tikuyenera kusamalira mabukuwa ndi kupewa kuwalembalemba.

Baibulo limanena kuti ngati tikufuna ‘kumudziwadi Mulungu,’ tiyenera kukhala akhama pofufuza mawu ake ngati mmene tingafufuzire “chuma chobisika.” (Miyambo 2:1-5) Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu ndi malo abwino amene mungayambire kufufuza nkhani zosiyanasiyana.

  • Kodi mulaibulale ya pa Nyumba ya Ufumu mumapezeka zinthu ziti zokuthandizani kufufuza nkhani?

  • Kodi ndani amene angakuphunzitseni mmene mungagwiritsire ntchito laibulale?